LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • hf section 3 gao 1-3
  • Mmene Mungathetsele Mavuto

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Mmene Mungathetsele Mavuto
  • N’zotheka Banja Lanu Kukhala Lacimwemwe
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • 1 KAMBILANANI VUTOLO
  • 2 KHALANI CETE NDI KUMVETSELA KWAMBILI
  • 3 CITAMPONI KANTHU
  • Khalani Okhulupilika kwa Wina ndi Mnzake
    N’zotheka Banja Lanu Kukhala Lacimwemwe
  • Dalilani Mulungu Kuti Banja Lanu Likhale Lacimwemwe
    N’zotheka Banja Lanu Kukhala Lacimwemwe
  • Mmene Mungakhalile Mwamtendele ndi Acibale Anu
    N’zotheka Banja Lanu Kukhala Lacimwemwe
  • Pambuyo Pa Tsiku La Cikwati
    Mmene Tingakhalilebe mu Cikondi ca Mulungu
N’zotheka Banja Lanu Kukhala Lacimwemwe
hf section 3 gao 1-3
Mwamuna akumvetsela pamene mkazi wake afotokoza maganizo ako

GAWO 3

Mmene Mungathetsele Mavuto

“Khalani okondana kwambili, pakuti cikondi cimakwilila macimo oculuka.”—1 Petulo 4:8

Pamene inu ndi mnzanu wa m’cikwati muyamba umoyo watsopano, padzakhala mavuto osiyanasiyana. Cimene cingacititse mavutowo ndi kusiyana maganizo, mmene mumaonela zinthu ndi mmene mumazicitila. Mwina mavuto angacokele kwina kapena cifukwa ca zotigwela zosayembekezeka.

Nthawi zina tingayese kuthaŵa mavuto, koma Baibulo limatilangiza kuti tiyenela kulimbana nao. (Mateyu 5:23, 24) Mwa kugwilitsila nchito mfundo za m’Baibulo mungapeze thandizo labwino kwambili pamavuto anu.

1 KAMBILANANI VUTOLO

ZIMENE BAIBULO LIMAKAMBA: ‘Pali nthawi yolankhula.’ (Mlaliki 3:1, 7) Tsimikizani kuti muli ndi nthawi yokwanila yokambilana vutolo. Musam’bise mnzanu mmene mukumvelela ndi zimene mukuganiza pankhaniyo. Nthawi zonse ‘lankhulani zoona’ kwa mnzanu wa m’cikwati. (Aefeso 4:25) Kaya pakhale kukwiyitsana kwambili muyenela kupewa maganizo ofuna kumenyana. Kuyankha mofatsa kungacititse kuti nkhani isakule ndi kuti pasakhale mkangano waukulu.—Miyambo 15:4; 26:20.

Ngakhale kuti mungasiyane maganizo, cofunika ndi kukhalabe okoma mtima, ndipo osaiŵala kusonyezana cikondi ndi ulemu. (Akolose 4:6) Yesetsani kuthetsa vutolo mwamsanga, ndipo osaleka kukambitsilana.—Aefeso 4:26.

Okwatilana akambitsilana vuto linalake

ZIMENE MUNGACITE:

  • Pezani nthawi yabwino yokambilana vutolo

  • Pamene mnzanu akamba pewani cizoloŵezi com’dula mau. Mudzakamba ikafika nthawi yanu

2 KHALANI CETE NDI KUMVETSELA KWAMBILI

ZIMENE BAIBULO LIMAKAMBA: “Khalani ndi cikondi ceniceni pakati panu. Posonyezana ulemu, khalani patsogolo.” (Aroma 12:10) Kumvetsela kwambili n’kofunika. Yesetsani kumvetsela malingalilo a mnzanu mwa ‘kumvelana cisoni’ ndiponso mwa kukhala ndi “maganizo odzicepetsa.” (1 Petulo 3:8; Yakobo 1:19) Musanamizile kuti mukumvetsela. Ngati n’zotheka lekezani zimene mukucita ndi kumvetsala kwambili zimene mnzanu akukamba, kapena pemphani kuti mukambilane nthawi ina. Ngati muona mnzanu wa m’cikwati monga wocita naye zinthu osati monga mdani, ‘simudzafulumila kukwiya.’—Mlaliki 7:9.

ZIMENE MUNGACITE:

  • Mvetselani zonse zimene mnzanu akukamba, ngakhale kuti zimene akukamba simunazikonde

  • Onani tanthauzo la zimene akukamba. Onetsetsani zimene mnzanu akucita ndipo mvetselani mmene mau akumvekela

3 CITAMPONI KANTHU

ZIMENE BAIBULO LIMAKAMBA: “Kugwila nchito iliyonse kumapindulitsa, koma kungolankhula mau cabe kumasaukitsa.” (Miyambo 14:23) Kungogwilizana mmene mungathetsele vutolo sikokwanila. Muyenela kucita zimene mwagwilizana. Zimenezo zingafune kulimbikila ndipo pamapeto pake mudzapindula. (Miyambo 10:4) Mukamacitila zinthu pamodzi monga banja, mudzakhala ndi “mphoto yabwino.”—Mlaliki 4:9.

ZIMENE MUNGACITE:

  • Kambilanani zimene aliyense payekha adzacita kuti muthetse vutolo

  • Nthawi ndi nthawi muziona ngati mukusintha

THETSANI MAVUTO PAMODZI

Mukamacitila zinthu pamodzi, mungacititse kuti banja lanu likhale lolimba komanso lacimwemwe m’malo mokhala losalimba ndi lamavuto. (Miyambo 24:3) Muziyang’ana kutsogolo, ndipo musafukule mavuto akalekale. (Miyambo 17:9) Ngati mugwilizana ndi kugwilitsila nchito mfundo za m’Baibulo, mungathetse bwinobwino mavuto alionse.

DZIFUNSENI KUTI . . .

  • Kodi vuto limene ine ndi mnzanga wa m’cikwati tifunika kukambilana mwamsanga ndi liti?

  • Ndingacite ciani kuti ndimvetsetse mmene mnzanga akuonela vutolo?

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani