LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • od mutu 12 masa. 123-129
  • Kucilikiza Nchito ya Ufumu m’Dziko Lathu Komanso Padziko Lonse

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kucilikiza Nchito ya Ufumu m’Dziko Lathu Komanso Padziko Lonse
  • Gulu Lokhazikitsidwa Kucita Cifunilo ca Yehova
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • NDALAMA ZOYENDETSELA NCHITO YA UFUMU PADZIKO LONSE
  • KUSAMALILA ZOFUNIKILA ZA MPINGO
  • KUSAMALILA ZOPELEKA
  • THUMBA LA DELA
  • KUSAMALILA OSAUKA
  • KUGAŴILA MABUKU
  • Mmene Timapezela Ndalama Zoyendetsela Nchito za Ufumu
    Ufumu wa Mulungu Ukulamulila
  • Oyang’anila Oweta Nkhosa za Mulungu
    Gulu Lokhazikitsidwa Kucita Cifunilo ca Yehova
  • Njila Zowonjezela Utumiki Wanu
    Gulu Lokhazikitsidwa Kucita Cifunilo ca Yehova
  • Kodi N’kumupatsilanji Amene Zonse N’zake?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2018
Gulu Lokhazikitsidwa Kucita Cifunilo ca Yehova
od mutu 12 masa. 123-129

MUTU 12

Kucilikiza Nchito ya Ufumu m’Dziko Lathu Komanso Padziko Lonse

POKWANILITSA ulosi wa Yesu wonena za masiku otsiliza, Mboni za Yehova zimalalikila uthenga wabwino “mpaka kumalekezelo a dziko lapansi.” (Mac. 1:8; Mat. 24:14) Kuti izi zitheke, iwo amadzipeleka na mtima wonse mwa kuseŵenzetsa nthawi komanso mphamvu zawo pouzako ena zinthu zauzimu. Podalila Yehova kuti adzawapatsa zosoŵa zawo monga anchito anzake, amaikabe Ufumu wa Mulungu patsogolo mu umoyo wawo. (Mat. 6:25-34; 1 Akor. 3:5-9) Zotulukapo zake zionetselatu kuti Yehova amakondwela na utumiki wawo ndipo akuwadalitsa.

NDALAMA ZOYENDETSELA NCHITO YA UFUMU PADZIKO LONSE

2 Anthu poona kuti polalikila timagaŵila kwaulele ma Baibo na mabuku ena ophunzitsa Baibo, ena amafunsa kuti: “Koma zimatheka bwanji?” Ndipo m’pake kufunsa, cifukwa kupulinta ma Baibo na mabuku ophunzitsa Baibo kumalila ndalama zambili. Kumanga na kusamalila nyumba za Beteli za atumiki ogwila nchito zopulinta mabuku, oyang’anila nchito yolalikila, komanso ogwila nchito zina zopititsa patsogolo uthenga wabwino, kumalilanso ndalama. Si apo pokha, oyang’anila madela, amishonale, apainiya apadela, komanso ena amene ali mu utumiki wanthawi zonse wapadela amapatsidwako alawansi yocepa yowathandizila kuti apitilize mautumiki awo. Monga mwaonela, nchito yolalikila uthenga wabwino m’masiku athu ano, kaya m’dziko lathu kapena padziko lonse, imalila ndalama zambili-mbili. Ndiye ndalamazo zimacokela kuti?

3 Anthu akufuna kwabwino oyamikila nchito ya Mboni za Yehova yophunzitsa anthu Baibo, mwa ufulu wawo amapeleka thandizo la ndalama pocilikiza nchito yathu ya padziko lonse. Koma kwakukulu-kulu, ndalama zambili zoyendetsela nchito yathu zimacokela kwa Mboni za Yehova. Ndipo ena a Mboni amatumiza zopeleka zawo mwacindunji ku ofesi ya nthambi ya m’dziko lawo. Iwo amaonetsa mzimu wodzipeleka umenenso atumiki a Mulungu akale anaonetsa popeleka mowolowa manja zothandizila pa nchito yomanga malo olambilila Yehova. (Eks. 35:20-29; 1 Mbiri 29:9) Zina zimacokela ku cuma monga nyumba kapena malo amene mwiniwake anapeleka ku gulu monga mphatso mu wilu yake. Zopeleka zina zimacokela kwa anthu, mipingo, komanso madela. Nthawi zambili zopelekazi zimakhala zing’ono-zing’ono. Koma kuziwonkhetsa pamodzi zimakwanitsa kuyendetsa nchito yathu yonse.

Mboni za Yehova zimaona kuti ni mwayi wapadela kuseŵenzetsa ndalama zawo na zinthu zina popititsa patsogolo nchito yolalikila

4 Mboni za Yehova zimaona kuti ni mwayi wapadela kuseŵenzetsa ndalama zawo na zinthu zina kupititsila patsogolo nchito yolalikila. Yesu na ophunzila ake anali na kabokosi kosungilamo ndalama. Ni mmene anali kucotsa ndalama zosamalila zinthu zofunikila. (Yoh. 13:29) Baibo imatiuzanso za akazi ena amene anatumikila Yesu na ophunzila ake. (Maliko 15:40, 41; Luka 8:3) Mtumwi Paulo anayamikila thandizo la zinthu zakuthupi zocokela kwa aja ofuna kupititsa patsogolo uthenga wabwino. Anam’thandiza kuti apitilize bwino utumiki wake. (Afil. 4:14-16; 1 Ates. 2:9) Mboni za Yehova masiku ano zimatengela citsanzo ca atumiki amakedzana amenewa poonetsa mzimu wopeleka mowolowa manja. Izi zimathandiza kuti anthu oona mtima padziko lonse alandile “madzi a moyo kwaulele.”—Chiv. 22:17.

KUSAMALILA ZOFUNIKILA ZA MPINGO

5 Zofunikila za mpingo nazonso zimasamalidwa na zopeleka zaufulu. Pamisonkhano yathu sipakhala kuyendetsa mbale ya pelekani-pelekani, kapena kuikila munthu mlingo wa ndalama zakuti azipeleka, ndiponso sitipemphetsa ndalama. Pamalo athu osonkhanila pamakhala tumabokosi toponyamo zopeleka kuti aliyense mwa kufuna kwake acite copeleka “mogwilizana ndi mmene watsimikizila mumtima mwake.”—2 Akor. 9:7.

6 Ndalama zikapelekedwa, coyamba zimagwila nchito yolipila zofunikila pa Nyumba ya Ufumu. Komanso bungwe la akulu lingagwilizane kuti ndalama zina zitumizidwe ku ofesi yawo ya nthambi kuti zikathandize pa nchito ya padziko lonse. Zikakhala conco, akulu amakonza cigamulo kuti mpingo ukavomeleze. Mwanjila imeneyi, mipingo yambili imatumiza copeleka mwezi uliwonse cothandizila nchito ya padziko lonse. Ngati onse mumpingo amakumbukila zofunikila za mpingo zolila ndalama, zingapewetse kumalengeza kaŵili-kaŵili kuti pakufunikila zopeleka.

KUSAMALILA ZOPELEKA

7 Pambuyo pa msonkhano uliwonse, abale aŵili ayenela kucotsa ndalama m’tumabokosi twa zopeleka na kuzilemba. (2 Maf. 12:9, 10; 2 Akor. 8:20) Bungwe la akulu limakhazikitsa njila yosungila bwino ndalamazi kufikila zitatumizidwa ku ofesi ya nthambi, kapena kugwila nchito zofunikila pampingo. M’bale wosamalila maakaunti a mpingo amakonza lipoti lapamwezi lodziŵitsa mpingo za mmene ndalama zinayendela. Ndipo pambuyo pa miyezi itatu iliyonse, mgwilizanitsi wa bungwe la akulu amakonza zopenda maakaunti.

THUMBA LA DELA

8 Ndalama zoyendetsela msonkhano wadela, komanso zolipilila zinthu zina za dela, zimacokela kwa Mboni za m’delalo. Tumabokosi twa zopeleka tumaikidwa pamalo a msonkhano kuti anthu aziponyamo mwa ufulu wawo. Ndiponso, pa zofunikila za dela za nthawi zonse, mipingo ingacitenso zopeleka panthawi ina iliyonse.

9 Kweni-kweni, dela liyenela kukwanitsa kulipilila zonse zoyendetsela msonkhano wadela, na kutsalako na ndalama yotumiza monga copeleka ku nchito ya padziko lonse. Koma ngati kwapezeka kuti kuthumba la dela kulibe ndalama zokwanila kulipilila zowonongedwa za msonkhano wadela, kapena zokonzekelela msonkhano wadela wotsatila, monga kulipila malo ocitilapo msonkhano wadela wotsatila, woyang’anila dela angapeleke malangizo akuti mipingo idziŵitsidwe za mwayi wocita zopeleka. Ndiyeno bungwe la akulu lililonse lidzakambilana kuona kuti mpingo wawo ungacite copeleka ca ndalama zingati ku thumba la dela. Akatelo, adzakonza cigamulo cokapeleka ku mpingo.

10 Pakabuka nkhani zokhudza dela zofuna ndalama, akulu a m’delalo amakhala na miting’i pa msonkhano wawo wadela. Zonse zimene akuluwo agwilizana zokhudza ndalama, ziyenela kulembedwa monga cigamulo, kupatulapo zowonongedwa za masiku onse. Pa zigamulo zimenezo, payenela kulembedwa ndalama zeni-zeni zofunikila. Ndipo nthawi zonse zigamulozo ziyenela kuvomelezedwa coyamba musanaseŵenzetse ndalama za dela.

11 Panthawi yake, makonzedwe amapangidwa openda maakaunti a dela.

KUSAMALILA OSAUKA

12 Colinga cina ca kabokosi ka ndalama komwe Yesu na ophunzila ake anali nako, cinali kuthandizila osauka. (Maliko 14:3-5; Yoh. 13:29) Udindo wa Akhristu umenewu ukaliko mpaka lelo, cifukwa Yesu anati: “Osaukawo muli nawo nthawi zonse.” (Maliko 14:7) Kodi Mboni za Yehova zimasamalila bwanji udindo umenewu masiku ano?

13 Nthawi zina, atumiki okhulupilika mumpingo angafunikile thandizo lakuthupi cifukwa ca ukalamba, matenda, kapena mavuto ena osoŵa nawo mtengo wogwila. Acibale awo kapena anthu ena odziŵa za vutolo angagwepo n’kuthandiza. Izi n’zogwilizana na mawu a mtumwi Yohane akuti: “Aliyense amene ali ndi zinthu zofunika pa moyo, n’kuona m’bale wake zikumusoŵa, koma osamusonyeza m’bale wakeyo cifundo cacikulu, kodi munthu ameneyu amakonda Mulungu? Ana anga okondedwa, tisamakondane ndi mawu okha kapena ndi pakamwa pokha, koma tizisonyezana cikondi ceni-ceni m’zocita zathu.” (1 Yoh. 3:17, 18; 2 Ates. 3:6-12) Kulambila koona kumaphatikizapo kusamalilanso mwakuthupi Akhristu okhulupilika.—Yak. 1:27; 2:14-17.

14 M’kalata yake yoyamba kwa Timoteyo, mtumwi Paulo anafotokoza mmene tingathandizile ofunikila thandizo lakuthupi. Mungaŵelenge malangizo amenewa pa 1 Timoteyo 5:3-21. Udindo waukulu uli paphewa la Mkhristu aliyense, cifukwa ndiye ayenela kusamalila a pabanja lake. Okalamba kapena athanzi lofooka ayenela kulandila thandizo kwa ana awo, adzukulu awo, kapena abululu ŵawo. Nthawi zina, pangakhale thandizo la boma kapena locokela ku mabungwe othandiza anthu ovutika. Conco, abululu ŵawo kapena anthu ena angawafotokozele ndondomeko zopezela mathandizo otelowo. Koma nthawi zina pangagwe vuto lofuna kuti mpingo wonse ugwepo ndithu kuthandiza abale na alongo omwe atumikila mokhulupilika kwa nthawi yaitali. Ngati palibe wacibale aliyense amene angawathandize, kapena ngati boma silikupeleka thandizo lokwanila, bungwe la akulu lingakonze zakuti mpingo upelekepo thandizo. Akhristu amaona kuti ni mwayi kugaŵilako zinthu zawo zakuthupi aja amene afunikila thandizo.

15 Abale na alongo ena angapezeke mu umphawi cifukwa ca kuzunzidwa, nkhondo, zivomezi, kusefukila kwa madzi, njala, kapena mavuto ena ofala m’masiku ano otsiliza. (Mat. 24:7-9) Nthawi zina mipingo ya m’delalo ingakhale ilibe ciliconse cowathandiza naco. Zikatelo, Bungwe Lolamulila limadziŵitsa abale a kumadela ena za vutolo, na kutsogolela nchito yopeleka thandizo. Ni mmenenso Akhristu a ku Asia Minor anacitila kuti apeleke thandizo la cakudya kwa abale awo ku Yudeya panthawi ya njala. (1 Akor. 16:1-4; 2 Akor. 9:1-5) Potengela citsanzo cawo, timaonetsa kuti timaŵakondadi abale athu, komanso kuti ndifedi ophunzila a Yesu Khristu eni-eni.—Yoh. 13:35.

KUGAŴILA MABUKU

16 Ma Baibo na mabuku ophunzitsa Baibo amathandiza kwambili pa nchito yofalitsa uthenga wa Ufumu. Kambili, bungwe la akulu limasankha mtumiki wothandiza kuti azionetsetsa kuti mpingo wawo uli na zofalitsa zokwanila. Abale opatsidwa udindo umenewu sautenga mopepuka ayi. Amalemba bwino-bwino ziŵelengelo za mabuku amene alandila, komanso amene akufunikila pampingo.

17 Monga Akhristu odzipatulila, timadziŵa kuti nthawi yathu, nzelu, mphamvu, maluso, ngakhale cuma cathu cimene, kuphatikizaponso moyo wathu weni-weniwo, ni mphatso zocokela kwa Mulungu zimene amafuna kuti tiziseŵenzetse pom’tumikila. (Luka 17:10; 1 Akor. 4:7) Mwa kuseŵenzetsa bwino zonse zimene tili nazo, timaonetsa kuzama kwa cikondi cathu pa Yehova. Cokhumba ca mtima wathu ni kulemekeza Yehova na zonse zimene tili nazo, podziŵa kuti iye amakondwela na mphatso iliyonse yoonetsa kuti tinadzipeleka kwa iye na mtima wonse. (Miy. 3:9; Maliko 14:3-9; Luka 21:1-4; Akol. 3:23, 24) Yesu anati: “Munalandila kwaulele, patsani kwaulele.” (Mat. 10:8) Podzipeleka ife eni na zinthu zathu potumikila Yehova, timalandila cimwemwe coculuka.—Mac. 20:35.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani