LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w14 2/1 masa. 23-27
  • Yehova Ndi Bwenzi Lathu Lapamtima

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Yehova Ndi Bwenzi Lathu Lapamtima
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • “BWENZI LANGA ABULAHAMU”
  • “YEHOVA NDI MTENDELE”
  • NDANI ANGAKHALE ‘MLENDO M’CIHEMA’ CA YEHOVA?
  • THANDIZANI ENA KUKHALA MABWENZI A YEHOVA
  • KUGWILA NCHITO PAMODZI NDI BWENZI LATHU LAPAMTIMA
  • MABWENZI AMAKAMBILANA
  • Inu Akulu—Tengelani Citsanzo ca Gidiyoni
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2023
  • Mukhoza Kukhala Bwenzi la Yehova
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
  • Gidiyoni Ndi Asilikali Ake 300
    Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
  • Gidiyoni Agonjetsa Amidiyani
    Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
w14 2/1 masa. 23-27

Yehova Ndi Bwenzi Lathu Lapamtima

“[Abulahamu] anachedwa ‘bwenzi la Yehova.’”—YAK. 2:23.

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

  • N’ciani cingatithandize kukhala paubwenzi ndi Yehova?

  • Malinga ndi Salimo 15:3, 5, kodi Mulungu amafuna kuti tizicita ciani kuti tikhale naye paubwenzi?

  • N’ciani cingatithandize kuti tizilankhula momasuka ndi Bwenzi lathu lapamtima?

1. Pokhala anthu olengedwa m’cifanizilo ca Mulungu, kodi timakwanitsa kucita ciani?

“MWANA mbuu make mbuu.” Awa ndi mau amene anthu ena amakamba akaona ana ofanana kwambili ndi makolo ao. Zimenezi n’zosadabwitsa cifukwa cakuti mwacibadwa mwana aliyense amatengela atate ndi amai ake. Yehova, Atate wathu wakumwamba, ndiye anatipatsa moyo. (Sal. 36:9) Ifeyo monga ana ake aumunthu, timafanana ndi Mulungu m’njila zambili. Cifukwa cakuti tinalengedwa m’cifanizilo cake, timatha kuganiza, kupanga zosankha ndi kukhala paubwenzi wolimba ndi ena.—Gen. 1:26.

2. N’cifukwa ciani n’zotheka kukhala paubwenzi ndi Yehova?

2 N’zotheka kukhala paubwenzi wolimba ndi Yehova. Ubwenzi umenewu umatheka cifukwa cakuti Mulungu amatikonda ndipo ngati ife tili ndi cikhulupililo mwa iye ndi mwana wake. Yesu anati: “Mulungu anakonda kwambili dziko mwakuti anapeleka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupilila iye asawonongeke, koma akhale ndi moyo wosatha.” (Yoh. 3:16) Pali anthu ambili amene anakhalako pa ubwenzi wolimba ndi Yehova. Tiyeni tikambilane zitsanzo ziŵili za anthu amenewa.

“BWENZI LANGA ABULAHAMU”

3, 4. Kodi ubwenzi wa Yehova ndi Abulahamu unasiyana bwanji ndi ubwenzi umene Yehova anali nao ndi Aisiraeli?

3 Yehova anacha Abulahamu, kholo la Aisiraeli kuti ‘bwenzi lake.’ (Yes. 41:8) N’ciani cinacititsa kuti munthu wokhulupilika ameneyu athe kukhala paubwenzi wolimba ndi Mlengi wake? Cinali cifukwa cakuti Abulahamu anali ndi cikhulupililo.—Gen. 15:6; ŵelengani Yakobo 2:21-23.

4 Aisiraeli omwe anali mbadwa za Abulahamu, poyamba anali paubwenzi ndi Yehova ndipo iye anali Atate wao. Komabe comvetsa cisoni n’cakuti io anataya ubwenzi wao ndi Mulungu. Cifukwa ciani? Cifukwa cakuti analephela kukhulupilila malonjezo a Yehova.

5, 6. (a) Kodi munacita ciani kuti mukhale paubwenzi ndi Yehova? (b) Kodi ndi mafunso ati amene tifunika kuganizila?

5 Tikamaphunzila zambili za Yehova, m’pamenenso timayamba kumukhulupilila ndi kumukonda kwambili. Ganizilani mmene munamvelela pamene munadziŵa kuti Mulungu ndi weni-weni ndi kuti mungathe kukhala naye paubwenzi wolimba. Munadziŵanso kuti tonsefe tinabadwa ocimwa cifukwa ca kusamvela kwa Adamu. Munazindikila kuti anthu ndi otalikilana ndi Mulungu. (Akol. 1:21) Ndiyeno munazindikila kuti Atate wathu wakumwamba amene ndi wacikondi sali kutali ndi ife ndipo amatiganizila. Pamene munadziŵa kuti iye anapeleka nsembe ya dipo la Yesu, munayamba kukhulupilila nsembeyo ndi kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu.

6 Pamene tiganizila mmene tinadziŵila Yehova, tiyenela kudzifunsa kuti: ‘Kodi ubwenzi wanga ndi Mulungu ukupita patsogolo? Kodi ndili ndi cikhulupililo colimba mwa Yehova ndipo kodi cikondi canga mwa iye cimakula tsiku lililonse?’ Munthu wina wakale amene anali paubwenzi wolimba ndi Yehova anali Gidiyoni. Tsopano tiyeni tikambilane za Gidiyoni ndi kuona mmene tingatengele citsanzo cake cabwino.

“YEHOVA NDI MTENDELE”

7-9. (a) Kodi ndi zinthu zocititsa cidwi ziti zimene zinacitikila Gidiyoni? Nanga zotsatilapo zake zinali zotani? (Onani cithunzi-thunzi kuciyambi kwa nkhani ino.) (b) Kodi tiyenela kucita ciani kuti tikhale pa ubwenzi wolimba ndi Yehova?

7 Woweluza Gidiyoni anatumikila Yehova panthawi yovuta pambuyo pakuti Aisiraeli alowa m’Dziko Lolonjezedwa. Lemba la Oweruza caputala 6 limanena kuti mngelo wa Yehova anaonekela kwa Gidiyoni ku Ofira. Panthawiyo, Amidiyani amene anali kukhala moyandikana ndi Aisiraeli anali pa udani woopsa ndi Aisiraeliwo. Pa cifukwa cimeneco, Gidiyoni anali kupunthila tiligu mopondelamo mphesa amene anali malo obisika kuti abise tiligu mwamsanga Amidiyani akabwela. Gidiyoni anadabwa kuti pamene mngelo anaonekela kwa iye anamucha kuti “munthu wolimba mtima ndi wamphamvu.” Ngakhale kuti Yehova anapulumutsa Aisiraeli ku Iguputo, Gidiyoni panthawiyi anakaikila ngati Yehova adzawathandizadi. Polankhula mmalo mwa Mulungu, mngeloyo anatsimikizila Gidiyoni kuti Yehova adzamuthandizadi.

8 Gidiyoni anafuna kudziwa kuti adzakwanitsa bwanji ‘kupulumutsa Isiraeli m’manja mwa Amidiyani.’ Yehova anamuyankha mosapita m’mbali kuti: “Popeza ndidzakhala ndi iwe, udzaphadi Amidiyani ngati kuti ukupha munthu mmodzi.” (Ower. 6:11-16). Cifukwa cakuti anali kukaikilabe, Gidiyoni anapempha Mulungu kuti amupatse cizindikilo. Mosakaikila pamene anali kukambilana ndi mngelo, Gidiyoni anali kuona kuti Yehova ndi weni-weni.

9 Zimene zinacitika pambuyo pake zinalimbitsa cikhulupililo ca Gidiyoni ndipo anayandikila kwambili kwa Yehova. Gidiyoni anakonza cakudya ndi kupatsa mngeloyo. Mngeloyo anakhudza cakudyaco ndi ndodo yake ndipo moto unanyeketsa cakudyaco mozizwitsa. Ataona zimenezi Gidiyoni anazindikila kuti mngeloyo anatumidwadi ndi Yehova. Iye anacita mantha ndi kufuula kuti: “Kalanga ine Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa! Ndaonana ndi mngelo wa Yehova maso ndi maso.” (Ower. 6:17-22) Kodi zimenezi zinapangitsa kuti ubwenzi wa Gidiyoni ndi Mulungu usokonezeke? Ayi ndithu. M’malomwake zinalimbitsa ubwenzi wake ndi Mulungu. Zinathandiza Gidiyoni kudziŵa bwino kwambili Yehova ndi kukhala naye pamtendele. Umboni wa zimenezi ndi wakuti iye anacha guwa la nsembe limene anamanga pamalowo kuti “Yehova-salomu.” Dzina limeneli limatanthauza kuti “Yehova ndi Mtendele.” (Ŵelengani Oweruza 6:23, 24; mau a munsi) Tikamasinkha-sinkha pa zimene Yehova amaticitila tsiku lililonse, timayamba kumuona monga bwenzi lathu leni-leni. Tikamapemphela kwa Yehova nthawi zonse, timakhala ndi mtendele woculuka wa mumtima ndipo ubwenzi wathu ndi iye umalimba kwambili.

NDANI ANGAKHALE ‘MLENDO M’CIHEMA’ CA YEHOVA?

10. Malinga ndi lemba la Salimo 15:3, 5, kodi Yehova amafuna kuti tizicita ciani kuti tikhale mabwenzi ake?

10 Pali zinthu zina zimene tifunika kucita kuti Yehova akhale Bwenzi lathu. Malinga ndi zimene zinalembedwa pa Salimo 15, Davide anaimba nyimbo yofotokoza zimene tifunika kucita kuti ‘tikhale mlendo m’cihema’ ca Yehova kapena kuti tikhale pa ubwenzi ndi Mulungu. (Sal. 15:1) Tsopano tiyeni tikambilane zinthu ziŵili mwa zinthu zimenezi. Zinthu ziŵilizi ndi kupewa misece ndi kukhala oona mtima m’zinthu zonse. Davide ananena kuti mlendo m’cihema ca Yehova “sanena misece ndi lilime lake. . .Ndipo salandila ciphuphu kuti akhotetse mlandu wa munthu wosalakwa.”—Sal. 15:3, 5.

11. N’cifukwa ciani tifunika kupewa misece?

11 Pa Salimo 34:13, Davide anacenjeza kuti: “Tetezani lilime lanu ku zinthu zoipa.” Kulephela kutsatila malangizo ouzilidwa amenewa kungaononge ubwenzi wathu ndi Atate wathu wakumwamba amene ndi wolungama. Misece kapena kuti mijedo ndi limodzi mwa makhalidwe a Satana amene ndi mdani wamkulu wa Yehova. Liu la Cingelezi limene limamasulidwa kuti “Mdyelekezi,” linacokela ku liu la Cigiriki limene limatanthauza kuti “woneneza.” Kukhala wosamala ndi zimene timakamba zokhudza ena kudzatithandiza kukhalabe pa ubwenzi ndi Yehova. Tifunika kusamala kwambili maka-maka tikamakamba za abale amene ali paudindo mumpingo.—Ŵelengani Aheberi 13:17; Yuda 8.

12, 13. (a) N’cifukwa ciani tifunika kucita zinthu zonse moona mtima? (b) Kodi anthu ena amakhudzidwa bwanji tikakhala oona mtima?

12 Atumiki a Yehova amafunikanso kukhala oona mtima osati odyela masuku pamutu anzao. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Pitilizani kutipemphelela, pakuti tikukhulupilila kuti tili ndi cikumbumtima coona, popeza tikufuna kucita zinthu zonse moona mtima.” (Aheb. 13:18) Popeza kuti timafunitsitsa “kucita zinthu zonse moona mtima,” timapewa kudyela masuku pamutu abale athu. Mwacitsanzo, ngati tinawalemba nchito, timacita nao zinthu mwacilungamo ndi kuwapatsa malipilo mogwilizana ndi zimene tinapangana. Monga Akristu, tiyenela kucita zinthu moona mtima ndi anthu onse kuphatikizapo anchito athu. Ndipo ngati tinalembedwa nchito ndi Mkristu mnzathu, timapewa kumudyela masuku pamutu mwa kufuna kuti aziticitila zinthu zina zabwino kuposa anchito ena.

13 Nthawi zambili anthu m’dzikoli amayamikila Mboni za Yehova cifukwa cakuti ndi anthu oona mtima. Mwacitsanzo, bwana wa kampani ina yaikulu yazomanga-manga anaona kuti Mboni za Yehova ndi zokhulupilika. Iye anati: “Inu nthawi zonse mumasunga mapangano.” (Sal. 15:4) Kukhala oona mtima kumatithandiza kukhalabe pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. Ndiponso Atate wathu wakumwamba amene ndi wacikondi amatamandidwa.

THANDIZANI ENA KUKHALA MABWENZI A YEHOVA

14, 15. Tikakhala muulaliki, kodi tingathandize bwanji anthu ena kukhala mabwenzi a Yehova?

14 Anthu ambili amene timakumana nao muulaliki samaona Mulungu monga bwenzi lao lapamtima ngakhale kuti amakhulupilila kuti iye aliko. Kodi tingawathandize bwanji? Ganizilani malangizo amene Yesu anapatsa ophunzila ake 70 pamene anawatuma aŵili-aŵili kuti akalalikile. Iye anawauza kuti: “Mukafika panyumba, coyamba muzinena kuti, ‘Mtendele ukhale panyumba pano.’ Ndipo ngati pakhomopo pali munthu wokonda mtendele, mtendele wanu udzakhala pa iye. Koma ngati palibe, udzabwelela kwa inu.” (Luka 10:5, 6) Tikakhala ndi mzimu waubwenzi polalikila, tingapangitse anthu kukopeka ndi coonadi. Tikakumana ndi anthu otsutsa, kukhala waubwenzi kudzathandiza kuti tipewe mikangano ndi kutsegula mpata wakuti nthawi ina akatilandile mwaulemu.

15 Tikakumana ndi anthu amene anasokeletsedwa ndi cipembedzo conama kapena amene amatsatila miyambo yacikunja, timawalankhula mwaubwenzi ndi mwamtendele. Anthu onse, maka-maka amene akunyansidwa ndi zinthu za m’dzikoli ndipo akufuna kudziŵa zambili za Mulungu amene timalambila, timawalandila ndi manja aŵili ku misonkhano yathu. Nkhani zimene zimapezeka mu Nsanja ya Olonda za mutu wakuti “Baibulo Limasintha Anthu” zili ndi zitsanzo zambili zocititsa cidwi za anthu otelo.

KUGWILA NCHITO PAMODZI NDI BWENZI LATHU LAPAMTIMA

16. N’cifukwa ciani timachedwa mabwenzi a Yehova ndiponso “anchito anzake”?

16 Anthu amene amagwilila nchito pamodzi, kaŵili-kaŵili amakhala pa ubwenzi wolimba. Anthu onse odzipeleka kwa Yehova ali ndi mwai wochedwa mabwenzi ake ndiponso “anchito anzake.” (Ŵelengani 1 Akorinto 3:9.) Tikamalalikila ndi kupanga ophunzila, timadziŵa bwino makhalidwe apamwamba a Atate wathu wakumwamba. Timaona mmene mzimu wake woyela umatithandizila kugwila bwino nchito yolalikila uthenga wabwino.

17. Kodi cakudya ca kuuzimu cimene timalandila pa misonkhano yadela ndi yacigawo cimaonetsa bwanji kuti Yehova ndi Bwenzi lathu?

17 Tikamagwila mwacangu nchito yopanga ophunzila, timalimbitsa ubwenzi wathu ndi Yehova. Timaona mmene Yehova walepheletsela zoyesa-yesa za adani zofuna kuletsa nchito yolalikila. Tikaganizila zimene zakhala zikucitika zaka zaposacedwapa, timaona mmene Mulungu amasamalilila anthu ake. Timacita cidwi ndi mmene amatipatsila cakudya cokonzedwa bwino ca kuuzimu nthawi zonse. Misonkhano yacigawo ndi yadela imaonetsa kuti Atate wathu wacikondi amadziŵa bwino mavuto athu ndi zosowa zathu. Pambuyo pa msonkhano wacigawo, banja lina linalemba kuti: “Msonkhanowu watikhudza mtima kwambili. Taona kuti Yehova amakonda kwambili aliyense wa ife ndipo amafunitsitsa kuti zinthu zizitiyendela bwino.” Banja linanso la ku Germany linalembela kalata ku Ofesi ya Nthambi yoyamikila mmene abale a ku Ireland anawalandilila bwino ndi kuwasamalila pamsonkhano wacigawo kumeneko. Iwo anati: “Tikuyamikila kwambili Yehova ndi Yesu Kristu, Mfumu imene iye anaika. Iwo anatilola kuti tikhale mbali ya gulu ili lomwe ndi logwilizana kwambili. Sitimakamba cabe kuti ndife ogwilizana koma timasangalaladi ndi mgwilizano weni-weni pakati pathu. Zimene tinaona pa msonkhano wacigawo wa ku Dublin nthawi zonse zizitikumbutsa mwai wamtengo wapatali umene tili nao wotumikila Mulungu wathu wamkulu limodzi ndi inu nonse.”

MABWENZI AMAKAMBILANA

18. Kodi tiyenela kudzifunsa mafunso ati pankhani yolankhulana ndi Yehova?

18 Ubwenzi umalimba ngati anthu amakambilana momasuka. Masiku ano, anthu amakonda kutumilana mauthenga pafoni kapena pa Intaneti. Popeza kuti Yehova ndiye Bwenzi lathu la pamtima, kodi tili ndi cizolowezi colankhulana naye m’pemphelo? Iye ndi “Wakumva pemphelo.” (Sal. 65:2) Koma kodi timakonda kulankhula naye m’phemphelo kawili-kawili?

19. N’ciani cingatithandize kufotokoza za mumtima mwathu kwa Atate wathu wakumwamba ngati zimativuta kutelo?

19 Atumiki ena a Mulungu zimawavuta kulankhula zimene zili mumtima mwao. Koma Yehova amafuna kuti tizilankhula naye momasuka. (Sal. 119:145; Maliro 3:41) Ngati zimativuta kufotokoza zimene zili mumtima mwathu, sitiyenela kutaya mtima, thandizo lilipo. Paulo analembela Akristu a ku Roma kuti: “Cimene tiyenela kupemphelela monga mmene tiyenela kupemphela sitikucidziŵa, koma mzimu umacondelela m’malo mwathu ndi madandaulo amene sitinathe kuwafotokoza. Koma iye amene amasanthula mitima amadziŵa zimene mzimu ukutanthauza, cifukwa umacondelela m’malo mwa oyela mogwilizana ndi cifunilo ca Mulungu.” (Aroma 8:26, 27) Kusinkha-sinkha mau olembedwa m’mabuku a m’Baibulo monga a Yobu, Masalimo ndi Miyambo, kudzatithandiza kuti tizitha kufotokoza za mumtima mwathu kwa Yehova.

20, 21. Kodi mau a Paulo a pa Afilipi 4:6, 7 amatitonthoza bwanji?

20 Tikakumana ndi zinthu zothetsa nzelu, tiyenela kutsatila malangizo ouzilidwa amene Paulo analembela Akristu a ku Filipi. Iye anati: “Musamade nkhawa ndi kanthu kalikonse, koma pa ciliconse, mwa pemphelo ndi pembedzelo, pamodzi ndi ciyamiko, zopempha zanu zidziŵike kwa Mulungu.” Tikamalankhula momasuka ndi Yehova, tidzatonthozedwa pa mavuto athu. Ndiye cifukwa cake Paulo anapitiliza ndi mau akuti: “Mtendele wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse, udzateteza mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.” (Afil. 4:6, 7) Nthawi zonse tifunika kukhala oyamikila cifukwa ca “mtendele wa Mulungu” umene ndi wapadela ndipo umateteza mitima yathu ndi maganizo athu.

21 Pemphelo limatithandiza kulimbitsa ubwenzi wathu ndi Yehova. Motelo, ‘tizipemphela mosalekeza.’ (1 Ates. 5:17) Tiyeni tipitilizebe kulimbitsa ubwenzi wathu ndi Mulungu ndi kucita zinthu mogwilizana ndi malamulo ake olungama. Ndiponso tiyenela kumasinkha-sinkha za madalitso amene timapeza cifukwa cokhala paubwenzi weni-weni ndi Yehova amene ndi Atate wathu, Mulungu wathu ndi Bwenzi lathu.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani