NYIMBO 116
Mphamvu ya Kukoma Mtima
Yopulinta
(Aefeso 4:32)
1. Tiyamikila imwe Yehova,
M’lungu wacikondi.
Ngakhale kuti muli na mphamvu
Ndimwedi wokoma mtima.
2. Mwana wanu Yesu aitana
Onse ovutika,
Kuti iwo abwele kwa iye,
Ndipo adzatonthozedwa.
3. Tikhale ngati M’lungu na Yesu,
Mu zocita zathu.
Ngati tikhala okoma mtima,
Tidzakhaladi amphamvu.
(Onaninso Mika 6:8; Mat. 11:28-30; Akol. 3:12; 1 Pet. 2:3.)