LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • hf section 9 gao 1-2
  • Lambilani Yehova Monga Banja

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Lambilani Yehova Monga Banja
  • N’zotheka Banja Lanu Kukhala Lacimwemwe
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • 1 LIMBITSANI UBWENZI WANU NDI YEHOVA
  • 2 SANGALALANI NDI KULAMBILA KWANU KWA PABANJA
  • Kodi Kulambila kwa Pabanja n’Ciani?
    Ndani Amene Akucita Cifunilo Ca Yehova Masiku Ano?
  • Kulambila kwa Pabanja—Zimene Mungacite Kuti Kukhale Kosangalatsa Kwambili
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
  • Kulambila Koona Kudzawonjezela Cimwemwe Canu
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2022
  • Thandizani a m’Banja Lanu Kukumbukila Yehova
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano —2017
Onaninso Zina
N’zotheka Banja Lanu Kukhala Lacimwemwe
hf section 9 gao 1-2
Mwamuna ndi mkazi wake aphunzilila pamodzi Baibulo

GAWO 9

Lambilani Yehova Monga Banja

“Lambilani iye amene anapanga kumwamba, dziko lapansi.”—Chivumbulutso 14:7

Monga mmene taphunzilila m’kabuku kano, m’Baibulo muli mfundo zambili zimene zingakuthandizeni pamodzi ndi banja lanu. Yehova afuna kuti mukhale acimwemwe. Iye walonjeza kuti ngati muika kulambila koona patsogolo, zinthu “zina zonsezi zidzaonjezedwa kwa inu.” (Mateyu 6:33) Iye afunitsitsa kuti mukhale bwenzi lake. Gwilitsilani nchito mpata uliwonse kuti mukulitse ubwenzi wanu ndi Mulungu. Uwu ndi mwai waukulu kwambili umene munthu angakhale nao.—Mateyu 22:37, 38.

1 LIMBITSANI UBWENZI WANU NDI YEHOVA

Mwamuna ndi mkazi ali pamodzi mu utumiki wakumunda

ZIMENE BAIBULO LIMAKAMBA: “‘Ndidzakhala atate wanu, ndipo inu mudzakhala ana anga aamuna ndi aakazi,’ watelo Yehova.” (2 Akorinto 6:18) Mulungu afuna kuti mukhale bwenzi lake la pamtima. Pemphelo ndi njila imodzi imene ingakuthandizeni kucita zimenezo. Yehova akupemphani kuti “muzipemphela mosalekeza.” (1 Atesalonika. 5:17) Iye ndi wofunitsitsa kumva zakukhosi kwanu ndi nkhawa zanu. (Afilipi 4:6) Mukamapemphela ndi banja lanu io adzaona kuti Mulungu ndi weniweni kwa inu.

Kuonjezela pa kukamba ndi Mulungu, muyenelanso kumumvela. Mungacite zimenezo mwa kuphunzila Mau ake ndi mabuku ofotokoza Baibulo. (Salimo 1:1, 2) Muzisinkhasinkha zimene mwaphunzila. (Salimo 77:11, 12) Kumvetsela kwa Mulungu kumafunanso kuti tizipezeka pa misonkhano yacikristu nthawi zonse.—Salimo 122:1-4.

Kulalikila kwa ena za Yehova ndi njila inanso yofunika yolimbitsila ubwenzi wanu ndi iye. Kulalikila kaŵilikaŵili kudzakuthandizani kumuyandikila kwambili.—Mateyu 28:19, 20.

ZIMENE MUNGACITE:

  • Tsiku lililonse muzipatula nthawi yoŵelenga Baibulo ndi kupemphela

  • Monga banja, ikani zinthu za kuuzimu pamalo oyamba, m’malo mwa zosangulutsa ndi kupumula

2 SANGALALANI NDI KULAMBILA KWANU KWA PABANJA

Tate akonzekela kuphunzila ndi banja lake ndipo kenako akucita kulambila kwa pa banja

ZIMENE BAIBULO LIMAKAMBA: “Yandikilani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikilani.” (Yakobo 4:8) Muyenela kukhala ndi ndandanda yokhazikika yocita kulambila kwa pabanja, ndipo muyenela kuitsatila. (Genesis 18:19) Koma muyenela kucita zambili kuposa pamenepa. Mulungu ayenela kukhala mbali ya moyo wanu watsiku ndi tsiku. Muyenela kulimbitsa ubwenzi wa banja lanu ndi Mulungu mwa kulankhula za iye ‘mukakhala pansi m’nyumba mwanu, poyenda pamseu, pogona ndi podzuka.’ (Deuteronomo 6:6, 7) Yesetsani kukhala ngati Yoswa, amene anati: “Koma ine ndi a m’nyumba yanga, tizitumikila Yehova.”—Yoswa 24:15.

ZIMENE MUNGACITE:

  • Khalani ndi pulogalamu yophunzitsa yodalilika imene idzakuthandizani kudziŵa zosoŵa za aliyense m’banja lanu

Mai aŵelengela mwana wake wamwamuna; banja licita seŵelo la m’Baibulo; tate aphunzila ndi mwana wake wamkazi

ATUMIKI A YEHOVA ACIMWEMWE

Palibe cinthu cabwino kuposa kulambila Yehova Mulungu. Iye akaona inu ndi banja lanu mukum’tumikila mokhulupilika amasangalala. Mukamacita zimenezi, mudzayamba kukonda ndi kutsanzila kwambili Yehova. (Maliko 12:30; Aefeso 5:1) Mulungu akakhala m’banja lanu, zimenezo zimacititsa kuti muzikondana kwambili ndi mnzanu wa m’cikwati. (Mlaliki 4:12; Yesaya 48:17) Inu ndi banja lanu mungakhale acimwemwe kosatha, podziŵa kuti “Yehova Mulungu wanu wakudalitsani.”—Deuteronomo 12:7.

DZIFUNSENI KUTI . . .

  • Ndi liti pamene ine ndi mkazi wanga tinapemphela pamodzi?

  • Ndingaphunzile ciani ndi banja langa cimene cingalimbitse cikhulupililo cathu mwa Yehova?

CIDZIŴITSO KU MITU YA BANJA

  • Musalole ciliconse kusokoneza kulambila kwanu kwa pabanja

  • Banja lanu liyenela kudziŵilatu pasadakhale zimene mudzakambilana kotelo kuti akonzekele

  • Tsimikizilani kuti onse m’banja apezekapo

  • Cititsani kuti pazikhala mtendele kuti onse azipindula

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani