LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • hf section 4 gao 1-2
  • Mmene Mungagwilitsile Nchito Ndalama

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Mmene Mungagwilitsile Nchito Ndalama
  • N’zotheka Banja Lanu Kukhala Lacimwemwe
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • 1 KONZANI ZINTHU MOSAMALA
  • 2 KHALANI OONA MTIMA NDI KUONA NDALAMA MOYENELA
  • Kodi Ndalama N’zimene Zimabweletsa Mavuto Onse?
    Kuyankha Mafunso Okhudza Baibo
N’zotheka Banja Lanu Kukhala Lacimwemwe
hf section 4 gao 1-2
Mwamuna ndi mkazi wake akambitsilana mmene angagwilitsile nchito ndalama mosamala

GAWO 4

Mmene Mungagwilitsile Nchito Ndalama

“Zolinga zimakhazikika anthu akakambilana.”—Miyambo 20:18

Tonse timafunika ndalama kuti tisamalile zofunika za mabanja athu. (Miyambo 30:8) Ndipo, “ndalama zimatetezela.” (Mlaliki 7:12) Monga banja, zingakhale zovuta kukambilana za ndalama. Koma musalole kuti ndalama ziyambitse mavuto m’cikwati canu. (Aefeso 4:32) Pokambilana mmene angagwilitsile nchito ndalama, anthu okwatilana ayenela kukhulupililana ndi kucitila zinthu pamodzi.

1 KONZANI ZINTHU MOSAMALA

ZIMENE BAIBULO LIMAKAMBA: “Ndani wa inu akafuna kumanga nsanja sayamba wakhala pansi kuŵelengela ndalama zimene adzaononge, kuti aone ngati ali ndi ndalama zokwanila kumalizila nsanjayo?” (Luka 14:28) Ndi bwino kukonzela pamodzi mmene mudzagwilitsila nchito ndalama. (Amosi 3:3) Sankhani zimene mufuna kugula ndipo muone ndalama zimene mungagwilitsile nchito. (Miyambo 31:16) Kukhala ndi ndalama zogulila cinacake sikutanthauza kuti mungangogula cinthu ciliconse. Yesetsani kupewa nkhongole. Gwilitsilani nchito ndalama zimene muli nazo.—Miyambo 21:5; 22:7.

ZIMENE MUNGACITE:

  • Ngati pakutha kwa mwezi mwatsalako ndi ndalama zina, muzikambilana mmene mudzazigwilitsila nchito

  • Ngati ndalama n’zocepa, kambilanani mmene mungacepetsele zogula. Mwacitsanzo, m’malo mogula cakudya cophikidwa kale, ndi bwino kuphika nokha

2 KHALANI OONA MTIMA NDI KUONA NDALAMA MOYENELA

ZIMENE BAIBULO LIMAKAMBA: ‘Samalilani zinthu zonse moona mtima, osati pamaso pa Yehova yekha ayi, komanso pamaso pa anthu.’ (2 Akorinto 8:21) Khalani woona mtima kwa mnzanu wa m’cikwati pa ndalama zimene mumapeza ndi kugwilitsila nchito.

Nthawi zonse muzifunsa mnzanu wa m’cikwati pamene mupanga zosankha zikuluzikulu zokhudza ndalama zanu. (Miyambo 13:10) Kukambilana za ndalama kudzathandiza kusunga mtendele m’cikwati canu. Muziona ndalama zimene mumapeza monga za banja osati zanu.—1 Timoteyo 5:8.

Mwamuna ndi mkazi wake akuona pamndandanda wa zinthu zofunika kugula

ZIMENE MUNGACITE:

  • Gwilizanani kuti ndi ndalama zingati zimene aliyense wa inu azigwilitsila nchito popanda kufunsa mnzake

  • Musamangokambilana za ndalama pakakhala vuto

MMENE MUMAONELA NDALAMA

Ngakhale kuti ndalama n’zofunika, musalole kuti zisokoneze cikwati canu kapena kucititsa nkhawa. (Mateyu 6:25-34) Simufunika kucita kukhala ndi ndalama zambili kuti mukondwele ndi umoyo. Baibulo limati: “Cenjelani ndi kusilila kwa nsanje kwamtundu uliwonse.” (Luka 12:15) Zimene mungagule ndi ndalama sizingakhale zofunika kwambili kuposa cikwati canu. Conco khalani wokhutila ndi zimene muli nazo ndipo musanyalanyaze ubwenzi wanu ndi Mulungu. Ngati mucita zimenezi, mudzakhala ndi banja lacimwemwe ndipo Yehova adzakondwela ndi banja lanu.—Aheberi 13:5.

DZIFUNSENI KUTI . . .

  • Monga banja, tingacite ciani kuti tisamakhale ndi nkhongole?

  • Ndi liti pamene ine ndi mnzanga wa m’cikwati tinakambitsilanapo momasuka za ndalama zathu?

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani