LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • lfb phunzilo 7 tsa. 24-tsa. 25 pala. 1
  • Nsanja ya Babele

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Nsanja ya Babele
  • Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • Nkhani Zofanana
  • Anthu Amanga Cinsanja
    Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
  • Cingalawa ca Nowa
    Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
lfb phunzilo 7 tsa. 24-tsa. 25 pala. 1
Yehova atasokoneza citundu cawo, anthu analeka nchito yomanga Nsanja ya Babele

PHUNZILO 7

Nsanja ya Babele

Pambuyo pa Cigumula, ana a Nowa pamodzi na akazi awo anabala ana ambili. Mabanja awo anakula, ndipo mogwilizana na zimene Yehova anawauza, iwo anapita kukakhala kumalo osiyana-siyana pa dziko lapansi.

Koma mabanja ena sanamvele Yehova. Iwo anati: ‘Tiyeni timange mzinda kuti tizikhala pano, ndipo nsanja yake ikafike kumwamba kweni-kweni. Tikacita zimenezi tidzachuka.’

Yehova sanakondwele na zimene anthuwo anali kucita. Conco, anawalepheletsa colinga cawo. Kodi udziŵa mmene anacitila zimenezi? Mwadzidzidzi anawapangitsa kuyamba kukamba vitundu vosiyana-siyana. Popeza kuti sanali kumvelana zimene anali kukamba, analeka nchito yomangayo. Mzinda umene iwo anali kumanga unachedwa Babele. Dzina limeneli litanthauza “Msokonezo.” Pamenepo, anthu anayamba kucoka kukakhala kumalo osiyana-siyana pa dziko lonse lapansi. Koma anapitiliza kucita vinthu voipa kumene anapita kukakhala. Kodi pali ena amene anapitiliza kukonda Yehova? Tidzaona m’nkhani yokonkhapo.

“Aliyense wodzikweza adzam’nyazitsa, koma wodzicepetsa adzamukweza.”—Luka 18:14

Mafunso: Kodi anthu a ku Babele anacita ciani? Nanga Yehova anawalepheletsa bwanji kucita zimene anali kufuna?

Genesis 11:1-9

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani