Nyimbo 140
Umoyo wa Mpainiya
Yopulinta
(Mlaliki 11:6)
Kukaca kuseni, tikali na tulo,
Timayenda
kulalikila anthu, kulikonse.
Timamwetulila powalalikila.
Ndipo sitileka,
ngakhale ena samvetsela.
(KOLASI)
Uyu ni umoyo
umene tasankha;
Kucita zofuna za M’lungu.
M’dzuŵa na mu mvula
ise tipilila.
Timaonetsa kuti M’lungu tim’konda.
Pofika m’madzulo, tikhala olema,
Koma timakhala
na cisangalalo mumtima.
Uyu ni umoyo, ise tinasankha.
Tiyamika Yehova
cifukwa watidalitsa.
(KOLASI)
Uyu ni umoyo
umene tasankha;
Kucita zofuna za M’lungu.
M’dzuŵa na mu mvula
ise tipilila.
Timaonetsa kuti M’lungu tim’konda.
(Onaninso Yos. 24:15; Sal. 92:2; Aroma 14:8.)