LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • rj gao 5 masa. 12-15
  • Bwelelani kwa “Mbusa Wanu ndi Woyang’anila Miyoyo Yanu”

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Bwelelani kwa “Mbusa Wanu ndi Woyang’anila Miyoyo Yanu”
  • Bwelelani kwa Yehova
  • Nkhani Zofanana
  • “Bwelelani kwa Ine”
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2020
  • Adzakulimbitsa
    ‘Imbani Mokweza ndi Mosangalala’ kwa Yehova
  • Mulungu Adzakupatsani Mphamvu
    Imbirani Yehova
  • Yehova Amakukondani Kwambili!
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2021
Onaninso Zina
Bwelelani kwa Yehova
rj gao 5 masa. 12-15

MBALI 5

Bwelelani kwa “Mbusa Wanu ndi Woyang’anila Miyoyo Yanu”

Mwina poŵelenga kabuku kano, mwapeza kuti kakukamba zimene zinakucitikilani. Ngati ndi conco, dziŵani kuti simuli nokha. Pali atumiki a Mulungu ambili okhulupilika, amakono ndiponso ochulidwa m’Baibulo, amene akumana ndi zopinga ngati zimenezi. Yehova anawathandiza kugonjetsa zopingazo, ndipo inunso adzakuthandizani.

Yehova adzakulandilani mukabwelela kwa iye

DZIŴANI kuti Yehova adzakulandilani mukabwelela kwa iye. Adzakuthandizaninso kulimbana ndi nkhawa, kusiya kudziimba mlandu, ndi kukhala ndi cikumbumtima coyela. Cikumbumtima coyela cidzakupatsani mtendele mumtima ndi m’maganizo. Ndiyeno mwina mudzafuna kuyambanso kutumikila Yehova pamodzi ndi alambili anzanu. Mukacita zimenezi, mudzafanana ndi Akristu ena oyambilila, amene mtumwi Petulo anawalembela kuti: “Munali ngati nkhosa zosocela, koma tsopano mwabwelela kwa mbusa wanu ndi woyang’anila miyoyo yanu.”—1 Petulo 2:25.

Kunena zoona, palibe cinthu cina cabwino kwambili cimene mungacite kuposa kubwelela kwa Yehova. N’cifukwa ciani tikutelo? Cifukwa cakuti mukabwelela kwa Yehova, mudzakondweletsa mtima wake. (Miyambo 27:11) Inu mukudziŵa kuti zocita zathu zimam’khudza Yehova. Ndipo Yehova satikakamiza kuti tizim’konda ndi kum’tumikila. (Deuteronomo 30:19, 20) Katswili wina wa Baibulo anati: “Palibe amene angakutsegulileni mtima wanu. Muyenela kuutsegula nokha.” Tingatsegule mtima wathu ngati tilambila Yehova cifukwa com’konda ndi mtima wathu wonse. Tikatelo, timapatsa Mulungu mphatso yamtengo wapatali. Mphatso imeneyo ndi kukhulupilika kwathu, ndipo mtima wake umakondwela kwambili. Inde, kulambila Yehova m’njila yoyenela kumatibweletsela cimwemwe cosaneneka.—Machitidwe 20:35; Chivumbulutso 4:11.

Mlongo wozilala alandilidwa mwacimwemwe mumpingo

Mukayamba kulambila Mulungu, mudzakhutilitsanso zosoŵa zanu za kuuzimu. (Mateyu 5:3) Tikunena conco cifukwa cakuti padziko lonse lapansi, anthu sadziŵa cifukwa cake tili ndi moyo. Iwo ali ndi njala yofuna kudziŵa colinga ca moyo. Ali ndi njala imeneyi cifukwa ndi mmene Yehova anawalengela. Iye anatilenga mwa njila yakuti tizikhala okhutila pom’tumikila. Conco, ngati tilambila Yehova cifukwa com’konda, timakhala okhutila kwambili.—Salimo 63:1-5.

Dziŵani kuti Yehova akufuna kuti mubwelele kwa iye. Kodi mungatsimikize bwanji zimenezi? Taganizilani mfundo izi: Mapemphelo ambili anapelekedwa pokonza kabukuka. Mwina munamva za kabukuka kwa mkulu mumpingo kapena kwa wokhulupilila mnzanu. Ndiyeno, mutakalandila munayamba kuŵelenga ndi kutsatila malangizo ake. Zonsezi ndi umboni wakuti Yehova sanakuiŵaleni iyai. M’malo mwake, akukukokani pang’onopan’ono kuti mubwelele kwa iye.—Yohane 6:44.

N’zotonthoza kwambili kudziŵa kuti Yehova saiŵala atumiki ake osocela. Mlongo wina, dzina lake Donna, anafika pomvetsetsa mfundo imeneyi. Iye anati: “Ndinasiya coonadi pang’onopang’ono. Koma sindinaleke kuganizila mau a pa Salimo 139:23, 24 omwe amati: ‘Ndifufuzeni, inu Mulungu, ndi kudziŵa mtima wanga. Ndisanthuleni ndi kudziŵa malingalilo anga amene akundisoŵetsa mtendele, ndipo muone ngati mwa ine muli ciliconse cimene cikundicititsa kuyenda m’njila yoipa, ndipo munditsogolele m’njila yamuyaya.’ Ndinali kudziŵa kuti kudzikoku si kwathu iyai. Kwathu ndi m’gulu la Yehova. Ndipo ndinayamba kuzindikila kuti Yehova sananditaye, ndingofunika kubwelela kwa iye. Pano ndine wokondwa kwambili kuti ndinacita zimenezo.”

“Ndinayamba kuzindikila kuti Yehova sananditaye, ndingofunika kubwelela kwa iye”

Ife tikukupemphelelani ndi mtima wonse kuti inunso mupeze “cimwemwe cimene Yehova amapeleka.” (Nehemiya 8:10) Ndipo mukabwelela kwa Yehova, zinthu zidzakuyendelani bwino kwambili.

Mafunso ndi Mayankho Ake pa Nkhani Yobwelela kwa Yehova

KODI NDINGAYAMBILE PATI?

Mlongo wozilala aŵelenga Baibulo

Ngati munthu anali kudwala matenda aakulu ndipo wacila, zimatenga nthawi kuti ayambe kugwila nchito zonse za panyumba. Cimodzimodzi inu. Kuti mupeze mphamvu monga Mkristu, mufunika kudya cakudya cakuuzimu pang’ono tsiku lililonse. Musaganize kuti muyenela kucita zonse panthawi imodzi. Mwina mungapatule mphindi zocepa pa tsiku kuti muziŵelenga Baibulo kapena kumvetsela CD yake, kuŵelenga buku lathu lina, kapena kufufuza zinthu pa webusaiti yathu ya jw.org,na tv.jw.org. Ndiponso, musazengeleze kuyamba kusonkhana. Koposa zonse, muyenela kupempha Yehova kuti akuthandizeni. ‘Mutulileni nkhawa zanu zonse, pakuti amakudelani nkhawa.’—1 Petulo 5:7.

“Pamene ndinali wozilala, ndinali kucita manyazi ngakhale kupemphela. Tsiku lina ndinalimba mtima ndipo ndinapemphela. Kenako mkulu anandicezela. Iye anandithandiza kuona kuti Yehova akali kundikonda. Mkuluyo anandipempha kuti ndiyambe kuŵelenga Baibulo tsiku ndi tsiku. Nditacita zimenezo, ndinakhala ndi mphamvu zopita ku misonkhano. Posapita nthawi, ndinayamba kulalikila. Ndikuyamikila kwambili kuti Yehova sananditaye.”—Eeva.

NANGA ABALE NDI ALONGO MUMPINGO ADZANDIONA BWANJI?

Abale ndi alongo adzakulandilani ndi manja aŵili. Iwo sadzakuimbani mlandu kapena kukuweluzani. M’malo mwake, adzakusonyezani cikondi, ndipo adzacita zonse zotheka kuti akulimbikitseni.—Aheberi 10:24, 25.

“Ndinali ndi manyazi popita ku Nyumba ya Ufumu cifukwa sindinali kudziŵa kuti anzanga adzandilandila bwanji. Nditafika, mlongo wina wacikulile amene analipo zaka 30 zapitazo anandiuza kuti: ‘Takulandilani ndi manja aŵili.’ Mau amenewa anandikhudza mtima kwambili. Apa ndinaona kuti ndafikadi kwathu.”—Javier.

“Ndinapita ku Nyumba ya Ufumu. Nditafika, ndinakhala mpando wakumbuyo kuti aliyense asadziŵe. Komabe, ambili atandiona anakumbukila kuti ndili mwana, ndinali kusonkhana. Iwo anandilandila ndi manja aŵili, ndipo anandikumbatila. Mtendele umene ndinamva pamenepo sindinaumvepo m’mbuyomu. Ndinaona ngati ndabwelela kwathu.”—Marco.

KODI AKULU ADZANDITHANDIZA BWANJI?

Akulu adzakukomelani mtima. Adzakuyamikilani kaamba ka mtima wanu wofuna kukhalanso ndi ‘cikondi cimene munali naco poyamba.’ (Chivumbulutso 2:4) Mwacifundo, iwo adzakuthandizani kuongolela zolakwa zanu, ndipo adzacita zimenezo “ndi mzimu wofatsa.” (Agalatiya 6:1; Miyambo 28:13) Akulu angakonze kuti munthu wina ayambe kuphunzila ndi inu buku lakuti Yandikirani kwa Yehova kapena lakuti “Khalanibe m’Cikondi ca Mulungu.” Dziŵani kuti akulu adzakutonthozani ndi kukuthandizani pa zoyesayesa zanu zonse.—Yesaya 32:1, 2.

“Ndinali wozilala kwa zaka 8, ndipo nthawi yonseyo akulu sanasiye kundithandiza. Tsiku lina, mkulu wina anandionetsa zithunzi zimene anatijambula m’mbuyomo. Nditaona zithunzi zimenezo, ndinakumbukila cisangalalo ca masiku amenewo. Inde, ndinayamba kulakalaka cisangalalo cimene ndinali naco m’mbuyomo potumikila Yehova. Akulu anandithandiza kukhalanso wokangalika pa zinthu zakuuzimu.”—Victor.

“Adzakulimbitsa”

Alongo aŵili agwilitsila nchito buku la nyimbo limodzi poimba pa msonkhano wa mpingo

Buku lathu la nyimbo la ‘Imbani Mokweza ndi Mosangalala’ kwa Yehova, lili ndi nyimbo zingapo zokhudza mtima. Nyimbo zimenezi zingakutonthozeni ndi kukulimbikitsani mukayambanso kucita zinthu za kuuzimu. Mwacitsanzo, taganizilani mau a nyimbo nambala 38. Mauwo azikidwa pa lemba la 1 Petulo 5:10 ndipo mutu wake ndi wakuti “Adzakulimbitsa.”

  1. Panali cifukwa cimene Yehova,

    Anakupatsila coonadi.

    Anaona kuti unali kufuna,

    Kucita zinthu zom’kondweletsa.

    Unalonjeza kum’tumikila,

    Ndipo iye anakuthandiza.

  2. Mwana wake Yesu anamupeleka,

    Afuna zinthu zikuyendele.

    Anamupeleka Yesu mwacikondi,

    Conco Iye adzakulimbitsa.

    Cikondi cako sadzaiŵala.

    Amasamala za anthu ake.

    (KOLASI)

    Na magazi a Yesu, anakuombola.

    Adzakulimbitsa, nokupatsa mphamvu.

    Adzakutsogolela, na kukuteteza.

    Adzakulimbitsa, nokupatsa mphamvu.

Imbirani Yehova​—Nyimbo za Mau

Kuti mumvetsele nyimbo ya mau imeneyi, na zinanso za Ufumu, unikani QR khodi iyi kapena yendani pa webusaiti ya www.jw.org. Onani pa MABUKU > NYIMBO..

[DO NOT SET] This page will not contain any WEB tags or SEO information.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani