TSANZILANI CIKHULUPILILO CAO
Anapilila Zinthu Zopanda Cilungamo
ELIYA anali kuyenda m’cigwa ca Yorodano. Iye anali atayenda kwa milungu ingapo kulowela kumpoto ndipo anali kucokela ku Phili la Horebe limene linali kutali. Atafika ku Isiraeli, anaona kuti zinthu tsopano zinali zitasintha. Mavuto amene anali m’dzikolo cifukwa ca cilala coopsa anayamba kucepa. Mvula inali itayamba kugwa ndipo alimi anali kulima minda yao. Mneneliyu ayenela kuti analimbikitsidwa pamene anaona kuti zinthu zayamba kumelanso. Koma iye anali kudela nkhawa kwambili anthu. Iwo anali kudwala mwakuuzimu. Kulambila Baala kunali kofala m’dzikolo ndipo Eliya anafunika kucita zambili kuti athandize anthuwo.a
Eliya atafika pafupi ndi tauni ya Abele-mehola, anapeza anthu akulima munda waukulu ndi ng’ombe 24 zimene zinali kukoka mapulawo. Iwo anazimanga ziŵili-ziŵili pa joko ndipo zonse zinali kulimila pamodzi m’mundawo. Munthu amene Eliya anali kufuna ndi Elisa amene anali kulima ndi pulawo yomaliza. Yehova anasankha Elisa kuti adzalowe m’malo mwa Eliya. Pa nthawi ina, Eliya anali kuganiza kuti panalibe wina aliyense amene anali kutumikila Mulungu mokhulupilika kupatulapo iye ndipo mwacionekele anali kufunitsitsa kukumana ndi Elisa.—1 Mafumu 18:22; 19:14-19.
Kodi mwina Eliya sanali kufuna kupatsako ena mwai ndi nchito zina zimene anali nazo? Kodi anali ndi nkhawa kuti munthu wina adzamuloŵa m’malo? Sitikudziŵa, koma n’zotheka kuti anali ndi nkhawa imeneyo cifukwa cakuti “anali munthu monga ife tomwe.” (Yakobo 5:17) Kaya maganizo ake anali otani, Baibulo limanena kuti: “Eliya anapita pamene panali Elisa n’kumuponyela covala cake cauneneli.” (1 Mafumu 19:19) Covala cimeneci cinali copangidwa ndi cikopa ca nkhosa kapena mbuzi ndipo anali kucivala monga mkhanjo umene unali kuonetsa kuti anapatsidwa nchito yapadela ndi Yehova. Kuponya covalaco pamapewa a Elisa kunali ndi tanthauzo lapadela. Kucita zimenezi kunaonetsa kuti Eliya anamvela lamulo la Yehova ndi mtima wonse lakuti aike Elisa kukhala womulowa m’malo. Eliya anali kukhulupilila ndi kumvela Mulungu wake.
Elisa, amene anali wacinyamata panthawiyo, anali wofunitsitsa kuthandiza mneneli wacikulileyo. Koma iye sanafunike kulowa m’malo Eliya nthawi yomweyo. Kwa zaka 6, Elisa anali kuyenda ndi mneneli wacikulileyo ndi kumuthandiza pa nchito yake. Pambuyo pake Elisa anayamba kudziŵika monga munthu “amene anali kuthilila Eliya madzi osamba m’manja.” (2 Mafumu 3:11) Mwacionekele, Eliya analimbikitsidwa kwambili kukhala ndi mtumiki wakhama ndi wom’thandiza ameneyu. Mosakaikila, anthu aŵili amenewa anakhala paubwenzi wolimba. Iwo anali kulimbikitsana, ndipo kucita zimenezi kunawathandiza kuti asataye mtima ndi zinthu zambili zopanda cilungamo zimene anali kuona m’dzikolo. Vuto lalikulu linali lakuti mfumu Ahabu inali kupitilizabe kucita zinthu zoipa.
Kodi mukukumana ndi zinthu zopanda cilungamo? Ambili a ife timakumana ndi zinthu zopanda cilungamo m’dziko lino loipa. Kukhala ndi bwenzi lokonda Mulungu kungatithandize kupilila zoipa. Tingaphunzile zambili kwa Eliya amene anali ndi cikhulupililo camphamvu pamene anali kulimbana ndi zinthu zopanda cilungamo.
“NYAMUKA, PITA . . . UKAKUMANE NDI AHABU”
Eliya ndi Elisa anayesetsa kuthandiza Aisiraeli mwakuuzimu. Mosakaikila, io anali kuphunzitsa anthu ena kuti akhale aneneli. N’kutheka kuti io anakhazikitsa makalasi amene anali kugwilitsila nchito kuphunzitsila anthu amenewo. M’kupita kwa nthawi, Yehova anapatsa Eliya nchito ina. Iye anauza Eliya kuti: “Nyamuka, pita ku Samariya ukakumane ndi Ahabu mfumu ya Isiraeli.” (1 Mafumu 21:18) Kodi Ahabu analakwa ciani?
Mfumuyo inapandukila Mulungu ndipo inakhala mfumu yoipa kwambili ya Isiraeli kuposa mafumu ena onse amene analiko iye asanakhale mfumu. Iye anakwatila Yezebeli amene anapangitsa kuti kulambila Baala kufalikile m’dzikolo ndipo mfumu nayonso inayamba kulambila Baala. (1 Mafumu 16:31-33) Kulambila Baala kunali kuphatikizapo kucita miyambo yokhudza mphamvu ya kubeleka, kucita ciwelewele ndi kupeleka ana ao nsembe. Ahabu sanamvelenso lamulo la Yehova lakuti aphe Beni-hadadi, Mfumu yoipa ya Siriya. Mwacionekele, Ahabu sanaphe Beni-hadadi cifukwa cofuna ndalama. (1 Mafumu 20) Panthawiyo Ahabu ndi Yezebeli anakhala adyela, okonda cuma ndi ankhanza kwambili kuposa ndi kale lonse.
Ahabu anali ndi nyumba yaikulu kwambili yacifumu ku Samariya. Analinso ndi nyumba ina ku Yezereeli, dela limene linali pa mtunda wa makilomita pafupi-fupi 37 kucokela ku Samariya. Pafupi ndi nyumba yaciŵiliyi panali munda wa mpesa. Munda umenewo unali wa Naboti, koma Ahabu anali kuusilila. Ahabu anaitanitsa Naboti ndi kumuuza kuti akufuna kugula mundawo. Koma Naboti anati: “Sindingacite zimenezo pamaso pa Yehova, kupeleka colowa ca makolo anga kwa inuyo.” (1 Mafumu 21:3) Kodi Naboti anali wamwano? Anthu ena amaganiza conco. Koma pamenepa iye anali kumvela Lamulo la Yehova lakuti Aisiraeli sayenela kugulitsilatu malo amene ndi colowa ca banja lao. (Levitiko 25:23-28) Naboti sanafune kucita zinthu zosemphana ndi Lamulo la Mulungu. Naboti anali kudziŵa kuti Ahabu ndi munthu woopsa, koma iye analankhula naye cifukwa anali ndi cikhulupililo colimba ndiponso wolimba mtima.
Koma Ahabu sanali kuganizila za Malamulo a Yehova ngakhale pang’ono. Iye anapita kunyumba “ali wacisoni ndi wokhumudwa” cifukwa cakuti zofuna zake sizinacitike. Baibulo limanena kuti iye “anakagona pabedi lake n’kutembenukila kukhoma, ndipo sanadya cakudya.” (1 Mafumu 21:4) Pamene Yezebeli anaona kuti mwamuna wake ali ndi msunamo, mwamsanga anapanga ciwembu ca kupha Naboti ndi anthu osalakwa a m’banja lake n’colinga cakuti alande munda umene Ahabu anali kufuna.
Tikamaŵelenga za ciwembu cimene Yezebeli anakonza, timanyansidwa ndi kuipa mtima kwake. Mfumukazi Yezebeli inali kudziŵa kuti Malamulo a Mulungu amanena kuti pamafunikila mboni ziŵili kuti zitsimikizile munthu kuti wacita colakwa cacikulu. (Deuteronomo 19:15) Motelo iye analemba makalata m’dzina la Ahabu, ndi kulamula anthu olemekezeka a ku Yezereeli kuti apeze anthu aŵili amene angalole kupeleka umboni wonama wotsutsana ndi Naboti. Iye anawauza kuti adzamunamizile kuti watembelela Mulungu ndi mfumu, zimene cilango cake cinali kuphedwa. Comvetsa cisoni n’cakuti ciwembu cakeco cinathekadi. ‘Amuna awili opanda pakewo’ anayamba kupeleka umboni wotsutsana ndi Naboti ndipo iye anaponyedwa miyala mpaka kufa. Koma si zokhazo, naonso ana aamuna a Naboti anaphedwa.b (1 Mafumu 21:5-14; Levitiko 24:16; 2 Mafumu 9:26) Ahabu ananyala-nyaza udindo wake monga mutu wa banja ndi kutsatila zofuna za mkazi wake za kupha anthu osalakwa.
Ganizilani mmene Eliya anamvelela pamene Yehova anamuuza zimene mfumu ndi mfumukazi Yezebeli anacita. Anthu oipa akamacitila nkhanza anthu osalakwa, zimatipweteka mtima kwambili. (Salimo 73:3-5, 12, 13) Masiku ano, anthu ambili amacita zinthu zopanda cilungamo, ndipo nthawi zina amene amacita zimenezi ndi atsogoleli amene amati ndi atumiki a Mulungu. Komabe nkhani ino ingatitonthoze. Pankhaniyi, Baibulo likutikumbutsa kuti palibe cobisika pamaso pa Yehova. Iye amaona zonse. (Aheberi 4:13) Kodi iye amacita ciani akaona zinthu zoipa zimene zikucitika?
“WANDIPEZA KODI MDANI WANGA?”
Yehova anauza Eliya kupita kwa Ahabu. Mulungu anamuuzanso momveka bwino kuti: “Iye ali m’munda wa mpesa wa Naboti.” (1 Mafumu 21:18) Yezebeli atauza Ahabu kuti munda wa mpesa tsopano ndi wake, Ahabu mwamsanga anapita ku mundawo. Iye anaiwala kuti Yehova akumuona. Taganizilani cisangalalo cimene anali naco pamene anali kuyenda-yenda m’mundamo poganizila kuti adzakhala ndi munda wabwino. Koma mwadzidzidzi, Eliya anamufikila. Nkhope ya Ahabu inasintha cifukwa ca ukali ndi cidani, ndipo mwaukali anati: “Wandipeza kodi mdani wanga?”—1 Mafumu 21:20.
Mau a Ahabu akuonetsa kuti iye anali ndi maganizo opanda nzelu. Coyamba, mwa kuuza Eliya kuti “Wandipeza,” iye anasonyeza kuti sanali kuganizila kuti Mulungu akumuona. Koma Yehova anali atamuona kale. Iye anaona Ahabu pamene anasankha kucita zoipa ndi kusangalala ndi zinthu zimene anapeza cifukwa ca ciwembu ca Yezebeli. Mulungu anaona kuti cifukwa ca mtima wokonda cuma, Ahabu anakhala wopanda cifundo, cilungamo ndi cikondi. Caciŵili, pamene Ahabu anauza Eliya kuti “mdani wanga,” anaonetsa kuti iye anali kudana ndi bwenzi la Yehova Mulungu, limene likanamuthandiza kusiya kucita zoipa.
Tingaphunzile zambili tikaganizila zimene Ahabu anacita. Tisaiwale kuti Yehova Mulungu amaona zonse. Monga Tate wacikondi, iye amaona ngati tayamba kuyenda njila yolakwika ndipo amafunitsitsa kuti tisinthe. Pofuna kutithandiza, Mulungu amagwilitsila nchito mabwenzi ake okhulupilika, monga mmene Eliya analili, kuti atipatse malangizo ake. Ndiye cifukwa cake kuona mabwenzi a Mulungu monga adani athu kungakhale kulakwitsa kwambili.—Salimo 141:5.
Poyankha mau a Ahabu, Eliya anati: “Inde ndakupezani.” Iye anadziŵa kuti Ahabu anali wakuba, wakupha ndi wopandukila Yehova Mulungu. Eliya anafunika kulimba mtima kuti alankhule ndi munthu woipa ameneyu. Iye anauzanso Ahabu uthenga waciweluzo wocokela kwa Mulungu. Yehova anaona kuti makhalidwe oipa a m’banja la Ahabu anali kufalikila kwa anthu ena. Conco, Eliya anauza Ahabu kuti Mulungu wanena kuti ‘adzaseselatu’ kapena kuonongelatu anthu onse a m’banja la Ahabu. Iye ananenanso kuti Yezebeli adzaweluzidwa.—1 Mafumu 21:20-26.
Eliya analibe maganizo akuti anthu akacita zinthu zoipa kapena zopanda cilungamo samalangidwa. Masiku ano, n’zosavuta kuganiza kuti anthu oipa samalangidwa. Koma nkhani ya Eliya imeneyi imatikumbutsa kuti Yehova Mulungu amaona zoipa zimene zikucitika ndi kuti amacitapo kanthu panthawi yake. Mau ake amatitsimikizila kuti iye adzathetselatu zinthu zonse zopanda cilungamo. (Salimo 37:10, 11) Koma mwina mungafunse kuti: ‘Kodi Mulungu amangolanga anthu osawacitila cifundo?’
“KODI WAONA MMENE AHABU WADZICEPETSELA?”
Mwina Eliya anadabwa ataona zimene Ahabu anacita pamene anamva ciweluzo ca Mulungu. Baibulo limati: “Ahabu atangomva mau amenewa, anang’amba zovala zake n’kuvala ciguduli. Iye anayamba kusala kudya, kugona paciguduli ndipo anali kuyenda mwacisoni.” (1 Mafumu 21:27) Kodi Ahabu anali kusonyeza kulapa?
Tinganene kuti mwina anasintha zocita zake. Ahabu anadzicepetsa, ndipo kucita zimenezi si cinali cinthu copepuka kwa munthu wonyada ndi wodzitukumula ameneyo. Koma kodi analapa kucokela pansi pa mtima? Taganizilani zocita za Manase mfumu imene inacita zinthu zoipa kwambili kuposa Ahabu. Pamene Yehova analanga Manase, iye anadzicepetsa ndipo anapempha Yehova kuti amuthandize. Koma Manase anacita zambili kuposa pamenepa. Iye anasintha zocita zake mwa kucotsa mafano amene anaika. Anayambanso kutumikila Yehova mwakhama ndi kulimbikitsa anthu ake kutumikila Mulungu. (2 Mbiri 33:1-17) Koma n’zomvetsa cisoni kuti Ahabu sanacite zimenezi.
Kodi Yehova anaona kudzicepetsa kumene Ahabu anasonyeza? Yehova anauza Eliya kuti: “Kodi waona mmene Ahabu wadzicepetsela pamaso panga? Popeza wadzicepetsa cifukwa ca ine, sindidzabweletsa tsokali m’masiku ake. M’malomwake, ndidzalibweletsa panyumba yake m’masiku a mwana wake.” (1 Mafumu 21:29) Kodi Yehova anamukhululukila Ahabu? Iyai. Mulungu amakhululukila anthu okhawo amene amalapa kucokela pansi pa mtima. (Ezekieli 33:14-16) Koma popeza kuti Ahabu anaonetsa kukhumudwa pang’ono ndi zimene anacita, Yehova anamucitila cifundo pang’ono. Anamucitila cifundo m’njila yakuti Ahabu sanaone banja lake lonse likuonongedwa cimene cikanakhala cinthu copweteka mtima kwambili.
Koma Yehova sanasinthe ciweluzo cake pa Ahabu. Patapita nthawi, Yehova anafunsa angelo ake za njila yabwino yopusitsila Ahabu kuti apite kunkhondo kumene adzaphedwa. Patangopita nthawi yocepa, Yehova anaweluza Ahabu. Iye anavulazidwa pa nkhondo ndipo anafela m’galeta lake. Baibulo limafotokozanso cinthu cina comvetsa cisoni cimene cinacitika pamene anthu anali kutsuka galeta la mfumu. Limati agalu anali kunyambita magazi a mfumuyo. Cocitika cimeneci cinakwanilitsa mau amene Yehova anauza Ahabu kudzela mwa Eliya akuti: “Pamalo amene agalu ananyambita magazi a Naboti, pomweponso agalu adzanyambita magazi ako, a iweyo.”—1 Mafumu 21:19; 22:19-22, 34-38.
Kuphedwa kwa Ahabu kunakumbutsa Eliya, Elisa ndi anthu ena a Mulungu okhululupilika kuti Yehova sanaiwale kulimba mtima ndi cikhulupililo ca Naboti. Mulungu wacilungamo salephela kulanga anthu oipa panthawi yake yoyenela ndipo amaweluza mwacifundo ngati n’koyenela kutelo. (Numeri 14:18) Limeneli linali phunzilo lofunika kwambili limene Eliya anaphunzila pambuyo popilila ulamulilo wa mfumu yoipa kwa zaka zambili. Kodi mukukumana ndi zinthu zopanda cilungamo? Kodi mumalakalaka Mulungu atakonza zinthu? Ngati ndi conco, muyenela kukhala ndi cikhulupililo monga Eliya. Iye pamodzi ndi mnzake Elisa anapitiliza kulengeza uthenga wa Mulungu ndi kupilila zinthu zopanda cilungamo.
a Aisiraeli anali kulambila Baala cifukwa anali kuganiza kuti ndi amene anali kubweletsa mvula ndi kupangitsa nthaka kukhala ya conde. Conco, Yehova anacititsa cilala m’dzikolo kwa zaka zitatu ndi hafu n’colinga cakuti aonetse kuti Baala ndi wopanda mphamvu. (1 Mafumu caputala 18) Onani nkhani za mutu wakuti “Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo” zopezeka m’magazini a Nsanja ya Olonda a January 1 ndi April 1, 2008.
b Yezebeli anapanga ciwembu ca kupha ana a Naboti mwina cifukwa coganiza kuti io adzatenga munda wa mpesawo monga colowa cao.