NYIMBO 51
Tinadzipeleka kwa Mulungu
Yopulinta
1. M’lungu watikokela ise kwa Yesu.
Afuna kuti tim’tsatile.
Iye wationetsa
Kuwala kwa co’nadi.
Lomba ise tasankha
Kutumikila Iye.
(KOLASI)
Tadzipeleka kwa Atate Yehova.
Mwa iye na Yesu tikondwela.
2. M’pemphelo ise tilonjeza Yehova,
Kukhala okhulupilika.
Ise timakondwela
Kulengeza za iye,
Na za Ufumu wake,
Ndipo sitidzaleka.
(KOLASI)
Tadzipeleka kwa Atate Yehova.
Mwa iye na Yesu tikondwela.
(Onaninso Sal. 43:3; 107:22; Yoh. 6:44.)