Tengelani Citsanzo kwa Aneneli—Yona
1. Kodi Yona anali ndi makhalidwe abwino ati?
1 Kodi mumaganiza ciani mukamva dzina la mneneli Yona? Ena amaganiza kuti anali munthu wamantha kapena wouma mtima. Komabe, iye anaonetsa kuti anali wodzicepetsa, wolimba mtima, ndi wodzimana. Kodi tingatengele bwanji citsanzo ca Yona coonetsa makhalidwe abwino?—Yak. 5:10.
2. Kodi tingatsanzile bwanji citsanzo ca Yona ca kudzicepetsa?
2 Kudzicepetsa: Poyamba Yona anathaŵa kupita kwina, m’malo mopita kudela limene anauzidwa. Izi n’zosadabwitsa cifukwa Asiriya anali kudziŵika kuti ndi anthu aciwawa kwambili, ndipo mzinda wa Nineve unali kudziŵika kuti “mzinda wokhetsa magazi.” (Nah. 3:1-3) Ngakhale n’conco, Yehova analanga Yona, amene pambuyo pake anadzicepetsa ndi kulandila udindo umene anapatsidwanso. (Miy. 24:32; Yona 3:1-3) Ngakhale kuti poyamba anathaŵa, iye pambuyo pake anacita cifunilo ca Yehova. (Mat. 21:28-31) Kodi nafenso ndife otsimikiza mtima kulalikila uthenga wabwino, mosasamala kanthu kuti tapatsidwa cilango kapena tili ndi gawo lovuta?
3. Kodi ndi panthawi iti pamene muyenela kukhala wolimba mtima komanso wodzimana muutumiki wanu?
3 Kulimba Mtima ndi Kudzimana: Pamene Yona anazindikila kuti cosankha cake colakwa caika miyoyo ya anthu oyendetsa combo pangozi, iye anali wofunitsitsa kupeleka moyo wake. (Yona 1:3, 4, 12) Ndiyeno atapita kukalalikila ku Nineve, anayenda pakati pa mzinda, mwina anali kufuna malo oyenelela kuti akalengeze ciweluzo ca Yehova. Zimene Yona anacita zinaonetsa kuti sanali munthu wamantha, koma kuti anali mneneli wa Mulungu wolimba mtima. (Yona 3:3, 4) Nanga bwanji ponena za ife lelo? Kuti tikwanitse kulalikila molimba mtima pamene titsutsidwa, timafunikila kulimba mtima kumene Mulungu amapeleka. (Mac. 4:29, 31) Ndithudi, kudzimana n’kofunika kuti tithele nthawi yathu ndi cuma cathu mu ulaliki.—Mac. 20:24.
4. N’cifukwa ciani tiyenela kukhala ndi nthawi yosinkha-sinkha pa zitsanzo zabwino za aneneli a Yehova?
4 Nthawi iliyonse imene muŵelenga nkhani yokhudza mmodzi wa aneneli a Yehova, mudzapindula ngati muona kuti ndinu amene muli mumkhalidwe umenewo. Conco dzifunseni kuti: ‘Kodi ndikanacita bwanji? Ndingatsanzile bwanji makhalidwe ake abwino paumoyo wanga?’ (Aheb. 6:11, 12) Nkhani za mtsogolo zimene zidzatuluka mu Utumiki wathu wa Ufumu zidzafotokoza maphunzilo ofunika amene tingatsanzile kwa aneneli ena okhulupilika a Yehova.