Mawu Oyamba a Cigawo 8
Yehova anadalitsa Solomo mwa kum’patsa nzelu zoculuka, na mwayi womanga kacisi. Koma m’kupita kwa nthawi, iye anasiya Yehova. Ngati ndimwe kholo, m’fotokozeleni mwana wanu zimene zinapangitsa Solomo kuti asiye Mulungu. Ufumu unagaŵika, ndipo mafumu oipa anapangitsa mtundu wa Isiraeli kupanduka na kuyamba kulambila mafano. Pa nthawi imeneyo, aneneli a Yehova ambili okhulupilika anazunzidwa na kuphedwa. Mfumukazi Yezebeli anapangitsa kuti ufumu wa kumpoto uloŵelele m’kulambila mafano. Imeneyi inali nthawi yovuta kwambili kwa Aisiraeli. Koma pakati pa Aisiraeli, panali atumiki a Yehova ambili okhulupilika. Ena a iwo anali Mfumu Yehosafati na mneneli Eliya.