NYIMBO 26
Munacitila Ine
1. Abale a Yesu
ndi a nkhosa zina,
Amatumikila mogwilizana.
Zimene a nkhosa zina amacita
Yesu Khristu adzazikumbukila.
(KOLASI)
“Munanitonthoza, poŵatonthoza.
Zonse zimene munaŵacitila,
Imwe munali kucitila ine.
Zonse imwe munaŵacitila,
Imwe munali kucitila ine.”
2. “Ninali na njala, ninali na njota,
munabwela msanga munathandiza.”
“Tiuzeni, izi
tinacita liti?”
Ndiyeno Mfumu idzayankha kuti:
(KOLASI)
“Munanitonthoza, poŵatonthoza.
Zonse zimene munaŵacitila,
Imwe munali kucitila ine.
Zonse imwe munaŵacitila,
Imwe munali kucitila ine.”
3. “Mokhulupilika munagwila nchito,
yolalikila na abale anga.
Landilani dziko
na moyo wosatha.”
Mfumu idzauza a nkhosa zina.
(KOLASI)
“Munanitonthoza, poŵatonthoza.
Zonse zimene munaŵacitila,
Imwe munali kucitila ine.
Zonse imwe munaŵacitila,
Imwe munali kucitila ine.”
(Onaninso Miy. 19:17; Mat. 10:40-42; 2 Tim. 1:16, 17.)