LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • lfb phunzilo 70 tsa. 166-tsa. 167 pala. 2
  • Angelo Alengeza za Kubadwa kwa Yesu

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Angelo Alengeza za Kubadwa kwa Yesu
  • Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • Nkhani Zofanana
  • Yesu Abadwila Mu Khola
    Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
  • Yesu Kristu Kodi Tifunika Kumukumbukila Monga Khanda Kapena Mfumu?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2013
  • Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2023
Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
lfb phunzilo 70 tsa. 166-tsa. 167 pala. 2
Angelo alengeza kwa abusa za kubadwa kwa Yesu

PHUNZILO 70

Angelo Alengeza za Kubadwa kwa Yesu

Kaisara Augusto, Wolamulila mu Ufumu wa Roma, analamula Ayuda onse kuti abwelele ku matauni akwawo kuti akadzilembetse m’kaundula. Conco, Yosefe na Mariya anapita ku Betelehemu, kwawo kwa Yosefe. Ndipo masiku anayandikila akuti Mariya abale mwana.

Atafika ku Betelehemu, anapeza kuti nyumba zonse n’zodzala. Conco anagona m’khola la ziŵeto. Mmenemo ndiye mmene Mariya anabalila mwana wake wamwamuna, dzina lake Yesu. Anamuika m’nsalu zofeŵa bwino, na kum’goneka bwino-bwino m’codyelamo ziŵeto.

Pafupi na Betelehemu, panali aciŵeta amene anali kuyang’anila ziŵeto zawo usiku. Mwadzidzidzi, mngelo anaima pafupi nawo, ndipo ulemelelo wa Yehova unawawalila. Aciŵetawo anacita mantha kwambili, koma mngelo anati: ‘Musaope. Ndili na uthenga wokondweletsa. Mesiya wabadwa lelo ku Betelehemu.’ Pa nthawi imeneyo, angelo ambili anaonekela m’mwamba, ndipo anali kufuula kuti: ‘Ulemelelo kwa Mulungu wakumwamba-mwamba, na mtendele pa dziko lapansi.’ Kenako angelowo anasoŵa. Kodi abusawo anacita bwanji?

Iwo anayamba kuuzana kuti: ‘Tiyeni tipite ku Betelehemu.’ Anapita mwamsanga-msanga, ndipo anapeza kuti Yosefe na Mariya ali m’khola, na mwana wawo wakhanda.

Aliyense amene anamvela zimene mngelo anauza abusa aja anadabwa. Mariya anaganizilapo kwambili pa mawu amene mngelo anakamba, ndipo sanawaiŵale. Abusa aja anabwelela kukayang’anila ziŵeto zawo, ndipo anayamikila Yehova pa zonse zimene anaona na kumva.

“Ine ndinacokela kwa Mulungu ndipo ndili pano. Sindinabwele mwakufuna kwanga ayi, koma Iyeyo anandituma.”—Yohane 8:42

Mafunso: Kodi angelo analengeza bwanji za kubadwa kwa Yesu? Nanga abusawo anapeza ndani ku Betelehemu?

Luka 2:1-20; Yesaya 9:6

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani