LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • hf section 2 gao 1-2
  • Khalani Okhulupilika kwa Wina ndi Mnzake

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Khalani Okhulupilika kwa Wina ndi Mnzake
  • N’zotheka Banja Lanu Kukhala Lacimwemwe
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • 1 MUZIONA BANJA LANU KUKHALA CINTHU COFUNIKA KWAMBILI
  • 2 TETEZANI MTIMA WANU
  • Dalilani Mulungu Kuti Banja Lanu Likhale Lacimwemwe
    N’zotheka Banja Lanu Kukhala Lacimwemwe
  • Pambuyo Pa Tsiku La Cikwati
    Mmene Tingakhalilebe mu Cikondi ca Mulungu
  • Mmene Mungakhalile Mwamtendele ndi Acibale Anu
    N’zotheka Banja Lanu Kukhala Lacimwemwe
  • Mmene Mungathetsele Mavuto
    N’zotheka Banja Lanu Kukhala Lacimwemwe
Onaninso Zina
N’zotheka Banja Lanu Kukhala Lacimwemwe
hf section 2 gao 1-2
Mwamuna agwilila mkazi wake ambulela pamene akumuthandiza kuloŵa m’galimoto

GAWO 2

Khalani Okhulupilika kwa Wina ndi Mnzake

“Cimene Mulungu wacimanga pamodzi, munthu asacilekanitse.” —Maliko 10:9

Yehova amafuna kuti tizikhala okhulupilika. (Mika 6:8) Zimenezi n’zofunika makamaka m’cikwati canu, cifukwa ngati simukhulupililana ndiye kuti simungadalilane. Ndipo kudalilana n’kofunika kuti cikondi cikule.

Masiku ano, kukhulupilika kukusoŵa m’zikwati. Kuti muteteze cikwati canu, muyenela kuyesetsa kucita zinthu ziŵili.

1 MUZIONA BANJA LANU KUKHALA CINTHU COFUNIKA KWAMBILI

ZIMENE BAIBULO LIMAKAMBA: “Muzitsimikizila kuti zinthu zofunika kwambili ndi ziti.” (Afilipi 1:10) Cikwati canu n’cimodzi mwa zinthu zofunika kwambili paumoyo wanu. Mufunikadi kuciona conco.

Yehova amafuna kuti muzisamalila kwambili mwamuna kapena mkazi wanu ndi kuti ‘musangalale ndi moyo’ pamodzi. (Mlaliki 9:9) Iye amafotokoza bwino kuti simufunika kunyalanyaza mnzanu wa m’cikwati, koma muyenela kupeza njila zosangalatsilana. (1 Akorinto 10:24) Mnzanu wa m’cikwati aziona kuti ndi wofunika ndipo mumamukonda.

Mwamuna abweletsela mkazi wake zakumwa zotentha; mwamuna wafika panyumba ndipo wapeza mkazi wake akuphika

ZIMENE MUNGACITE:

  • Tsimikizilani kuti nthawi zambili mukuceza pamodzi, ndi kumvetsela mosamalitsa zimene mnzanu akamba

  • Muziganizilana

Mwamuna ndi mkazi akucezela pamodzi ku pikiniki

2 TETEZANI MTIMA WANU

ZIMENE BAIBULO LIMAKAMBA: “Aliyense woyang’anitsitsa mkazi mpaka kumulakalaka, wacita naye kale cigololo mumtima mwake.” (Mateyu 5:28) Ngati munthu amangokhalila kuganiza za ciwelewele, m’mau ena tingati ndi wosakhulupilika kwa mnzake wa m’cikwati.

Yehova amanena kuti mufunika ‘kuteteza mtima wanu.’ (Miyambo 4:23; Yeremiya 17:9) Kuti mucite zimenezi muyenela kuteteza maso anu. (Mateyu 5:29, 30) Tsatilani citsanzo ca Yobu, amene anacita pangano ndi maso ake kuti asayang’ane mkazi momulakalaka kapena kuti momukhumbila. (Yobu 31:1) Yesetsani nthawi zonse kupewa kuonelela zamalisece. Pewani kukopana ndi munthu aliyense amene si mkazi kapena mwamuna wanu.

Mwamuna ali ndi cithunzi ca mkazi wake pa desiki ya kunchito

ZIMENE MUNGACITE:

  • Lolani kuti ena adziŵe kuti mumakondana kwambili ndi mkazi kapena mwamuna wanu.

  • Ganizilani mmene mnzanu wa m’cikwati akumvelela, ndipo lekani kuceza ndi anthu alionse amene angacititse mkazi kapena mwamuna wanu kusakondwela

CITANI MBALI YANU

Dzifufuzeni moona mtima, ndipo dziŵani zofooka zanu. (Salimo 15:2) Musacite manyazi kupempha thandizo. (Miyambo 1:5) Mukayamba kuganiza zoipa, yesetsani kuzicotsa m’maganizo anu. Musacite ulesi. (Miyambo 24:16) Yehova adzadalitsa zoyesayesa zanu zofuna kukhala wokhulupilika kwa mnzanu wa m’cikwati.

DZIFUNSENI KUTI . . .

  • Ndingacite ciani kuti ndizipeza nthawi yambili yoceza ndi mnzanga wa m’cikwati?

  • Kodi mnzanga wa m’cikwati ndiye bwenzi langa lapamtima?

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani