Mawu Oyamba a Cigawo 3
Pambuyo pa Cigumula, Baibo imangochula anthu ocepa amene anatumikila Yehova. Mmodzi wa iwo ni Abulahamu, amene anadziŵika monga bwenzi la Yehova. Koma n’cifukwa ciani anachedwa bwenzi la Yehova? Ngati ndimwe kholo, thandizani mwana wanu kudziŵa kuti Yehova amam’konda, na kuti amafuna kum’thandiza. Monga mmene anacitila Abulahamu, komanso amuna ena okhulupilika, monga Loti na Yakobo, na ise tingapemphe thandizo kwa Yehova momasuka. Tingakhale na cidalilo cakuti Yehova adzacita zonse zimene walonjeza.