PHUNZILO 54
Yehova Anamulezela Mtima Yona
Mu mzinda wa Asuri wochedwa Nineve, munali anthu oipa kwambili. Yehova anauza mneneli Yona kupita ku Nineve, kukacenjeza anthu kuti aleke kucita zoipa. Koma iye anathaŵa n’kupita kwina. Anakwela boti yopita ku Tarisi.
Pamene boti inali pa nyanja, kunabwela cimphepo camphamvu, ndipo oyendetsa boti anacita mantha kwambili. Anapemphela kwa milungu yawo, ndipo anafunsa kuti: ‘N’cifukwa ciani izi zikucitika?’ Pothela pake, Yona anawauza kuti: ‘Ndine nacititsa izi. Nithaŵa nchito imene Yehova ananipatsa. Niponyeni pa nyanja, ndipo cimphepo cidzaleka.’ Oyendetsa botiwo sanafune kum’ponya pa nyanja, koma Yona anawaumiliza. Pamene anam’ponya, cimphepo cinaleka.
Yona anaganiza kuti adzafa. Pamene anali kumilila-milila pa nyanjapo, anali kupemphela kwa Yehova. Ndiyeno Yehova anatumiza cinsomba cacikulu. Cinam’meza Yona, koma sicinamuphe. Ali m’mimba mwa cinsombaco, Yona anapemphela kuti: ‘Nilonjeza kuti nidzakumvelani nthawi zonse.’ Yehova anateteza Yona m’mimba mwa cinsomba kwa masiku atatu. Kenako, cinamulavulila kumtunda.
Popeza kuti Yehova anapulumutsa Yona, kodi anafunikilabe kupita ku Nineve? Inde. Yehova anamuuzanso kuti apitebe ku Nineve. Apa lomba Yona anavomela. Anapitadi kumeneko na kuuza anthu oipawo kuti: ‘M’masiku 40, Nineve adzawonongedwa.’ Koma panacitika zosayembekezeleka. Anthu a ku Nineve aja anamvela na kuleka kucita zoipa. Mfumu ya ku Nineve inauza anthu ake kuti: ‘Fuulani kwa Mulungu, ndipo mulape. Mwina sadzatiwononga.’ Yehova ataona kuti anthuwo alapa, sanawonge mzinda wa Nineve.
Koma Yona anakwiya kwambili poona kuti mzindawo sunawonongedwe. Ganizila cabe: Yehova anamulezela mtima Yona na kumumvelela cifundo, koma iye sanafune kumvelela cifundo anthu a ku Nineve. M’malo mwake, anapita kukakhala kunja kwa mzinda, pa mthunzi wa comela ca mtundu wa mphonda, apo ali khwi na msunamo. Kenako comelaco cinauma, ndipo Yona anakwiya. Ndiye Yehova anamuuza kuti: ‘Iwe umvelela cifundo comela ici kuposa anthu a mu Nineve. Ine naŵacitila cifundo, ndipo apulumuka.’ Kodi mfundo yake inali iti? Anthu a ku Nineve anali ofunika kwambili kuposa comela ciliconse.
“Yehova . . . akuleza nanu mtima, pakuti safuna kuti wina aliyense adzawonongedwe, koma amafuna kuti anthu onse alape.”—2 Petulo 3:9