LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • my nkhani 85
  • Yesu Abadwila Mu Khola

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Yesu Abadwila Mu Khola
  • Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
  • Nkhani Zofanana
  • Angelo Alengeza za Kubadwa kwa Yesu
    Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • Yesu Kristu Kodi Tifunika Kumukumbukila Monga Khanda Kapena Mfumu?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2013
  • Nthawi Zonse Yesu Anali Womvela
    Phunzitsani Ana Anu
  • Mngelo Acezela Mariya
    Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
my nkhani 85

Nkhani 85

Yesu Abadwila Mu Khola

KODI wakadziŵa kamwana aka? Inde, ni Yesu. Wabadwa posacedwa mu khola. Khola ni malo amene amasungilamo zinyama. Mariya agoneka Yesu modyelamo ziweto, malo oikamo cakudya ca abulu ndi zinyama zina. Nanga n’cifukwa ciani Mariya ndi Yosefe ali m’malo amenewa pamodzi ndi zinyama? Malo amenewa si oyenela kubadwilamo, si conco?

Inde. Koma cimene cacititsa kuti apezeke m’malo amenewa ni ici: Wolamulila wa Roma, Kaisara Augusto, anaika lamulo lakuti aliyense abwelele kumzinda umene anabadwilako kuti akalembetse dzina lake mu kaundula. Yosefe anabadwila mu mzinda umenewu wa Betelehemu. Koma pamene iye ndi mkazi wake Mariya anafika kumeneko, anapeza kuti zipinda zonse n’zodzala ndi anthu. Conco anapeza malo mu khola la ziŵeto. Koma patsiku limeneli Mariya anabala Yesu! Kamwanako kanabadwa bwino-bwino, monga mmene uonela pacithunzi-thunzi apa.

Kodi waaona abusa amene abwela kuti aone Yesu? Iwo anali kusanga usiku kuyang’anila nkhosa zao. Koma kuwala kwakukulu kunaunika pamalo ponse pamene anali. Anacititsa kuwala kumeneko anali mngelo! Abusa anacita mantha kwambili. Koma mngelo anati: ‘Musaope! Ine ndabwela kudzalengeza kwa inu uthenga wabwino. Cifukwa lelo, mu Betelehemu Kristu Ambuye wakubadwilani. Iye adzapulumutsa anthu! Mudzamupeza ali mu nsalu, ndipo amugoneka modyelamo ziweto.’ Mwadzidzidzi, angelo ambili anabwela ndipo anayamba kutamanda Mulungu. Conco nthawi imeneyo, abusa amenewa anafulumila kuti akafune Yesu, ndipo tsopano amupeza.

Kodi udziŵa cifukwa cake Yesu ni munthu wapadela kwambili? Nanga udziŵa kuti iye ndani kweni-kweni? Kumbukila kuti, mu nkhani yoyamba mu buku lino, tinakambitsilana za Mwana wa Mulungu woyamba. Mwana ameneyu anagwila nchito pamodzi ndi Yehova popanga kumwamba ndi dziko lapansi, ndiponso zinthu zonse. Conco, uyu ndiye Yesu!

Inde, Yehova anatenga moyo wa Mwana wake kucokela kumwamba ndi kuuika m’mimba mwa Mariya. Kucokela panthawi imeneyo, kamwana kanayamba kukula m’mimba mwa Mariya monga mmene ana onse amakulila m’mimba mwa amai ao. Koma mwana uyu anali Mwana wa Mulungu. Potsilizila pake, Yesu anabadwila mu khola ku Betelehemu. Kodi waona cimene angelo anakondwelela kwambili cakuti anayamba kuuza anthu kuti Yesu wabadwa?

Luka 2:1-20.

Mafunso Ophunzilila

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani