NYIMBO 120
Tengelani Kufatsa kwa Khristu
Yopulinta
1. Yesu anali wopambana m’zonse.
Koma sananyade, sanadzikweze.
Modzicepetsa anadzipeleka,
Kucita cifunilo ca Yehova.
2. Olemedwa na nkhawa zosautsa,
Adzaŵathandiza kuthetsa nkhawa.
Ndipo iwo adzatsitsimulidwa
Akafuna za Ufumu coyamba.
3. Yesu anati ‘se ndise abale.
Tisadzikweze tikhale ofatsa.
Yehova M’lungu adzatidalitsa,
Tidzapezadi moyo wamuyaya.
(Onaninso Miy. 3:34; Mat. 5:5; 23:8; Aro. 12:16.)