LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • lfb phunzilo 34 tsa. 84-tsa. 85 pala. 2
  • Gidiyoni Agonjetsa Amidiyani

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Gidiyoni Agonjetsa Amidiyani
  • Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • Nkhani Zofanana
  • Gidiyoni Ndi Asilikali Ake 300
    Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
  • Inu Akulu—Tengelani Citsanzo ca Gidiyoni
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2023
  • Yehova Ndi Bwenzi Lathu Lapamtima
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
  • “Pita ndi Mphamvu Zimene Ndakupatsazi”
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2021
Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
lfb phunzilo 34 tsa. 84-tsa. 85 pala. 2
Gidiyoni na asilikali ake aliza malipenga, kuphwanya mitsuko, kuthuvula nyale zawo na kufuula

PHUNZILO 34

Gidiyoni Agonjetsa Amidiyani

M’kupita kwa nthawi, Aisiraeli anamusiyanso Yehova na kuyamba kulambila milungu yonyenga. Kwa zaka 7, Amidiyani anali kuba ziŵeto za Aisiraeli na kuwononga mbewu m’minda yawo. Poopa Amidiyani, Aisiraeli anali kupita kukabisala m’mapanga kapena kuti m’mphako na m’mapili. Iwo anacondelela Yehova kuti awapulumutse. Conco, Yehova anatumiza mngelo kwa wacinyamata Gidiyoni. Mngeloyo anati: ‘Yehova wasankha iwe, munthu wolimba mtima ndi wamphamvu.’ Gidiyoni anafunsa kuti: ‘Ndine ndani ine, kuti nipulumutse Aisiraeli?’

Kodi Gidiyoni akanadziŵa bwanji kuti Yehova ndiye anam’sankha? Anaika ubweya wa nkhosa pa nthaka, na kupempha Yehova kuti: ‘Mailo kuseni ngati ubweya uwu udzakhala na mame koma nthaka n’kukhala youma, nidzadziŵa kuti mufuna ine nipulumutse Aisiraeli.’ M’maŵa mwake, ubweya uja unali wokhuta na mame, koma nthaka inali youma! Gidiyoni anapemphanso kuti tsiku lotsatila m’maŵa, ubweya ukakhale wouma koma nthaka ikanyowe na mame. Zinacitikadi. Ndipo Gidiyoni lomba anatsimikiza kuti Yehova anali atam’sankhadi. Iye lomba anasonkhanitsa asilikali ake kuti akamenyane na Amidiyani.

Yehova anauza Gidiyoni kuti: ‘Nidzamenyela nkhondo Aisiraeli kuti apambane. Koma cifukwa uli na asilikali ambili, ungaganize kuti wapambana nkhondo mwa mphamvu zako. Auze kuti aliyense amene wacita mantha abwelele ku nyumba.’ Asilikali 22,000 anabwelela, cakuti panatsala asilikali 10,000. Koma Yehova anati: ‘Ukali na asilikali ambili-mbili. Pita nawo ku mtsinje na kuwauza kuti amwe madzi. Usankhepo cabe amene akhale chelu kuyang’ana adani pakumwa madzi.’ Asilikali 300 cabe ndiwo anakhala chelu pakumwa madzi. Yehova analonjeza kuti amuna ocepa amenewa adzagonjetsa asilikali 135,000 acimidiyani.

Usiku wa tsikulo, Yehova anauza Gidiyoni kuti: ‘Nthawi lomba yafika yogonjetsa Amidiyani!’ Gidiyoni anapatsa asilikali ake nyanga za mwana wa nkhosa, na mbiya zikulu-zikulu, zokhala na nyale mkati mwake. Ndiyeno anawauza kuti: ‘Onani, zimene nicite ine, imwenso mucite zimenezo.’ Gidiyoni analiza lipenga lake, kuphwanya mbiya yake, kuthuvula nyale yake, na kufuula kuti: ‘Lupanga la Yehova ndi la Gidiyoni!’ Nawonso asilikali ake onse 300 anacita cimodzimodzi. Amidiyani pocita mantha na kusokonezeka, anabalalika n’kumathaŵila kulikonseko. Posokonezeka motelo, anayamba kuphana okha-okha. Apanso Yehova anathandiza Aisiraeli kugonjetsa adani awo.

Asilikali acimidiyani acita mantha

“Kuti mphamvu yoposa yacibadwa icokele kwa Mulungu, osati kwa ife.”—2 Akorinto 4:7

Mafunso: Kodi Yehova anacita ciani potsimikizila Gidiyoni kuti ndiye anamusankha? N’cifukwa ciani Gidiyoni anali na asilikali 300 cabe?

Oweruza 6:1–16; 6:36–7:25; 8:28

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani