LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • wp20 na. 1 masa. 12-13
  • Coonadi Ponena za Ufumu wa Mulungu

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Coonadi Ponena za Ufumu wa Mulungu
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2020
  • Nkhani Zofanana
  • Kodi Ufumu Wa Mulungu N’ciani?
    Zimene Baibulo Ingatiphunzitse
  • Kodi Ufumu wa Mulungu N’ciani?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2020
  • Kodi Ufumu wa Mulungu N’ciani?
    Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
  • Kodi Baibulo Imakamba Ciani?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2016
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2020
wp20 na. 1 masa. 12-13
Kuyang’ana dziko lapansi kucokela kuthambo, ndipo ni lounikilidwa bwino na kuwala kwa dzuŵa

Coonadi Ponena za Ufumu wa Mulungu

Yesu anaphunzitsa otsatila ake kupemphela kuti: “Atate wathu wakumwamba, dzina lanu liyeletsedwe. Ufumu wanu ubwele. Cifunilo canu cicitike, monga kumwamba, cimodzimodzinso pansi pano.” (Mateyu 6:9, 10) Kodi Ufumu wa Mulungu n’ciani? Kodi palipano ucita ciani? Nanga n’cifukwa ciani tifunika kupemphela kuti ubwele?

Yesu Ndiye Mfumu ya Ufumu wa Mulungu.

Luka 1:31-33: “Udzam’patse dzina lakuti Yesu. Ameneyu adzakhala wamkulu ndipo adzachedwa Mwana wa Wam’mwambamwamba. Yehova Mulungu adzam’patsa mpando wacifumu wa Davide atate wake. Iye adzalamulila monga Mfumu panyumba ya Yakobo kwamuyaya, moti Ufumu wake sudzatha konse.”

Ufumu wa Mulungu ndiye inali nkhani yaikulu ya ulaliki wa Yesu.

Mateyu 9:35: “Yesu anayamba ulendo woyendela mizinda ndi midzi yonse. Anali kuphunzitsa m’masunagoge awo, kulalikila uthenga wabwino wa ufumu ndi kucilitsa matenda amtundu uliwonse ndi zofooka zilizonse.”

Yesu anapatsa ophunzila ake cizindikilo coŵathandiza kudziŵa kuti Ufumu wa Mulungu watsala pang’ono kubwela.

Mateyu 24:7: “Mtundu udzaukilana ndi mtundu wina, ndipo ufumu udzaukilana ndi ufumu wina. Kudzakhala njala ndi zivomezi m’malo osiyanasiyana.”

Ophunzila a Yesu palipano akulalikila za Ufumu wa Mulungu pa dziko lonse lapansi.

Mateyu 24:14: “Uthenga wabwino uwu wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse, kenako mapeto adzafika.”

Zoona Zake Ponena za Ufumu wa Mulungu

Kumene kuli Ufumuwo. Ufumu wa Mulungu ni boma leni-leni limene linakhazikitsidwa na Mulungu kumwamba.—DANIELI 2:44; MATEYU 4:17.

Colinga. Ufumu wa Mulungu udzasandutsa dziko lapansi kukhala paradaiso, malo amene anthu adzakhala mwa mtendele komanso mogwilizana, ndipo sadzadwala kapena kufa. —SALIMO 37:11, 29.

Olamulila. Mulungu anasankha Yesu kukhala Mfumu kumwamba, ndipo adzalamulila pamodzi ndi a 144,000 amene anagulidwa pa dziko lapansi. —LUKA 1: 30-33; 12:32; CHIVUMBULUTSO 14:1, 3.

Nzika. Nzika za Ufumuwo zidzakhala pa dziko lapansi, ndipo zidzagonjela na mtima wonse ku ulamulilo wa Yesu, komanso zidzamvela malamulo a Ufumuwo.—MATEYU 7:21.

Cifukwa Cake Yesu Ndiye Woyenela Kulamulila Anthu

Ali pa dziko lapansi, Yesu anaonetsa kuti adzakhala wolamulila wabwino komanso wacikondi, cifukwa

  • Anamvela cifundo anthu osauka.—LUKA 14:13, 14.

  • Anali kudana na zacinyengo komanso kupanda cilungamo.—MATEYU 21:12, 13.

  • Analamulila mphamvu za cilengedwe.—MALIKO 4:39.

  • Anadyetsa anthu ambili-mbili.—MATEYU 14:19-21.

  • Anamvelela cifundo anthu odwala na kuwacilitsa. —MATEYU 8:16.

  • Anaukitsa akufa.—YOHANE 11:43, 44.

Mmene Ufumu wa Mulungu Ungakupindulitsileni Palipano

Mungakhale na umoyo wacimwemwe palipano, ngati mungakhale nzika ya Ufumu wa Mulungu. Mwacitsanzo, nzika za Ufumu wa Mulungu

  • ‘Zimayesetsa kukhala pa mtendele ndi anthu onse.’—AHEBERI 12:14.

  • Zimasangalala na mtendele komanso mgwilizano wa m’banja, cifukwa okwatilana amakondana na kulemekezana.—AEFESO 5:22, 23, 33.

  • Zimakhala na umoyo wacimwemwe, komanso wokhutila cifukwa ‘amazindikila zosoŵa zawo zauzimu.’—MATEYU 5:3.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani