NYIMBO 18
Tikuyamikani Cifukwa ca Dipo
Yopulinta
1. Atate Yehova
tikuyamikani,
Cifukwa ca cikondi
munationetsa.
Munapeleka mphatso
ya Mwana wanu,
kuti ise tikapeze
moyo wosatha.
(KOLASI)
Anafela anthu onse
kuti atipulumutse.
Ise tidzakuyamikilani
kwamuyaya.
2. Mwa cikondi
Yesu anadzipeleka.
Kufela anthu onse
akapeze moyo.
Mphatso imene Yesu
anapeleka,
imapatsa anthu onse
ciyembekezo.
(KOLASI)
Anafela anthu onse
kuti atipulumutse.
Ise tidzakuyamikilani
kwamuyaya.
(Onaninso Aheb. 9:13, 14; 1 Pet. 1:18, 19.)