LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • lfb phunzilo 9 tsa. 28-tsa. 29 pala. 1
  • Mpaka Anakhala na Mwana Wake!

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Mpaka Anakhala na Mwana Wake!
  • Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • Nkhani Zofanana
  • Mulungu Anamucha Mfumukazi
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2017
  • “Ndiwe Mkazi Wokongola m’Maonekedwe Ako”
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2017
  • Mulungu Ayesa Cikhulupililo Ca Abulahamu
    Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
  • Abulahamu na Sara Anamvela Mulungu
    Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
Onaninso Zina
Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
lfb phunzilo 9 tsa. 28-tsa. 29 pala. 1
Sara ali mu hema, koma amvelako zimene angelo akuuza Abulahamu

PHUNZILO 9

Mpaka Anakhala na Mwana Wake!

Abulahamu na Sara anakhala zaka zambili m’cikwati cawo. Iwo anasiya nyumba yawo yabwino ku Uri na kukakhala mu tenti. Koma Sara sanadandaule, cifukwa anadalila Yehova.

Sara anali kufuna ngako kukhala na mwana, cakuti anauza Abulahamu kuti: ‘mukabala mwana kwa Hagara, adzakhala monga wanga.’ M’kupita kwa nthawi, Hagara anabala mwana. Dzina lake anali Isimaeli.

Sara ali na pakati

Patapita zaka zambili, pamene Abulahamu anali na zaka 99 ndipo Sara zaka 89, iwo analandila alendo atatu. Abulahamu anawapempha kuti apumuleko munsi mwa mtengo kuti adyeko cakudya. Uganiza alendowo anali ndani? Anali Angelo! Mmodzi wa iwo anauza Abulahamu kuti: ‘Caka camaŵa, nthawi ngati ino, iwe na mkazi wako mudzakhala na mwana.’ Sara anali kumvetselako ali mu hema. Iye anangoseka, na kukamba mu mtima mwake kuti: ‘Mmene nakalambila conco ine, ningabale mwana?’

Koma caka cotsatila, Sara anabala mwana wamwamuna, malinga na lonjezo la mngelo wa Yehova. Abulahamu anam’patsa dzina lakuti Isaki, lotanthauza “Kuseka.”

Pamene Isaki anali na zaka 5, Isimaeli anali kumuseka, ndipo Sara anali kuona zimenezo. Pofuna kuteteza mwana wake, Sara anapempha Abulahamu kuti acotse Hagara na Isimaeli pa nyumba. Poyamba, Abulahamu sanafune kucita zimenezo. Koma Yehova naye pofuna kuteteza Isaki, anauza Abulahamu kuti: ‘Mvela Sara. Isimaeli nidzamusamalila. Koma malonjezo anga adzakwanilitsidwa kupitila mwa Isaki.’

Sara wagwila Isaki pamene Hagara na Isimaeli acoka pa nyumba

“Mwa cikhulupililo, Sara nayenso analandila mphamvu yokhala ndi pakati, . . . cifukwa anaona kuti wolonjezayo ndi wokhulupilika.”—Aheberi 11:11

Mafunso: Kodi Sara anamvela ciani cimene angelo anali kuuza Abulahamu? Kodi Yehova anamuteteza bwanji Isaki?

Genesis 16:1-4, 15, 16; 17:25-27; 18:1-15; 21:1-14; Aheberi 11:11

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani