Nyimbo 149
Tikuyamikani Cifukwa ca Dipo
Yopulinta
Atate Yehova
tikuyamikani
cifukwa ca cikondi
munationetsa.
Munapeleka mphatso
ya Mwana wanu
kuti ise tikapeze
moyo wosatha.
(KOLASI)
Anafela anthu onse
kuti atipulumutse.
Ise tidzakuyamikilani
kwamuyaya.
Mwa cikondi
Yesu anadzipeleka
Kufela anthu onse
akapeze moyo.
Mphatso imene Yesu
anapeleka
imapatsa anthu onse
ciyembekezo.
(KOLASI)
Anafela anthu onse
kuti atipulumutse.
Ise tidzakuyamikilani
kwamuyaya.
(Onaninso Aheb. 9:13, 14; 1 Pet.1:18, 19.)