PHUNZILO 80
Yesu Asankha Atumwi 12
Yesu atagwila nchito yolalikila pafupi-fupi caka cimodzi na hafu, anafunika kucita cinthu cofunika kwambili. Anafunikila kusankha amene angawagwilitsile nchito kwambili, na kuwaphunzitsa za kuyang’anila mpingo. Akalibe kusankha anthu amenewo, anafunikila thandizo la Yehova. Conco anapita kwa yekha ku phili, kumene anakapemphela usiku wonse. M’mawa mwake, Yesu anaitana ena mwa ophunzila ake, na kusankhapo atumwi 12. Ndani amene ukumbukilako maina awo? Panali Petulo, Andireya,Yakobo, Yohane, Filipo, Batolomeyo, Tomasi, Mateyu,Yakobo mwana wa Alifeyo, Tadeyo, Simoni, na Yudasi Isikariyoti.
Andireya, Petulo, Filipo, Yakobo
Atumwi 12 amenewa anali kuyenda na Yesu. Atawaphunzita nchito yolalikila, anawatumiza kukalalikila paokha. Yehova anapatsa atumwiwo mphamvu zocotsa ziwanda, na kucilitsa odwala.
Yohane, Mateyu, Batolomeyo, Tomasi
Yesu anachula atumwi 12 amenewo kuti mabwenzi ake, ndipo anali kuŵadalila. Afarisi anali kuona atumwi kukhala anthu wamba osaphunzila. Koma Yesu anawaphunzitsa bwino nchito yawo. Anakhala pamodzi na Yesu pa zocitika zikulu-zikulu mu umoyo wake, monga pa imfa yake, komanso ataukitsidwa. Unyinji wa atumwi 12 amenewo anacokela ku Galileya, kumenenso Yesu anacokela. Ndipo ena mwa iwo anali okwatila.
Yakobo mwana wa Alifeyo, Yudasi Isikariyoti, Tadeyo, Simoni
Atumwi nawonso anali opanda ungwilo, ndipo nthawi zina anali kulakwitsa. Nthawi zina anali kuthamangila kukamba akalibe kuganiza bwino, cakuti anali kulakwitsa zinthu. Nthawi zinanso sanali kuleza mtima. Mpaka nthawi ina anakangana pa nkhani yakuti wamkulu ndani pakati pawo. Komabe onse anali anthu abwino, komanso okonda Yehova. Ndiwo anakhala monga maziko a mpingo woyambilila wacikhristu, Yesu atabwelela kumwamba.
“Ndakuchani mabwenzi, cifukwa zonse zimene ndamva kwa Atate wanga ndakudziwitsani.”—Yohane 15:15