LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • ijwbq nkhani 166
  • Kodi Ndalama N’zimene Zimabweletsa Mavuto Onse?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Ndalama N’zimene Zimabweletsa Mavuto Onse?
  • Kuyankha Mafunso Okhudza Baibo
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • Yankho la m’Baibo
  • Kodi Baibo imati ciyani pa nkhani ya ndalama?
  • N’cifukwa ciyani Baibo imati kukonda ndalama n’koipa?
  • Kodi timapindula bwanji na malangizo a m’Baibo pa nkhani ya ndalama?
  • Mmene Mungagwilitsile Nchito Ndalama
    N’zotheka Banja Lanu Kukhala Lacimwemwe
  • Zinsinsi Zotithandiza Kukhala Okhutila
    Galamuka!—2021
  • Kodi Baibo Imakamba Ciyani pa Zanchito Komanso Ndalama?
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
Kuyankha Mafunso Okhudza Baibo
ijwbq nkhani 166
Munthu ali na ndalama zankhani-nkhani.

Kodi Ndalama N’zimene Zimabweletsa Mavuto Onse?

Yankho la m’Baibo

Iyai. Baibo sikamba kuti ndalama n’zoipa, kapenanso kuti n’zimene zimabweletsa mavuto. Zimene anthu ambili amakonda kukamba zakuti “ndalama ndiye muzu wa zoipa zonse” si zoona, ndipo zimangoonetsa kuti samvetsa zimene Baibo imakamba. Baibo imati “kukonda ndalama ndi muzu wa zoipa zonse.”—1 Timoteyo 6:10.

  • Kodi Baibo imati ciyani pa nkhani ya ndalama?

  • N’cifukwa ciyani Baibo imati kukonda ndalama n’koipa?

  • Kodi timapindula bwanji na malangizo a m’Baibo pa nkhani ya ndalama?

  • Malemba a m’Baibo okamba za ndalama

Kodi Baibo imati ciyani pa nkhani ya ndalama?

Baibo imakamba kuti ndalama tikamazigwilitsa nchito mwanzelu, zikhoza kutithandiza komanso ‘kutiteteza.’ (Mlaliki 7:12) Kuwonjezela apo, Baibo imayamikila anthu amene amathandiza anzawo, zimene zingaphatikizepo kuwapatsa ndalama.—Miyambo 11:25.

Komabe, imaticenjezanso kuti tisamakonde kwambili ndalama. Imati: “Moyo wanu ukhale wosakonda ndalama, koma mukhale okhutila ndi zimene muli nazo pa nthawiyo.” (Aheberi 13:5) Apa mfundo ni yakuti tiziona ndalama moyenela, ndipo tipewe kumangofuna-funa cuma. Tizikhala okhutila na zinthu zimene timafunikila, monga cakudya, zovala, komanso pogona.—1 Timoteyo 6:8.

N’cifukwa ciyani Baibo imati kukonda ndalama n’koipa?

Anthu a umbombo sadzapeza moyo wosatha. (Aefeso 5:5) Cifukwa cake n’cakuti umbombo ni mbali ya kulambila mafano kapena kulambila konyenga. (Akolose 3:5) Cina, anthu a umbombo kambili amaphwanya mfundo za m’Baibo kuti apeze zimene akufuna. Miyambo 28:20 imakamba kuti munthu “woyesetsa kuti apeze cuma mofulumila, sadzapitiliza kukhala wosalakwa.” Iye angafike ngakhale pocita zinthu zoipa, monga ciphuphu, kulanda zinthu za ena mokakamiza, cinyengo, kuba anthu n’kukawasunga, kapena kupha anthu.

Olo kuti kukonda ndalama sikungacititse anthu kukhala na makhalidwe oipa, kumakhala na zotulukapo zina zoipa. Baibo imati: “Anthu ofunitsitsa kulemela, amagwela m’mayeselo ndi mumsampha. Iwo amakodwa ndi zilakolako zambili zowapweteketsa.”—1 Timoteyo 6:9.

Kodi timapindula bwanji na malangizo a m’Baibo pa nkhani ya ndalama?

Tikamapewa kuphwanya mfundo za m’Baibo za makhalidwe abwino pa nkhani ya ndalama, tidzadzisungila ulemu ndipo Mulungu adzakondwela nafe komanso adzaticilikiza. Mulungu analonjeza anthu amene amayesetsa kumukondweletsa kuti: “Sindidzakusiyani kapena kukutayani ngakhale pang’ono.” (Aheberi 13:5, 6) Iye amatitsimikizilanso kuti “munthu wocita zinthu mokhulupilika adzapeza madalitso ambili.”—Miyambo 28:20.

Malemba a m’Baibo Okamba za Ndalama

Mlaliki 7:12: “Ndalama zimatetezela.”

Mfundo yake: Ndalama zikhoza kuteteza munthu ngati azigwilitsa nchito mwanzelu.

Luka 12:15: “Ngakhale munthu atakhala ndi zoculuka cotani, moyo wake sucokela m’zinthu zimene ali nazo.”

Mfundo yake: Ndalama si ndiye zofunika kwambili pa umoyo wathu, ndipo sizingatithandize kuti tikapulumuke.

1 Timoteyo 6:10: “Kukonda ndalama ndi muzu wa zopweteka za mtundu uliwonse, ndipo pokulitsa cikondi cimeneci, ena asoceletsedwa n’kusiya cikhulupililo ndipo adzibweletsela zopweteka zambili pathupi lawo.”

Mfundo yake: Ndalama pazokha si zoipa. Koma anthu amene amazikonda kwambili, kutanthauza kungokhalila kuganizila ndalama basi, amazibweletsela mavuto ambili, monga kutha kwa maukwati, komanso kusakhala na thanzi labwino cifukwa congokhalila kugwila nchito.

Aheberi 13:5: “Moyo wanu ukhale wosakonda ndalama, koma mukhale okhutila ndi zimene muli nazo pa nthawiyo.”

Mfundo yake: M’malo momangokhalira kusakila cuma, tizikhutila na zimene tili nazo.

Mateyu 19:24: “N’capafupi kuti ngamila iloŵe padiso la singano kusiyana n’kuti munthu wolemela aloŵe mu Ufumu wa Mulungu.”

Mfundo yake: Pa nthawiyi, Yesu anauza mnyamata wina wacuma kuti akhale wotsatila wake. Mnyamatayo anakana cifukwa cokonda kwambili cuma cakeco. Conco, Yesu anapeleka cenjezo lakuti munthu amene amakonda kwambili cuma kuposa Mulungu, sadzapeza moyo wosatha.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani