LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • lfb phunzilo 87 tsa. 204-tsa. 205 pala. 3
  • Mgonelo wa Ambuye

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Mgonelo wa Ambuye
  • Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • Nkhani Zofanana
  • M’cipinda Capamwamba
    Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
  • ‘Citani Zimenezi Pondikumbukila’
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2013
  • Mgonelo wa Ambuye—Mwambo Umene Umalemekeza Mulungu
    Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
  • Yesu Adyetsa Khamu la Anthu
    Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
Onaninso Zina
Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
lfb phunzilo 87 tsa. 204-tsa. 205 pala. 3
Yesu ayambitsa Mgonelo wa Ambuye pamodzi na atumwi 11 okhulupilika

PHUNZILO 87

Mgonelo wa Ambuye

Caka ciliconse, Ayuda anali kucita cikondwelelo ca Pasika pa tsiku la 14 la mwezi wa Nisani. Cinali kuŵakumbutsa mmene Yehova anawapulumutsila ku ukapolo ku Iguputo, na kuŵaloŵetsa m’Dziko Lolonjezedwa. Mu 33 C.E., Yesu na atumwi ake anacita cikondwelelo ca Pasika m’cipinda cinali pamwamba ku Yerusalemu. Cakumapeto kwa cakudyaco, Yesu anati: ‘Mmodzi wa imwe adzanipeleka.’ Atumwiwo anadabwa kwambili, ndipo anafunsa Yesu kuti: ‘Ni ndani ameneyo?’ Poyankha Yesu anati: ‘Ni amene nim’patse mkate uwu.’ Kenako anatenga mkate na kupatsa Yudasi Isikariyoti. Basi pamenepo Yudasi ananyamuka kucoka m’cipindaco.

Ndiyeno Yesu anapemphela. Kenako, anatenga mkate na kuubenthula-benthula. Atatelo anaugaŵila kwa atumwi otsalawo. Anati: ‘Dyani mkate uwu. Uimila thupi langa limene nidzalipeleka cifukwa ca inu.’ Atapemphelanso, anatenga vinyo na kuupeleka kwa atumwi ake. Iye anati: ‘Mwani vinyo uwu. Uimila magazi anga amene nidzawapeleka kuti macimo a anthu akhululukidwe. Nikulonjezani kuti mudzakhala mafumu pamodzi na ine kumwamba. Muzicita zimenezi caka ciliconse ponikumbukila.’ Mpaka lelo, otsatila a Yesu amasonkhana caka ciliconse kucita mwambo umenewo, pa Nisani 14 m’madzulo. Msonkhano umenewu umachedwa Mgonelo wa Ambuye.

Atatsiliza kudya, atumwiwo anayamba kukangana zakuti wamkulu ndani pakati pawo. Koma Yesu anaŵauza kuti: ‘Wamkulu pakati panu ni amene amadziona wamng’ono, wapansi.’

Yesu anapitiliza kuti: ‘Imwe ndimwe anzanga. Nimakuuzani zonse zimene Atate wanga amafuna kuti nikuuzeni. Posacedwa nidzapita kumwamba kwa Atate wanga. Koma imwe mudzayamba mwatsalila. Conco kuti anthu akudziŵeni kuti ndimwe ophunzila anga, muzikondana wina na mnzake, mmene ine nakukondelani.’

Pothela pake, Yesu anapemphela, kupempha Yehova kuti ateteze atumwi onse. Anapempha kuti awathandize kucita zinthu mogwilizana, komanso mwamtendele. Anapemphelanso kuti dzina la Yehova liyeletsedwe. Ndiyeno Yesu ndi atumwi ake anaimba nyimbo zotamanda Yehova. Atatsiliza anacoka panja. Apa lomba, nthawi inayandikila yakuti Yesu amugwile.

“Musaope, kagulu ka nkhosa inu, cifukwa Atate wanu wavomeleza kukupatsani Ufumu.”—Luka 12:32

Mafunso: Kodi Yesu anawalonjeza ciani atumwi ake? Kodi Yesu anaphunzitsa atumwi ake mfundo ziti zofunika pa mgonelo wake wothela?

Mateyu 26:20-30; Luka 22:14-26; Yohane 13:1, 2, 26, 30, 34, 35; 15:12-19; 17:3-26

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani