Kulambila kwa Pabanja Zimene Mungacite Kuti Kukhale Kosangalatsa Kwambili
Tate wina ku Brazil anati: “Timatengeka ndi Kulambila kwa Pabanja cakuti ngati sindinakumbutse banja kuti nthawi yatha timafika mpaka pakati pausiku.” Mutu wina wabanja ku Japan unanena kuti mwana wao wa zaka khumi samazindikila kuti nthawi yatha, iye amafuna kuti apitilizebe. N’cifukwa ciani amatelo? Atate ake anati, “iye amalimbikitsidwa ndi Kulambila kwa Pabanja, ndipo zimenezo zimam’cititsa kuti azisangalala.”
Komabe, si ana onse amene amafunitsitsa kucita Kulambila kwa Pabanja, ndipo kunena zoona ena samasangalala. N’cifukwa ciani? Tate wina ku Togo anasimba kuti, “Kulambila Yehova sikuyenela kukhala kocititsa ulesi.” Ngati kulambila kwa Pabanja kumacititsa ulesi, mwina n’cifukwa ca mmene mumatsogozela. Mabanja ena ‘amasangalala kwambili’ ndi kulambila kwa pabanja monga mmene Yesaya anafotokozela ponena za Sabata.—Yes. 58:13, 14.
Kuti banja lizisangalala ndi kulambila kwa pabanja, makolo acikristu aona kuti ndi bwino kucititsa aliyense kukhala womasuka. Ralf amene ali ndi ana anai anati, kulambila kwao kwa pabanja kumakhala ngati kuceza cabe, ndipo aliyense amatengamo mbali. N’zoona kuti kucititsa onse kusangalala ndi kutengamo mbali nthawi zina kungakhale kovuta. Mai wina anavomeleza kuti: “Nthawi zina zimandivuta kuti ndicititse kulambila kwa pabanja kukhala kosangalatsa, monga mmene ndimafunila.” Kodi mungacite ciani kuti muthetse vuto limenelo?
MUZISINTHA-SINTHA NKHANI ZOKAMBILANA
Tate wina wa ana aŵili ku Germany anati: “Tizikhala okonzeka kusintha.” Natalia, mai wa ana aŵili anati: “Taona kuti cofunika kwambili ku banja lathu ndi kusintha-sintha nkhani zokambilana.” Mabanja ambili amagaŵa nthawi ya kulambila kwa pabanja m’zigawo zingapo. Cleiton, kholo la ana acinyamata aŵili ku Brazil anafotokoza kuti, “Zimenezo zimacititsa kuti phunzilo likhale laumoyo ndi kuti onse atengemo mbali.” Pogaŵa nthawi yolambila, makolo ayenela kuganizila zosoŵa za mwana aliyense, maka-maka ngati ali ndi zaka zosiyana. Zimenezo zingathandize makolo kusamalila zosoŵa za aliyense m’banja, ndipo zingawapatse mpata wosintha nkhani ndi kacitidwe kake.
Kodi mabanja ena amacita ciani kuti acititse kulambila kwa Pabanja kukhala kosangalatsa? Ena amayamba kulambila kwa pabanja mwa kuimba nyimbo zotamanda Yehova. Juan wa ku Mexico anati: “Zimenezo zimacititsa onse kukhala omasuka kwambili ndipo amakonzekela nkhani imene tidzakambilana.” Ndipo banjalo limasankha nyimbo zogwilizana ndi nkhani zophunzila tsikulo.
Mabanja ambili amaŵelengela pamodzi cigawo ca m’Baibulo. Pofuna kusintha-sintha nkhani zophunzila, io amagaŵana zigawo za anthu osiyana-siyana a m’Baibulo ndi kuziŵelenga monga banja. Tate wina ku Japan anavomeleza kuti, “poyamba zinali zacilendo kuŵelenga mwa njila imeneyo.” Koma ana ao aŵili anasangalala kucita zimenezo ndi makolo. Mabanja ena amacita maseŵelo a nkhani za m’Baibulo. Roger, tate wa ana aŵili ku South Africa anafotokoza kuti, “ana athu amapeza zinthu zimene sitinazione m’Baibulo.”
Njila ina imene imathandiza kusintha-sintha nkhani ndi kukhala ndi pulogalamu yocita zinazake, monga kupanga Combo ca Nowa coyelekezela kapena kacisi wa Solomo. Zocitika zimenezi zimafuna kufufuza, ndipo kufufuzako kungakhale kosangalatsa. Mwacitsanzo, ku Asia, kamtsikana ka zaka zisanu, makolo, ndi agogo ake anali kukonza seŵelo lonena za ulendo waumishonale wa mtumwi Paulo m’cipinda cocezela. Mabanja ena amacita maseŵela ozikidwa pa zocitika za m’buku la Ekisodo. Donald wa zaka 19 ku Togo anati, kusintha-sintha “kwacititsa kuti nkhani zizimveka zatsopano ndiponso kwasintha umoyo wathu wabanja.” Kodi pali zinthu zina zimene mungacite kuti kulambila kwanu kwa pabanja kukhala kosangalatsa?
KUKONZEKELA N’KOFUNIKA
Ngakhale kuti kusintha-sintha nkhani zokambitsilana kumacititsa kulambila kwa pabanja kukhala kosangalatsa, onse ayenela kukonzekela kuti kulambilako kukhaledi kogwila mtima. Popeza nthawi zina ana amatopa, zingakhale bwino kuti tate aone kuti ndi nkhani ziti zimene angasankhe ndipo ayenela kupeza nthawi yokonzekela. Tate wina ananena kuti, “Ndikakonzekela, onse amakhala ndi phunzilo lopindulitsa.” Tate wina ku Germany amauzilatu banja lake zimene adzaphunzila milungu ingapo pasadakhale. Tate wina wa ana 6 ku Benin ananena kuti, ngati wasankha kuti adzapenyelela DVD yophunzitsa Baibulo pa kulambila kwao kwa pabanja, iye amapelekelatu mafunso ku banja lake kukali nthawi. Ndithudi, kukonzekela kumacititsa kuti kulambila kwathu kwa pabanja kukhale kopindulitsa.
Ngati a m’banja adziŵilatu nkhani zimene adzakambilana, io akhoza kumasimbilana nkhaniyo mkati mwa mlunguwo, ndipo zimenezo zimawacititsa kukhala okonzeka. Aliyense akapatsidwa mbali, angapange kulambila kwa pabanja kukhala kwake-kwake.
YESETSANI KUKHALA NDI NDANDANDA YOKHAZIKIKA
Mabanja ambili zimawavuta kucita kulambila kwa pabanja mokhazikika.
Mitu ina ya banja imagwila nchito maola ambili kuti asamalile banja lao. Mwacitsanzo, tate wina ku Mexico amacoka panyumba 6 koloko mmaŵa, ndipo amabwelela kunyumba 8 koloko usiku. Nthawi zina pangafunike kusintha nthawi yocita Kulambila kwa Pabanja cifukwa ca mapulogalamu ena a kuuzimu.
Ngakhale n’conco, tiyenela kuonetsetsa kuti kulambila kwathu kwa pabanja kumacitika mokhazikika. Loïs wa zaka 11 ku Togo ananena za mzimu umene banja lao lili nao kuti: “Ngakhale kuti nthawi zina tingayambe kulambila kwathu mocedwa cifukwa ca zinthu zina zimene zacitika pa tsikulo, timaonetsetsa kuti sitinaphonye.” Ndiye cifukwa cake mabanja ena amacita kulambila kwa pabanja kuciyambi kwa mlungu. Pakagwa za mwadzidzidzi, io amasinthila patsiku lina mlungu umodzi-modziwo.
Monga mmene mutu wankhani ukuonetsela, “kulambila kwa pabanja” ndi mbali imodzi ya kulambila kwathu Yehova. Conco, lolani kuti onse a m’banja lanu azibweletsa kwa Yehova nsembe ya “ana amphongo a ng’ombe” mlungu uliwonse. (Hos. 14:2) Inde, nthawi ya kulambila kwa pabanja iyenela kukhala yosangalatsa kwa onse m’banja, “pakuti cimwemwe cimene Yehova amapeleka ndico malo anu acitetezo.”—Neh. 8:9, 10.