Nyimbo 146
Munacitila Ine
Abale a Yesu
ndi a Nkhosa zina,
Amatumikila mogwilizana.
Zimene a nkhosa zina amacita
Yesu Khristu adzazikumbukila.
(KOLASI)
“Munanitonthoza, powatonthoza.
Zonse zimene munawacitila,
imwe munali kucitila ine.
Zonse imwe munawacitila,
Imwe munali kucitila ine.”
“Ninali na njala, ninali na njota,
Munabwela msanga kunithandiza.”
“Tiuzeni, izi
tinacita liti?”
Ndiyeno Mfumu idzayankha kuti:
(KOLASI)
“Munanitonthoza, powatonthoza.
Zonse zimene munawacitila,
imwe munali kucitila ine.
Zonse imwe munawacitila,
Imwe munali kucitila ine.”
“Mokhulupilika munagwila nchito
yolalikila na abale anga.
Landilani dziko
na moyo wosatha.”
Mfumu idzauza a nkhosa zina.
(KOLASI)
“Munanitonthoza, powatonthoza.
Zonse zimene munawacitila,
imwe munali kucitila ine.
Zonse imwe munawacitila,
Imwe munali kucitila ine.”
(Onaninso Miy. 19:17; Mat. 10:40-42; 2 Tim. 1:16, 17.)