NYIMBO 102
“Thandizani Ofooka.”
Yopulinta
1. Tonse tingalakwitse
Nthawi ‘liyonse,
Koma Mulungu wathu
Amatikonda.
Iye ni cikondi;
Ni wokoma mtima.
Tionetse cikondi
Kwa ovutika.
2. Tiyeni tilimbitse
Onse ofo’ka.
Tingaŵalimbikitse
Mwa mau athu.
Ni nkhosa za M’lungu
Adzaŵalimbitsa.
Akapeza mavuto
Tiŵathandize.
3. Ise tisasulize
Anthu ofo’ka.
Tiŵaonetse
Kuti timaŵakonda.
Ticite mwakhama
Poŵalimbikitsa.
Tikaŵathandizila,
Atonthozedwa.
(Onaninso Yes. 35:3, 4; 2 Akor. 11:29; Agal. 6:2.)