CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | OBADIYA 1–YONA 4
Tizitengelapo Phunzilo pa Zolakwa Zathu
Nkhani ya Yona imaonetsa kuti Yehova saleka kutithandiza tikalakwitsa. Ndiponso, amayembekezela kuti titengelepo phunzilo pa zolakwa zathu, na kupanga masinthidwe ofunikila.
Yona 1:3
Kodi Yona analakwitsa ciani atapatsidwa nchito na Yehova?
Yona 2:1-10
Kodi Yona anapempha ciani kwa Yehova? Nanga Yehova anamuyankha bwanji?
Yona 3:1-3
Kodi Yona anaonetsa bwanji kuti anatengelapo phunzilo pa zolakwa zake?