CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
Zimene Tiphunzilamo m’Buku la Yona
Yehova anasunga nkhani za amuna na akazi okhulupilika m’Mau ake, n’colinga cakuti titengepo maphunzilo ofunikila. (Aroma 15:4) Kodi munaphunzila ciani m’buku la Yona? Tambani vidiyo yakuti Kulambila kwa Pabanja: Yona Anaphunizilapo Kanthu pa Cifundo ca Yehova. Ndiyeno yankhani mafunso aya:
Ni mavuto ati amene ofalitsa atatu mu vidiyoyi anakumana nawo?
Kodi buku la Yona lingatilimbikitse bwanji tikapatsidwa uphungu kapena kutaikidwa mwayi wa utumiki?— (1 Sam. 16:7; Yona 3:1, 2.)
Kodi nkhani ya Yona ingatithandize bwanji kukhala na maganizo abwino a gawo lathu?— (Yona 4:11; Mat. 5:7.)
Ngati tidwala matenda osathelapo, kodi zimene zinacitikila Yona zingatitonthoze bwanji?— (Yona 2:1, 2, 7, 9.)
Mwaphunzila ciani mu vidiyoyi za kufunika koŵelenga Baibo na kusinkha-sinkha?