Muzilemekeza Okalamba Ali Pakati Panu
“Munthu wacikulile uzim’patsa ulemu.”—LEV. 19:32.
1. Kodi anthu amakumana ndi mavuto otani?
YEHOVA sanafune kuti anthu azivutika ndi ukalamba. M’malo mwake, cifuno cake cinali cakuti anthu onse asangalale ndi thanzi labwino mu Paladaiso. Koma “cilengedwe conse cikubuula limodzi ndi kumva zoŵaŵa.” (Aroma 8:22) Kodi muganiza kuti Mulungu amamva bwanji akaona anthu akuvutika ndi mavuto obwela ndi ucimo? Ndipo n’zacisoni kuti okalamba ambili amanyalanyazidwa panthawi imene afunikila cisamalilo cacikulu.—Sal. 39:5; 2 Tim. 3:3.
2. N’cifukwa ciani Akristu amayamikila kukhala ndi okalamba mumpingo?
2 Anthu a Yehova amayamikila kukhala ndi okalamba mumpingo. Timapindula ndi nzelu zao ndi kukhulupilika kwao. Mwina okalamba amenewa ndi acibale athu. Conco, kaya okalamba amenewa ndi acibale athu kapena ai, tiyenela kuwasamalila kwambili. (Agal. 6:10; 1 Pet. 1:22) Ife tonse tidzapindula mwa kudziŵa mmene Mulungu amaonela okalamba. Ndipo tidzakambilananso zimene banja ndi mpingo uyenela kucita ponena za okalamba athu okondedwa.
“MUSANDITAYE”
3, 4. (a) Kodi wolemba Salimo 71 anapempha ciani kwa Yehova mocokela pansi pamtima? (b) Nanga okalamba mumpingo angapemphe ciani kwa Mulungu?
3 Wolemba Salimo 71:9 anacondelela Mulungu kuti: “Musanditaye nthawi ya ukalamba wanga. Musandisiye pa nthawi imene mphamvu zanga zikutha.” Cioneka kuti amene analemba mau amenewa ndi Davide. Iye anatumikila Mulungu kuyambila ali mnyamata mpaka atakalamba. Ndipo Yehova anamugwilitsila nchito kucita zinthu zazikulu. (1 Sam. 17:33-37, 50; 1 Maf. 2:1-3, 10) Ngakhale n’conco, Davide anapempha Yehova kuti apitilize kum’thandiza.—Ŵelengani Salimo 71:17, 18.
4 Masiku ano, ambili ali ngati Davide. Mosasamala kanthu za ukalamba ndi “masiku oipa,” io apitilizabe kutamanda Mulungu mmene angathele. (Mlal. 12:1-7) Ndipo ambili amalephela kucita zimene anali kucita kale, kuphatikizapo ulaliki. Koma naonso angacondelele Yehova kuti apitilizebe kuwathandiza ndi kuwasamalila. Okalamba okhulupilika amenewa angakhale ndi cidalilo cakuti Mulungu adzayankha mapemphelo ao. Tidziŵa zimenezi cifukwa mouzilidwa ndi Yehova, Davide anapemphelela zinthu zimenezo.
5. Kodi Yehova amawaona bwanji okalamba okhulupilika?
5 Malemba amakamba mosapita m’mbali kuti Yehova amaona okalamba okhulupilika kukhala amtengo wapatali, ndipo amafuna kuti atumiki ake aziwalemekeza. (Sal. 22:24-26; Miy. 16:31; 20:29) Levitiko 19:32 imati: “Anthu aimvi uziwagwadila, munthu wacikulile uzim’patsa ulemu ndipo uziopa Mulungu wako. Ine ndine Yehova.” Inde, pamene mau awa analembedwa, kulemekeza okalamba mumpingo kunali nkhani yofunika kwambili, ndipo n’cimodzi-modzinso masiku ano. Koma kodi kusamalila okalamba ndi udindo wa ndani?
ZIMENE BANJA LIYENELA KUCITA
6. Kodi Yesu anapeleka citsanzo cotani pankhani yosamalila amai ake?
6 Mau a Mulungu amati: “Uzilemekeza bambo ako ndi mai ako.” (Eks. 20:12; Aef. 6:2) Yesu anagogomezela kufunika kwa lamulo limeneli mwa kudzudzula Afalisi ndi alembi amene sanali kusamalila makolo ao. (Maliko 7:5, 10-13) Yesu anapeleka citsanzo cabwino pankhani imeneyi. Mwacitsanzo, ali pafupi kufa pamtengo wozunzikilapo, iye anapeleka udindo wosamalila amai ake amene mwacionekele anali amasiye kwa Yohane wophunzila wake wokondedwa.—Yoh. 19:26, 27.
7. (a) Kodi mtumwi Paulo analemba mfundo iti yokhudza kusamalila makolo? (b) Ndipo anafotokozanso ciani?
7 M’kalata yake kwa Timoteyo, Mtumwi Paulo analemba kuti Akristu ayenela kusamalila a m’banja lao. (Ŵelengani 1 Timoteyo 5:4, 8, 16.) Paulo anafotokoza amene anali woyenelela kulandila cithandizo mumpingo. Iye analemba mosapita mbali kuti ana acikristu, adzukulu, ndi acibale ena ndi amene anali ndi udindo waukulu wosamalila akazi amasiye okalamba m’banja lao. Conco, zimenezi zinathandiza kuti mpingo usakhale ndi mtolo. Mofananamo, masiku ano njila imodzi imene Akristu amaonetsela kuti ndi “odzipeleka kwa Mulungu” ndi mwa kusamalila acibale ao osoŵa mwakuthupi.
8. N’cifukwa ciani Baibulo silipeleka malangizo acindunji okhudza kusamalila makolo okalamba?
8 Mwacidule tinganene kuti, ana acikulile acikristu ndi amene ali ndi udindo wosamalila zosoŵa za makolo ao. Apa Paulo anali kunena za kuthandiza acibale amene ndi Akristu, koma makolo amene si Akristu naonso sayenela kunyalanyazidwa. Banja lingasankhe mmene lingapelekele cisamalilo, cifukwa banja lililonse lili ndi mavuto ake. Zofuna, mikhalidwe ndi thanzi la opeleka cisamalilo zimasiyana. Okalamba ena ali ndi ana ambili pamene ena ali ndi mmodzi cabe. Ena amalandila cisamalilo ca Boma koma ena samatelo. Ndiponso zofuna za anthu ofunika cisamalilo zimasiyana. Conco, ndi kusoŵa cikondi kusuliza mmene ena amasamalila acibale ao okalamba.
9-11. (a) Kodi ena amakumana ndi mavuto otani? (Onani cithunzi-thunzi kuciyambi kwa nkhani ino.) (b) N’cifukwa ciani ana acikulile sayenela kufulumila kusiya utumiki wanthawi zonse? Pelekani citsanzo.
9 Ngati makolo okalamba ndi ana akhala motalikilana, zingakhale zovuta kwa ana kupeleka cisamalilo coyenelela. Ana angafunike mwamsanga kupita kukacezela makolo ao okalamba amene anadziphweteka cifukwa cakugwa kapena cifukwa ca mavuto ena aakulu. Ndipo mwina makolowo angafunikile cisamalilo kwa kanthawi kapena kwa nthawi yaitali.a
10 Atumiki a nthawi zonse amene akutumikila kutali ndi makolo ao, angavutike kusankha cocita. Atumiki a pa Beteli, amishonale ndi oyang’anila oyendela, onse amaona nchito yao kukhala yamtengo wapatali, ndiponso dalitso locokela kwa Yehova. Koma makolo ao akadwala, zimene zingabwele mwamsanga m’maganizo ao n’zakuti, ‘Tiyeni tisiye utumiki kuti tikasamalile makolo athu.’ Komabe, zingakhale bwino kuganizila nkhaniyo mwapemphelo ndi kuona ngati makolo ao afunikiladi zimenezo. Sitiyenela kufulumila kusiya utumiki wathu cifukwa nthawi zina zimenezo zingakhale zosafunikila. Kodi vutolo ndi laling’ono cakuti mpingo wa makolo anu ungakwanitse kulisamalila?—Miy. 21:5.
11 Mwacitsanzo, ganizilani za abale aŵili ocokela m’banja limodzi amene anali kutumikila kutali ndi makolo ao. Wina anali kutumikila monga mmishonale ku Paraguay, ndipo wina anali kutumikila ku likulu ku Brooklyn, New York. Makolo okalamba a abalewa anafunikila cithandizo. Ana amenewa ndi akazi ao anapita kukaona makolo ao ku Japan, kuti akaone mmene angathandizile. Mwana amene anali kutumikila ku Paraguay ndi mkazi wake anaganiza zosiya utumiki wao kuti akasamalile makolo. Ndiyeno analandila foni kucokela kwa mgwilizanitsi wa bungwe la akulu wa kumpingo wa makolo ao. Akuluwo anakambilana nkhaniyo ndipo anali kufuna kuti amishonalewo apitilize ndi utumiki wao. Akuluwo anali kuyamikila kwambili utumiki wa amishonalewo ndipo anati adzapeleka thandizo lonse lofunikila kwa makolowo. Banjalo linayamikila kwambili cikondi cimeneco.
12. Kodi banja lacikristu liyenela kutsimikiza ciani posankha mmene lingasamalile makolo okalamba?
12 Zilizonse zimene banja lacikristu lingasankhe posamalila makolo okalamba, onse ayenela kutsimikizila kuti zosankha zao zilemekeza dzina la Mulungu. Tisakhale monga atsogoleli acipembedzo a m’nthawi ya Yesu. (Mat. 15:3-6) Tifuna kuti zosankha zathu zizilemekeza Mulungu ndi mpingo.—2 Akor. 6:3.
ZIMENE MPINGO UYENELA KUCITA
13, 14. Kodi Baibulo lionetsa bwanji kuti mpingo uyenela kugwapo posamalila okalamba?
13 Si mipingo yonse imene ingathandize atumiki a nthawi zonse monga unacitila mpingo umene tachula. Komabe, Baibulo limaonetsa kuti mpingo uyenela kucita zonse zimene ungathe kuthandiza Akristu okalamba. Ponena za mpingo wa ku Yerusalemu Baibulo limati, “panalibe ngakhale mmodzi wosoŵa kanthu.” Izi sizitanthauza kuti onse anali olemela. Mwacionekele, ena anali osauka, koma zopeleka “anali kuzigaŵa kwa aliyense malinga ndi zosoŵa zake.” (Mac. 4:34, 35) Pambuyo pake, mumpingo munabuka vuto lalikulu. Zinamveka kuti “akazi amasiye . . . anali kunyalanyazidwa pa kagaŵidwe ka cakudya ca tsiku ndi tsiku.” Conco, atumwi anasankha amuna oyenelela kuti asamalile akazi amasiye ndi kuwagaŵila cakudya cokwanila. (Mac. 6:1-5) Kugaŵila cakudya catsiku ndi tsiku kunali makonzedwa akanthawi. Makonzedwe amenewa anali akuti asamalile zosoŵa za anthu amene anakhala Akristu pa Pentekosite mu 33 C.E. Ndipo anthuwa anatsala ku Yerusalemu kwa kanthawi kuti alimbikitsidwe mwa kuuzimu. Conco, zimene atumwi anacita zionetsa kuti mpingo ungathandize kusamalila osoŵa.
14 Monga taonela, Paulo anapeleka malangizo kwa Timoteyo ofotokoza mikhalidwe imene ingacititse kuti akazi amasiye acikristu alandile thandizo la mpingo. (1 Tim. 5:3-16) Mofananamo, Yakobo anauzilidwa kulemba za udindo wa Mkristu wosamalila ana ndi akazi amasiye ndi ena amene ali m’mavuto kapena osoŵa. (Yak. 1:27; 2:15-17) Nayenso mtumwi Yohane anati: “Aliyense amene ali ndi zinthu zofunika pa moyo, n’kuona m’bale wake zikumusoŵa, koma osamusonyeza m’bale wakeyo cifundo cacikulu, kodi munthu ameneyu amakonda Mulungu?” (1 Yoh. 3:17) Conco, ngati Mkristu ali ndi udindo wosamalila osoŵa, naonso mpingo uli ndi udindo umenewu.
15. Kodi n’ciani cingathandize posamalila abale ndi alongo okalamba?
15 M’maiko ena boma limathandiza okalamba mwa kupeleka mapenshoni ndi kukonza mapulogalamu othandiza osauka. (Aroma 13:6) Koma kwina makonzedwe amenewa kulibe. Conco, thandizo limene acibale ndi mpingo ungapeleke kwa abale ndi alongo okalamba limasiyana-siyana. Ngati ana akhala kutali ndi makolo ao okalamba, thandizo limene angapeleke kwa io lingakhale locepa. Anawo ayenela kudziŵitsa akulu a ku mpingo wa makolo ao ponena za cisamalilo cimene banja lingapeleke. Mwacitsanzo, akulu angadziŵitse makolowo za thandizo limene boma limapeleka kwa okalamba. Ndiponso, angadziŵitse ana a makolowo zinthu zofunika monga makalata amene sanaŵelengedwe kapena mankhwala amene sanamwedwe. Ngati ana ndi akulu amakambilana bwino-bwino zingathandize kusamalila makolo okalamba. Kukhala ndi wina amene ayang’anila makolo okalamba, kungacepetse nkhawa zimene anawo angakhale nazo.
16. Kodi Akristu ena amacita ciani kuti athandize okalamba mumpingo?
16 Cifukwa cokonda okalamba amenewa, Akristu ena amadzipeleka kuti awathandize mmene angathele. Iwo amawasamalila monga kuti ndi makolo ao eni-eni. Posamalila okalamba amenewa ena amasinthana-sinthana. Popeza kuti Akristu amenewa sangathe kucita utumiki wanthawi zonse, io amasangalala kuthandiza ana a makolowo kuti apitilize ndi utumiki wanthawi zonse. Ndithudi, zimene Akristu amenewa amacita n’zolimbikitsa kwambili! Komabe, thandizo limene amapeleka silicotsela anawo udindo wosamalila makolo ao mmene angathele.
MUZILEMEKEZA OKALAMBA NDI MAU OLIMBIKITSA
17, 18. N’ciani cingatithandize kuti kusamalila okalamba kusakhale kotopetsa?
17 Okalamba pamodzi ndi owasamalila, angacititse zinthu kukhala zosavuta ngati ali ndi maganizo oyenela. Ngati zimenezi zikukhudzani, yesetsani kukhalabe ndi maganizo oyenela. Nthawi zina ukalamba umacititsa munthu kuvutika maganizo. Cotelo, muyenela kuyesetsa kulemekeza ndi kulimbikitsa abale ndi alongo okalamba mwa kulankhula mau olimbikitsa. Tiyenela kuwayamikila amene atumikila zaka zambili. Yehova ndi Akristu anzanu samaiŵala zimene mumacita pom’tumikila.—Ŵelengani Malaki 3:16; Aheberi 6:10.
18 Zocita zatsiku ndi tsiku zidzakhala zosatopetsa ngati okalamba ndi owasamalila amakhala ansangala. (Mlal. 3:1, 4) Okalamba ambili amayesetsa kukhala ndi moyo wosalila zambili. Iwo amadziŵa kuti angapeze cisamalilo cacikulu ngati aonetsa khalidwe labwino. Ambili amene amacezela okalamba kaŵili-kaŵili amati: “Ndinapita kukacezela wokalamba wina, ndipo anandilimbikitsa kwambili.”—Miy. 15:13; 17:22.
19. N’ciani cingathandize acicepele ndi okalamba kukhalabe olimba panthawi zovuta?
19 Timalakalaka nthawi pamene ukalamba, kuvutika ndi kupanda ungwilo zidzatha. Pakali pano, atumiki a Mulungu ayenela kuyembekezelabe moyo wosatha. Timadziŵa kuti kukhulupilila malonjezo a Mulungu kungatithandize kukhala olimba panthawi zovuta. Cifukwa ca cikhulupililo cathu, “sitikubwelela m’mbuyo. Koma ngakhale munthu wathu wakunja akutha, ndithudi munthu wathu wamkati akukhalitsidwanso watsopano tsiku ndi tsiku.” (2 Akor. 4:16-18; Aheb. 6:18, 19) Nanga n’ciani cingathandizenso amene asamalila okalamba? M’nkhani yotsatila tidzakambilana mfundo zothandiza.
a M’nkhani yotsatila tidzakambilana njila zina zimene zingathandize makolo okalamba ndi ana ao.