NYIMBO 135
Yehova Alangiza Mwacikondi Kuti: “Mwana Wanga, Khala Wanzelu”
Yopulinta
(Miyambo 27:11)
1. Anyamata na ‘tsikana,
nimveleni—
Mdani wanga
wonitonzayo aone
Kuti mun’tumikila
na mtima wonse.
Onetsani onse
kuti munikonda.
(KOLASI)
Ana anga nikukondani.
Inu khalani anzelu.
Sankhani kunitumikila
Ndipo nidzasangalala.
2. Muzisangalala
ponitumikila.
Mukalakwa
n’dzakukhululukilani.
Olo kuti ena
sangakukondeni,
Ine Atate wanu
nikukondani.
(KOLASI)
Ana anga nikukondani.
Inu khalani anzelu.
Sankhani kunitumikila
Ndipo nidzasangalala.
(Onaninso Deut. 6:5; Mlal. 11:9; Yes. 41:13)