Mawu Oyamba a Cigawo 9
M’cigawo cino tidzaphunzila za acicepele, aneneli, komanso mafumu amene anaonetsa cikhulupililo camphamvu mwa Yehova. Ku Siriya, kunali kamtsikana kena kaciisiraeli komwe kanali kukhulupilila kuti mneneli wa Yehova angacilitse Namani. Mneneli Elisa anali na cidalilo conse mwa Yehova kuti adzam’teteza ku gulu la adani ake. Mkulu wa Ansembe Yehoyada anaika moyo wake paciswe, kuti ateteze wacicepele Yehoasi kwa ambuye ake aakazi oipa kwambili, Ataliya. Mfumu Hezekiya inali na cidalilo cakuti Yehova adzapulumutsa Yerusalemu, ndipo iye sanagonje kwa Asuri pomuwopseza. Mfumu Yosiya inafafaniza kulambila mafano m’dziko lawo, inamanganso kacisi, na kuthandiza anthu kuyambanso kulambila koona.