MUTU 4
Mmene Mpingo Anaukonzela na Mmene Amauyendetsela
M’KALATA yoyamba kwa Akorinto, mtumwi Paulo anachula mfundo yofunika kwambili ponena za Mulungu. Analemba kuti: “Mulungu si Mulungu wacisokonezo, koma wamtendele.” Ndiyeno pokamba za misonkhano ya mpingo, anati: “Zinthu zonse zizicitika moyenela ndi mwadongosolo.”—1 Akor. 14:33, 40.
2 Kuciyambi kweni-kweni kwa kalatayo, Paulo anapeleka uphungu cifukwa ca magaŵano omwe anali mumpingo wa Akorinto. Analimbikitsa abalewo kuti ‘azilankhula mogwilizana,’ komanso kuti akhale “ogwilizana pokhala ndi mtima umodzi ndi maganizo amodzi.” (1 Akor. 1:10, 11) Anawapatsanso uphungu pa nkhani zina zosiyana-siyana zimene zinali kusokoneza mgwilizano mumpingo. Pofuna kulimbikitsa mfundo ya umodzi na mgwilizano, iye anaseŵenzetsa citsanzo ca thupi la munthu. Analimbikitsa onse mumpingo wacikhristu kukhala okondana, mosayang’ana udindo wa munthu. (1 Akor. 12:12-26) Kuti mgwilizano umenewu utheke mumpingo, panafunika dongosolo m’kacitidwe ka zinthu.
3 Ndiye kodi mpingo wacikhristu umenewo unakhazikitsidwa mwadongosolo lotani? Nanga anaukhazikitsa ndani? Ndipo ndani anali kutumikila pa maudindo? Lekani Baibo itiunikile mayankho pa mafunso amenewa.—1 Akor. 4:6.
UNAKHAZIKITSIDWA NA MULUNGU
4 Mpingo wacikhristu unakhazikitsidwa pa tsiku la Pentekosite mu 33 C.E. Kodi tiyenela kudziŵa mfundo yanji ponena za mpingo woyambilila umenewo? Ni mfundo yakuti unakhazikitsidwa na Mulungu mwiniwake, ndipo anautsogolela mwadongosolo. Nkhani youzilidwa yosimba zimene zinacitika ku Yerusalemu zaka pafupi-fupi 2,000 zapitazo, imaonetsa kuti mpingo wa Akhristu odzozedwa umenewo unakhazikitsidwadi na Mulungu. (Mac. 2:1-47) Unali nyumba ya Mulungu, inde banja lake. (1 Akor. 3:9; Aef. 2:19) Conco, mpingo wacikhristu wa masiku ano umatsatilabe dongosolo limene linakhazikitsidwa m’nthawi ya Akristu oyambilila.
Masiku ano, mipingo yonse ya Mboni za Yehova imatsatila dongosolo limene linakhazikitsidwa m’nthawi ya Akhristu oyambilila
5 Mpingo woyambilila unali na ophunzila okwana 120. Mzimu woyela unatsanulidwa pa ophunzila amenewo kukwanilitsa ulosi wa pa Yoweli 2:28, 29. (Mac. 2:16-18) Ndipo patsiku lomwelo anthu pafupi-fupi 3,000 anabatizika m’madzi, na kuloŵa mumpingo wa anthu obadwa mwa mzimu woyela. Anthuwo anakhulupilila uthenga wonena za Khristu, ndipo “anapitiliza kulabadila zimene atumwiwo anali kuphunzitsa.” Pambuyo pake, “Yehova anapitiliza kuwawonjezela anthu amene anali kuwapulumutsa.”—Mac. 2:41, 42, 47.
6 Mpingo ku Yerusalemu unakula mothamanga kwambili, cakuti mkulu wa ansembe waciyuda anadandaula kuti ophunzilawo anadzaza Yerusalemu na ciphunzitso cawo. Ophunzila atsopano ku Yerusalemu anaphatikizapo ansembe ambili aciyuda. Nawonso analoŵa mumpingo wacikhristu.—Mac. 5:27, 28; 6:7.
7 Yesu anakamba kuti: “Mudzakhala mboni zanga mu Yerusalemu, ku Yudeya konse ndi ku Samariya, mpaka kumalekezelo a dziko lapansi.” (Mac. 1:8) Izi zinacitika pamene cizunzo coopsa cinabuka ku Yerusalemu, pambuyo pa kuphedwa kwa Sitefano. Ophunzilawo anathaŵila ku Yudeya na ku Samariya. Koma kulikonse kumene anapitako anapitiliza kulalikila uthenga wabwino na kupanga ophunzila, kuphatikizapo Asamariya. (Mac. 8:1-13) M’kupita kwa nthawi, uthenga wabwino unafika mpaka kwa anthu osadulidwa, amene sanali Ayuda. (Mac. 10:1-48) Zotulukapo za nchito yolalikila imeneyi n’zakuti ophunzila anaculuka kwambili, ndiponso mipingo yambili yatsopano inakhazikitsidwa kunja kwa Yerusalemu.—Mac. 11:19-21; 14:21-23.
8 Nanga panakhala makonzedwe otani pofuna kuti mpingo uliwonse watsopano ukhale wolinganizidwa bwino, na kuyendetsedwa m’njila ya Mulungu? Mwa mzimu wa Mulungu, abusa aang’ono anasankhidwa kuti asamalile nkhosa za Mulungu. M’mipingo imene Paulo na Baranaba anacezela pa ulendo wawo woyamba wa umishonale, anali kuika akulu. (Mac. 14:23) Wolemba Baibo Luka anafotokoza za miting’i imene Paulo anakhala nayo na akulu a mpingo wa ku Efeso. Paulo anawauza kuti: “Mukhale chelu ndi kuyang’anila gulu lonse la nkhosa, limene mzimu woyela wakuikani pakati pawo kukhala oyang’anila, kuti muwete mpingo wa Mulungu, umene anaugula ndi magazi a Mwana wake weniweni.” (Mac. 20:17, 28) Amunawo anayenelezedwa kukhala akulu cifukwa anakwanilitsa ziyenelezo za m’Malemba. (1 Tim. 3:1-7) Tito, wanchito mnzake wa Paulo, anapatsidwa mphamvu zoika akulu m’mipingo ya ku Kerete.—Tito 1:5.
9 Pamene mipingo inali kuwonjezeleka, atumwi komanso akulu ku Yerusalemu ndiwo anakhala oyang’anila akutsogolo a mipingo yonse m’nthawi ya Akhristu oyambilila. Inde, ndiwo anali m’bungwe lolamulila.
10 M’kalata yake yopita ku mpingo wa ku Efeso, mtumwi Paulo anafotokoza kuti kutsatila citsogozo ca mzimu wa Mulungu, komanso kugonjela umutu wa Yesu Khristu, kudzathandiza mpingo wacikhristu kukhalabe wogwilizana. Mtumwiyu analimbikitsa Akhristu amenewo kukhala odzicepetsa, na “kusunga umodzi wathu mwa mzimuwo,” pocita zinthu mwamtendele na onse mumpingo. (Aef. 4:1-6) Kenako anagwila mawu Salimo 68:18, pochula makonzedwe a Yehova akuti abale oyenelela mwauzimu azitumikila mumpingo monga atumwi, aneneli, alaliki, abusa, komanso aphunzitsi. Amuna otelo, amene ni mphatso zocokela kwa Yehova, anathandiza mpingo kukhala wolimba kuuzimu, zimene zinakondweletsa Mulungu.—Aef. 4:7-16.
MIPINGO MASIKU ANO IMATSATILA DONGOSOLO LIMENE LINAKHAZIKITSIDWA M’NTHAWI YA ATUMWI
11 Masiku ano, mipingo yonse ya Mboni za Yehova imatsatila dongosolo limene linakhazikitsidwa mumpingo woyambilila kalelo. Mipingo yonse imeneyi imapanga gulu logwilizana padziko lonse, limene Akhristu odzozedwa na mzimu ndiwo phata lake. (Zek. 8:23) Izi zinatheka cifukwa ca Yesu Khristu. Monga mwa lonjezo lake, iye wakhalabe na ophunzila ake odzozedwa “masiku onse mpaka m’nyengo ya mapeto a nthawi ino.” Anthu amene akuloŵa mumpingo amakhulupilila uthenga wabwino wonena za Mulungu, amadzipatulila kwa Yehova, kenako amabatizika monga ophunzila a Yesu. (Mat. 28:19, 20; Maliko 1:14; Mac. 2:41) Amavomeleza kuti Yesu Khristu ndiye “m’busa wabwino,” kutinso ndiye Mutu wa gulu lonse la nkhosa, lophatikizapo Akhristu odzozedwa na “nkhosa zina.” (Yoh. 10:14, 16; Aef. 1:22, 23) “Gulu limodzi “ limeneli ni logwilizana cifukwa onse amalemekeza utsogoleli wa Khristu, na kugonjela kwa “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu,” woikidwa na Khristu. Conco, tiyeni tipitilize kum’dalila na kum’khulupilila kapolo ameneyu.—Mat. 24:45.
NCHITO YA MABUNGWE ALAMULO
12 Kuti cakudya cauzimu cizipelekedwa pa nthawi yake, komanso kuti uthenga wabwino wa Ufumu ulalikidwe mapeto asanafike, gulu lathu linakhazikitsa mabungwe alamulo. Mabungwe amenewa amalembetsedwa kuboma m’maiko osiyana-siyana, ndipo amacita zinthu mogwilizana. Amathandiza kuti nchito yolalikila pa dziko lonse izigwilika bwino.
MAKONZEDWE A OFESI YA NTHAMBI
13 Ofesi ya nthambi ikakhazikitsidwa, Bungwe Lolamulila limasankha abale atatu kapena oposelapo kukhala Komiti ya Nthambi. Abalewa ndiwo amayang’anila nchito ya m’dzikolo, mwinanso na maiko ena osamalidwa na nthambi yawo. M’bale mmodzi wa m’komitiyo amasankhidwa kukhala mgwilizanitsi wa Komiti ya Nthambi.
14 Mipingo yonse yoyang’anilidwa na ofesi ya nthambi amaigaŵa kupanga madela. Madelawo amasiyana-siyana kukula kwake potengela malo, cilankhulo, komanso ciŵelengelo ca mipingo imene ofesi ya nthambi imayang’anila. Woyang’anila dela amaikidwa kuti azitumikila mipingo yopanga dela. Ndiponso ofesi ya nthambi ndiyo imapeleka malangizo kwa woyang’anila dela a mmene ayenela kugwilila nchito yake.
15 Mipingo imatsatila makonzedwe amenewa kuti tonsefe tipindule. Pamaikidwa akulu amene amayang’anila nchito pa nthambi zolekana-lekana, madela, komanso m’mipingo. Tonse timadalila kapolo wokhulupilika ndi wanzelu, amene amatigaŵila cakudya cauzimu pa nthawi yake. Nayenso kapolo wokhulupilika amalemekeza Khristu monga mutu wa mpingo, ndiponso amamamatila ku mfundo za m’Baibo, na kulabadila citsogozo ca mzimu woyela. Pamene tonsefe pamodzi ticita zinthu mogwilizana, timapeza madalitso ofanana na amene Akhristu oyambilila anapeza. Inde, “mipingo inapitiliza kulimba m’cikhulupililo ndipo ciŵelengelo cinapitiliza kuwonjezeka tsiku ndi tsiku.”—Mac. 16:5.