LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • lfb phunzilo 93 tsa. 216-tsa. 217 pala. 5
  • Yesu Abwelela Kumwamba

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Yesu Abwelela Kumwamba
  • Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • Nkhani Zofanana
  • Pa Phili La Maolivi
    Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
  • Yesu Analalikila Uthenga wa Ufumu
    Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • Ophunzila a Yesu Alandila Mzimu Woyela
    Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
lfb phunzilo 93 tsa. 216-tsa. 217 pala. 5
Yesu akwela kumwamba pamene atumwi ake akuyang’ana

PHUNZILO 93

Yesu Abwelela Kumwamba

Yesu atakumana na ophunzila ake ku Galileya, anawapatsa lamulo lofunika kwambili lakuti: ‘Pitani, kapangeni ophunzila m’maiko onse. Mukawaphunzitse zimene ine n’nakuphunzitsani, ndipo mukaŵabatize.’ Ndiyeno anawalonjeza kuti: ‘Kumbukilani kuti n’dzakhala na imwe nthawi zonse.’

Yesu anakhala masiku 40 pambuyo poukitsidwa. Pa nthawiyi anaonekela kwa ophunzila ake ambili ku Galileya na ku Yerusalemu. Ndipo anawaphunzitsa zinthu zambili zofunika, komanso anacita zozizwitsa zoculuka. Kenako, Yesu anakumana na atumwi ake komaliza pa Phili la Maolivi. Ali ku Yerusalemu, Yesu anauza atumwi ake kuti: ‘Musacoke mu Yerusalemu. Yembekezelanibe zimene Atate analonjeza.’

Atumwi ake sanamvetsetse zimene Yesu anatanthauza. Conco anam’funsa kuti: ‘Kodi tsopano mudzakhala Mfumu ya Isiraeli?’ Yesu anayankha kuti: ‘Iyai, nthawi ya Yehova yakuti nikhale Mfumu sinakwane. Posacedwa mudzalandila mphamvu ya mzimu woyela, ndipo mudzakhala mboni zanga. Pitani mukalalikile ku Yerusalemu, ku Yudeya, ku Samariya, mpaka ku malekezelo a dziko lapansi.’

Pamenepo Yesu ananyamuka n’kuyamba kukwela kumwamba, mpaka anaphimbika m’mitambo. Ophunzila ake anali kungoyang’ana kumwamba, koma sanaonekenso.

Ophunzila ake anaseluka m’Phili la Maolivi n’kupita ku Yerusalemu. Anali kukumana kaŵili-kaŵili m’cipinda capamwamba na kupemphela. Anali kuyembekezela kuti Yesu aŵapatse malangizo owonjezeleka.

“Uthenga wabwino uwu wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse, kenako mapeto adzafika”—Mateyu 24:14

Mafunso: Kodi Yesu anapatsa ophunzila ake lamulo la kucita ciani? Nanga n’ciani cinacitika pa Phili la Maolivi?

Mateyu 28:16-20; Luka 24:49-53; Yohane 20:30, 31; Machitidwe 1:2-14; 1 Akorinto 15:3-6

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani