Nyimbo 141
Kusakila Anthu Okonda Mtendele
Yopulinta
Yesu anati: ‘Lalikilani.’
Paliponse, kulikonse,
Iye analalikila.
Anasakila nkhosa za M’lungu
Mpaka kuloŵa
kwa dzuŵa ‘nasakilabe.
Mu makomo na m’misewu,
Tilalikila ‘liyense
Tiuza anthu:
“Mavuto adzatha.”
(KOLASI)
Tisakila
A mtendele m’mitundu yonse.
Tisakila
Ofunadi cipulumutso,
Sitisiya
aliyense.
Nthawi ikutha, ticite cangu.
Tisakile, tifufuze,
Tipulumutseko ena.
Cifukwa timawakonda anthu.
Timabwelelako
na mau otontoza.
Mu midzi na m’matauni
Tisakila omvetsela,
Ndipo tikawapeza timakondwa.
(KOLASI)
Tisakila
A mtendele m’mitundu yonse.
Tisakila
Ofunadi cipulumutso,
Sitisiya
aliyense.
(Onaninso Yes. 52:7; Mat. 28:19, 20; Luka 8:1; Aroma 10:10.)