LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • lfb phunzilo 57 tsa. 138-tsa. 139 pala. 1
  • Yehova Atumiza Yeremiya Kuti Akalalikile

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Yehova Atumiza Yeremiya Kuti Akalalikile
  • Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • Nkhani Zofanana
  • Yeremiya Sanaleke Kulankhula za Yehova
    Phunzitsani Ana Anu
  • Mwamuna Wosaopa Munthu
    Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
  • Khalani Wolimba Mtima Monga Yeremiya
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano —2017
Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
lfb phunzilo 57 tsa. 138-tsa. 139 pala. 1
Yeremiya aphwanya mtsuko wamadzi pamaso pa akulu-akulu

PHUNZILO 57

Yehova Atumiza Yeremiya Kuti Akalalikile

Yehova anasankha Yeremiya kuti akhale mneneli kwa Ayuda. Anamuuza kuti akalalikile kwa anthu, na kuwacenjeza kuti aleke kucita zinthu zoipa. Koma Yeremiya anayankha kuti: ‘Yehova, ine ndine mwana. Sinidziŵa mokambila ndi anthu.’ Yehova anamuuza kuti: ‘Usacite mantha. Ine nidzakuuza zokakamba. N’dzakuthandiza.’

Yehova anauza Yeremiya kuti asonkhanitse akulu-akulu a mu mzinda, ndiyeno aphwanye mtsuko wamadzi pamaso pawo, na kuwauza kuti: ‘Umu ni mmenenso Yerusalemu adzam’phwanyila.’ Yeremiya atacita zimene Yehova anamuuza, akulu-akuluwo anakwiya kwambili. Ndipo wansembe wina, Pasuri, anamenya Yeremiya na kum’manga m’matangadza. Usiku wonse Yeremiya sanakwanitse kuyenda. Anam’masula m’mawa mwake. Cifukwa ca izi, Yeremiya anati: ‘Siningazikwanitse izi. N’dzaleka kulalikila.’ Koma kodi analeka? Iyai. Ataganizilapo anakamba kuti: ‘Uthenga wa Yehova uli monga moto mu mtima mwanga. Sinidzaleka kulalikila.’ Inde, Yeremiya anapitiliza kucenjeza anthu.

Zaka zinapitapo, ndipo Ayuda anakhala na mfumu yatsopano. Ansembe komanso aneneli onama anali kuipidwa nawo uthenga wa Yeremiya. Iwo anauza atsogoleli kuti: ‘Munthu uyu afunika kufa.’ Koma Yeremiya anati: ‘Ngati munganiphe, ndiye kuti mwapha munthu wosalakwa. Mawu amene nilankhula si anga, ni ocokela kwa Yehova.’ Atsogoleli atamva zimenezi anati: ‘Munthu uyu safunika kuphedwa.’

Koma pamene Yeremiya anapitiliza kulalikila, atsogoleli a anthu anakwiya kwambili. Anapempha mfumu kuti imuphe Yeremiya. Mfumu inawauza kuti angacite naye ciliconse cimene angafune. Iwo anatenga Yeremiya na kum’ponya m’citsime cakuya komanso ca matika kuti afe. Ndipo Yeremiya anayamba kumila m’matikamo.

Ebedi-meleki ndi anthu amene ali nawo acotsa Yeremiya m’citsime

Koma nduna ya pa nyumba ya mfumu dzina lake Ebedi-meleki, inauza mfumu kuti: ‘Akulu-akulu aponya Yeremiya m’citsime! Tikamusiya mmenemo adzafa.’ Mfumuyo inauza Ebedi-meleki kutenga amuna 30 kuti akacotse Yeremiya m’citsimemo. Kodi na ise sitiyenela kukhala monga Yeremiya, amene sanalole ciliconse kum’letsa kulalikila?

“Anthu onse adzadana nanu cifukwa ca dzina langa, koma yekhayo amene adzapilile mpaka pa mapeto ndi amene adzapulumuke.”—Mateyu 10:22

Mafunso: N’cifukwa ciani Yeremiya anamvela Yehova olo kuti anali wamng’ono? N’ndani anafuna kuletsa Yeremiya kulalikila?

Yeremiya 1:1-19; 19:1-11; 20:1-13; 25:8-11; 26:7-16; 38:1-13

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani