Mawu Oyamba a Cigawo 14
Akhristu oyambilila analalikila uthenga wabwino wa Ufumu mpaka ku madela akutali kwambili pa dziko. Yesu anaŵauza kumene anafunika kukalalikila. Ndipo mozizwitsa anathandiza ophunzila ake kuphunzitsa anthu mu vitundu vawo. Yehova anawalimbitsa mtima kuti apilile pokumana na mazunzo oopsa.
Yesu anapatsa mtumwi Yohane masomphenya oona ulemelelo wa Yehova. M’masomphenya ena, Yohane anaona Ufumu wa kumwamba ukugonjetsa Satana na kuthetsa ulamulilo wake kwamuyaya. Yohane anaona Yesu akulamulila monga Mfumu pamodzi ndi anthu 144,000. Yohane anaona dziko lonse likusintha kukhala paradaiso, mmene aliyense anali kulambila Yehova mwamtendele, komanso mogwilizana.