CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | YEREMIYA 25-28
Khalani Wolimba Mtima Monga Yeremiya
Yeremiya anacenjeza kuti Yerusalemu adzasakazidwa mofanana ndi mzinda wa Silo
26:6
Pa nthawi ina likasa la pangano, loimila Yehova, linali kusungidwila ku Silo
Yehova analola kuti Afilisiti alande likasalo, ndipo siinabwelelenso ku Silo
Ansembe, aneneli, ndi anthu onse anaopseza kuti adzamupha Yeremiya
26:8, 9, 12, 13
Anthu anam’gwila Yeremiya cifukwa colosela zakuti kacisi adzawonongedwa
Yeremiya sanaope ndi kuthaŵa
Yehova anam’teteza Yeremiya
26:16, 24
Yeremiya anakhalabe wolimba mtima, ndipo Yehova sanamusiye
Mulungu anacititsa Ahikamu wolimba mtima kuteteza Yeremiya
Yeremiya sanaleke kulengeza uthenga umene anthu anali kukwiya nawo cifukwa Yehova anali kumucilikiza na kumulimbikitsa kwa zaka 40