Muzisamalila Okalamba
“Ana anga okondedwa, tisamakondane ndi mau okha kapena ndi pakamwa pokha, koma tizisonyezana cikondi ceni-ceni m’zocita zathu.”—1 YOH. 3:18.
1, 2. (a) Kodi mabanja ambili amakumana ndi mavuto otani? Ndipo pangabuke funso liti? (b) Kodi makolo ndi ana angakonzekele bwanji mavuto amene angabwele?
ZINGAKHALE zopweteka mtima kuona kuti makolo anu amene kale anali olimba ndipo anali kudzicitila okha zinthu sangathenso kudzisamalila. Mungalandile uthenga wakuti amai kapena atate anu agwa ndi kudzipweteka, adwala matenda a maganizo ndipo acoka panyumba, kapena kuti awapeza ndi matenda aakulu. Komanso zingakhale zopweteka kwa okalamba kuona kuti umoyo wao wasintha ndi kuti sangathenso kucita zinthu paokha. (Yobu 14:1) Kodi tingawasamalile bwanji?
2 Nkhani ina yofotokoza za kusamalila okalamba inati: “Ngakhale kuti kukambitsilana nkhani yosamalila okalamba kungakhale kovuta, banja likakambilana pasadakhale njila zocitila zimenezi lingasamalile bwino mavuto amene angabwele.” Tifunika kuzindikila kuti sitingapewe mavuto obwela ndi ukalamba. Ndiye cifukwa cake banja liyenela kukonzekela pasadakhale. Tiyeni tione zimene mabanja angacite kuti apange zosankha zovuta zimenezi mogwilizana.
KONZEKELANI “MASIKU OIPA”
3. Kodi mabanja angacite ciani pamene makolo okalamba afunikila thandizo? (Onani cithunzi-thunzi kuciyambi kwa nkhani ino.)
3 Nthawi imafika pamene okalamba sangathenso kudzisamalila, ndipo amafuna thandizo. (Ŵelengani Mlaliki 12:1-7.) Zimenezi zikacitika, makolo okalamba ndi ana ao ayenela kukambilana za thandizo limene lingakhale bwino ndiponso limene angakwanitse. N’kofunika kuti banja likambilane za thandizo lofunikila, mmene lingapelekedwele, ndi zimene aliyense angacite. Onse m’banja maka-maka makolo ayenela kuyesetsa kuona zinthu moyenela ndi kukambilana momasuka. Banja lingakambitsilane kaya makolo angapitilize kukhala okha malinga ngati pali thandizo lina.a Mwina angakambitsilane zimene aliyense m’banja angacite kuti athandize makolo. (Miy. 24:6) Mwacitsanzo, ena angazisamalila zosoŵa zao za tsiku ndi tsiku ndipo ena angazipeleka thandizo la ndalama. Aliyense ayenela kuzindikila kuti ali ndi udindo, koma m’kupita kwa nthawi maudindo angasinthe, ndipo pangafunike kumasinthana zocita.
4. Kodi ndi kuti kumene banja lingapeze thandizo?
4 Pamene muyamba kupeleka thandizo muyenela kudziŵa bwino matenda a makolo anu. Ngati atate kapena amai anu akudwala matenda osacilitsika, ndi bwino kudziŵa zoloŵetsedwamo. (Miy 1:5) Funsilani ku maofesi a boma amene amapeleka thandizo kwa okalamba kuti mudziŵe thandizo limene makolo anu angalandile. Kusintha kwa zinthu m’banja kungacititse kuti mukhale ndi maganizo osoŵetsa mtendele monga cisoni ndi kukhumudwa. Uzankoni mzanu wodalilika mmene mumvelela. Muyenelanso kupemphela kwa Yehova. Iye adzakupatsani mtendele wamaganizo kuti mulimbane ndi vuto lililonse.—Sal. 55:22; Miy. 24:10; Afil. 4:6, 7.
5. N’cifukwa ciani n’kofunika kufufuza pasadakhale thandizo limene lingapelekedwe kwa okalamba?
5 Okalamba ndi mabanja ao ayenela kufufuza pasadakhale za thandizo limene lingapelekedwe. Mwacitsanzo, banja lingafune kudziŵilatu ngati zidzakhala zoyenela kuti makolo azikhala ndi ana ao, kunyumba yosungila okalamba kapena kuona ngati pali thandizo lina kudela lao. Mwa njila imeneyi banja lingakonzekele ‘mavuto ndi zopweteka’ zimene zimabwela ndi ukalamba. (Sal. 90:10) Mabanja amene samapanga makonzedwe pasadakhale amakakamizika kupanga zosankha mofulumila mavuto akabwela. Katswili wina anati: “Iyi si nthawi yabwino yopanga zosankha.” Ngati banja lipanga zosankha mofulumila lingapanikizike ndipo pangakhale mikangano. Koma kupanga zosankha pasadakhale kungathandize kusapanikizika kwambili umoyo ukasintha.—Miy. 20:18.
6. N’cifukwa ciani makolo ndi ana ayenela kukambitsilana pasadakhale za kumene makolo adzakhala akadzakalamba?
6 Zingakhale zovuta kukambitsilana ndi makolo za kusintha zinthu zina panyumba yao kapena zakuti panthawi ina angafunike kusamuka. Koma ambili aona kuti kukambitsilana kwa conco kwakhala kothandiza. N’cifukwa ciani tikutelo? Cifukwa cakuti kukambitsilana kwa conco kumathandiza banja kugwilizana ndi kulemekezana popanga zosankha zovuta. Anthuwo anaona kuti kukambitsilana pasadakhale mwacikondi ndi mokoma mtima kunaŵathandiza kupanga zosankha popanda mavuto. Ngakhale kuti makolo okalamba angafune kukhala okha ndi kumadzicitila zinthu, n’kofunika kuti io akambitsilane ndi ana za thandizo limene angafune pakabwela vuto.
7, 8. Kodi ndi zinthu ziti zimene mabanja angakambitsilane? Nanga n’cifukwa ciani?
7 Pokambitsilana, makolo muyenela kudziŵitsa banja lanu zimene mufuna, kuculuka kwa ndalama zimene mufunikila ndi zinthu zina. Izi zidzathandiza ana kupanga zosankha zoyenela panthawi imene inuyo simungathe kucita zimenezi. Mwacionekele, ana anu adzalemekeza zofuna zanu ndi kucita zonse zimene angathe kuti muzikhala nokha. (Aef. 6:2-4) Mwacitsanzo, kodi mungafune kukhala ndi mmodzi wa ana anu ndi banja lake? Kapena kodi mungafune zina zake? Khalani ndi maganizo oyenela ndipo kumbukilani kuti ena m’banja angakhale ndi maganizo osiyana ndi anu. Zimathenga nthawi kuti onse asinthe maganizo ao.
8 Onse m’banja ayenela kudziŵa kuti angapewe mavuto mwa kukambitsilana ndi kukonzekela pasadakhale. (Miy. 15:22) Izi ziphatikizapo kukambitsilana za thandizo la mankhwala limene makolo angafune. Pokambitsilana, mungagwilitsile nchito mfundo zili pa khadi la DPA la Mboni za Yehova. Munthu aliyense ali ndi ufulu wodziŵa mtundu wa mankhwala amene alipo, ndipo ali ndi ufulu wolandila mankhwala kapena kukana. Khadi la DPA limafotokoza zofuna za munthu. Kusankha munthu wodalilika kukuimilani pankhani ya thandizo la mankhwala kudzathandiza kuti munthuyo akupangileni zosankha zoyenela ngati n’kofunika. Anthu onse okuimilani ayenela kukhala ndi fotokope ya DPA lanu. Okalamba ena amasunga khadi lao la DPA pamodzi ndi wilo, zipepala zina zofunika za inshuwalansi, za ku banki, ndi manambala a maofesi a boma othandiza okalamba.
ZIMENE MUNGACITE ZINTHU ZIKASINTHA
9, 10. Kodi n’zocitika ziti zimene zingacititse ana kupeleka thandizo lalikulu kwa makolo ao?
9 Nthawi zambili onse m’banja angafune kuti makolo okalamba azikhala okha. Ngati makolo amakwanitsa kuphika, kuyeletsa, kumwa mankhwala, ndi kulankhulana bwino ndi ana ao, ana sangafunikile kulamulila makolo ao pa kalikonse. Koma ngati m’kupita kwa nthawi makolo ayamba kuvutika kuyenda, kugula zinthu zofunikila, kapena kuiŵala-iŵala, ana angafunikile kusintha zinthu zina.
10 Makolo okalamba angadwale cifukwa ca maganizo. Iwo angayambe kusamvetsetsa, kusaona bwino, kuiŵala-iŵala, ndi kuvutika kupita ku cimbudzi. Ngati makolo akhala ndi mavuto monga amenewa, mwamsanga angafunike thandizo la zacipatala. Ana adzafunika kukonza zokaonana ndi adokotala ndi kuthandiza makolo pa mbali zosiyana-siyana. Kuti makolo alandile thandizo lofunika, ana ayenela kuŵaimilako, kuŵathandiza pa mbali zofunikila kulemba ndi kuŵapeleka kulikonse kumene afunika kupita ndi zina zake.—Miy. 3:27.
11. Kodi mungacite ciani kuti makolo azoloŵele mwamsanga ndi kusintha kwa zinthu?
11 Ngati makolo anu ali ndi matenda osacilitsika, mungafunikile kusintha njila zoŵasamalila kapena kusintha zinthu zina m’nyumba yao. Mukapanga masinthidwe aang’ono, makolo angazoloŵele mwamsanga ndi kusinthako. Ngati mumakhala kutali ndi makolo anu, Mboni kapena munthu wina amene akhala pafupi ndi makolo anu angadziŵaonako ndi kukudziŵitsani mmene umoyo wao ulili. Kodi makolo anu amafuna kuŵathandiza kuphika ndi kuyeletsa cabe? Kodi kusintha zinthu zina m’nyumba yao, kudzathandiza kuti makolo aziyenda, azisamba, ndi kucita zinthu zina popanda vuto? Mwina okalamba amangofunikila munthu woŵathandiza nchito zina kuti akhale okha. Koma ngati makolo sangakhale okha pangafunikile kupeza njila ina yoŵasamalila. Mulimonse mmene zingakhalile muyenela kufufuza cithandizo ca okalamba kwanuko.b—Ŵelengani Miyambo 21:5.
ZIMENE ENA AMACITA
12, 13. Kodi ana ena amacita ciani kuti azilemekeza ndi kusamalila makolo ao amene akhala kutali ndi io?
12 Ana amafuna kuti makolo ao azikhala bwino cifukwa amaŵakonda. Timakhala ndi mtendele wamaganizo ngati makolo athu asamalilidwa bwino. Komabe, ana ambili amakhala kutali ndi makolo ao. Ana ena akakhala pachuthi amapita kukaona makolo ao, kuŵasamalila, ndi kuŵathandiza nchito zimene sangathe kugwila. Ana angaonetse kuti amakonda makolo ao mwa kukamba nao pafoni nthawi zonse kapena kuwalembela makalata.—Miy. 23:24, 25.
13 Ngakhale kuti mumakhala kutali ndi makolo anu mudzafunikila kuona zimene amafunikila tsiku ndi tsiku. Ngati makolo anu ndi Mboni ndipo amakhala kutali ndi inu, mungakambe ndi akulu a kumpingo wao kuti mufunsile zimene mungacite. Ndipo muzichula makolo anu m’pemphelo. (Ŵelengani Miyambo 11:14.) Muyenela ‘kulemekeza atate ndi amai anu’ ngakhale kuti io si Mboni. (Eks. 20:12; Miy. 23:22) Mabanja amapanga zosankha zosiyana-siyana. Ena amasankha kukhala ndi makolo ao kapena kukhala kufupi ndi kumene amakhala. Koma nthawi zina zimenezi n’zosatheka. Makolo ena sangafune kukhala ndi ana ao. Iwo angafune kukhala paokha kuti asakhale mtolo kwa ana ao. Makolo ena amakwanitsa kudzipezela zofunika pamene akhala okha.—Mlal. 7:12.
14. Kodi ndi vuto liti limene ana osamalila makolo angakumane nalo?
14 M’mabanja ambili, ana amene akhala pafupi ndi makolo ndiye amapeleka cisamalilo cacikulu. Komabe, ana amene amasamalila makolo ao sayenela kunyalanyaza udindo wosamalila mabanja ao. Munthu aliyense amakhala ndi malile ocita zinthu. Conco, zinthu zikasintha pa umoyo wa mwana wosamalila makolo, banja lingapangenso makonzedwe ena. Kodi mwanayo ali ndi zinthu zambili zofunika kusamalila? Kodi ana ena angathandizileko mbali zina, monga kusinthana-sinthana kupeleka cisamalilo?
15. Kodi n’ciani cingathandize kuti mwana wosamalila makolo asatope?
15 Ngati kholo lokalamba limafunikila thandizo nthawi zonse, mwana wolisamalila angatope. (Mlal. 4:6) Ana amene amakonda makolo ao amayesetsa kucita zimene angathe, koma nthawi zina nchito yowasamalila ingakule kwambili. Ngati n’conco, anawo ayenela kuona zinthu moyenela, mwina angapemphe thandizo. Ngati thandizo limapelekedwa kwa makolo nthawi ndi nthawi, makolo sangafunikile kupita kukakhala kunyumba yosungila okalamba.
16, 17. Kodi ndi mavuto ati amene ana angakumane nao posamalila makolo okalamba? Nanga angapilile bwanji? (Onani bokosi yakuti “Anapeleka Thandizo Loyenela.”)
16 Zimakhudza mtima kuona mmene makolo athu amavutikila ndi ukalamba. Ana ambili osamalila makolo amakhala ndi cisoni, nkhaŵa, ndipo angakwiye ndi kukhumudwa. Nthawi zina kholo lokalamba lingakambe mau opweteka kapena kuonetsa kusayamikila. Zikakhala conco simuyenela kukwiya. Katswili wina wa matenda a maganizo anati: “Njila yabwino yogonjetsela maganizo amenewa ndi kudziŵa kuti n’zacibadwa kumva conco, ndipo musamadziimbe mlandu mukakhala ndi maganizo amenewo.” Mungauzeko mwamuna kapena mkazi wanu, wacibale, kapena mzanu wodalilika mmene mumvelela. Kucita zimenezi kudzathandiza kuti muone zinthu moyenela.
17 Nthawi ingafike pamene simungathenso kusamalila okalamba panyumba. Conco, banja lingagwilizane kuti kholo likakhale kunyumba yosungila okalamba. Mlongo wina anali kupita kunyumba yosungila okalamba kukaona amai ake pafupi-fupi tsiku lililonse. Iye anati: “Tinalephela kupeleka cisamalilo ca nthawi zonse cimene amai anali kufunikila. Zinali zovuta kwambili kuti amai avomele kupita kunyumba yosungila okalamba. Iwo anavutika maganizo kwambili. Komabe, miyezi yocepa io asanamwalile anaona kuti anacita bwino kuvomela kukakhala kunyumbayo.”
18. Kodi anthu osamalila okalamba angatsimikize za ciani?
18 Nchito yosamalila makolo anu okalamba ingakhale yovuta. Njila zosamalila okalamba zimasiyana-siyana. Komabe, ngati mwakonzekela pasadakhale, mumagwilizana m’banja, mumalankhulana bwino, ndipo koposa zonse ngati mumapemphela kwa Yehova, mudzakwanilitsa udindo wanu wolemekeza makolo anu okondedwa. Ngati mukwanilitsa udindo wanu mudzasangala kudziŵa kuti makolo anu akulandila cisamalilo ndi cikondi cimene amafunikila. (Ŵelengani 1 Akorinto 13:4-8.) Koposa zonse, mungakhale otsimikiza kuti mudzakhala ndi mtendele wamaganizo ndi kulandila madalitso a Yehova.—Afil. 4:7.
a M’maiko ena makolo amakhala pamodzi ndi ana ao aakulu ndipo mabanja ena angasankhe kucita zimenezo.
b Ngati makolo anu amakhala okha, tsimikizilani kuti anthu odalilika amene amawasamalila ali ndi makiyi kuti azitsegula nyumbayo ngati pagwa zamwadzidzidzi.