Nyimbo 154
Tidzapilila Mosalekeza
Yopulinta
Daunilodi
Yesu anati,
‘Pililani mayeselo.’
Anapeleka
citsanzo ca kupilila.
Anali kudziŵa
lonjezo la M’lungu.
(KOLASI)
Tiyeni tipilile.
Tikhale olimba.
Mwa mphamvu ya Yehova,
Ise tipilile mosaleka.
Tingakumane
Na mavuto nthawi zina.
Koma tidziŵa
M’lungu adzatidalitsa
Na moyo wosatha
m’dziko la mtendele.
(KOLASI)
Tiyeni tipilile.
Tikhale olimba.
Mwa mphamvu ya Yehova,
Ise tipilile mosaleka.
Sitidzafoka
Kapena kucita mantha.
Tidzapilila
potumikila Yehova.
Mavuto adzatha
m’dziko latsopano.
(KOLASI)
Tiyeni tipilile.
Tikhale olimba.
Mwa mphamvu ya Yehova,
Ise tipilile mosaleka.
(Onaninso Mac 20:19, 20; Yak 1:12; 1 Pet 4:12-14.)