LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • lvs mutu 4 masa. 45-59
  • N’cifukwa Ciani Tiyenela Kulemekeza Ulamulilo?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • N’cifukwa Ciani Tiyenela Kulemekeza Ulamulilo?
  • Mmene Tingakhalilebe mu Cikondi ca Mulungu
  • Ŵelengani mu “m’Cikondi ca Mulungu”
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • N’CIFUKWA CIANI KUMVELA KUMAKHALA KOTIVUTA?
  • CIFUKWA CAKE TIMALEMEKEZA ULAMULILO WA YEHOVA
  • KULEMEKEZA ULAMULILO M’BANJA
  • KULEMEKEZA ULAMULILO MU MPINGO
  • KULEMEKEZA OIMILA BOMA
  • Lemekezani Ena
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
  • N’cifukwa Ciyani Ulemu Ni Wofunika?
    Galamuka!—2024
  • Mmene Banja Lanu Lingakhalile Lacimwemwe
    Zimene Baibulo Ingatiphunzitse
  • Kumvetsa Tanthauzo la Umutu Mumpingo
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2021
Mmene Tingakhalilebe mu Cikondi ca Mulungu
lvs mutu 4 masa. 45-59
Tate alangiza ana ake mwacikondi

MUTU 4

N’cifukwa Ciani Tiyenela Kulemekeza Ulamulilo?

“Lemekezani anthu, kaya akhale amtundu wotani. Kondani gulu lonse la abale, opani Mulungu, lemekezani mfumu.”—1 PETULO 2:17.

1, 2. (a) Kodi tifunika kutsatila malangizo a ndani? (b) Nanga tidzakambilana mafunso ati m’nkhani ino?

PAMENE munali mwana, mwacidziŵikile nthawi zina makolo anu anakuuzani kucita zinthu zimene imwe simunafune. Munali kuŵakonda makolo anu, ndipo munali kudziŵa kuti muyenela kuŵamvela. Ngakhale n’conco, mwina nthawi zina simunafune kuwamvela.

2 Naye Yehova, monga Tate wathu, amatikonda. Amatisamalila, ndipo amatipatsa zonse zofunikila kuti tizikondwela na moyo. Ndiponso amatitsogolela kuti tipambane. Nthawi zina, amaseŵenzetsa anthu ena kuti ationetse njila pamene tifunikila thandizo. Conco, tiyenela kulemekeza ulamulilo wa Yehova. (Miyambo 24:21) Koma n’cifukwa ciani nthawi zina cimakhala cotivuta kutsatila malangizo a Yehova? Nanga n’cifukwa ninji iye amafuna kuti tizikonkha malangizo ake? Nanga timaonetsa bwanji kuti timalemekeza ulamulilo wake?—Onani Mfundo ya Kumapeto 9.

N’CIFUKWA CIANI KUMVELA KUMAKHALA KOTIVUTA?

3, 4. Kodi ise anthu tinakhala bwanji opanda ungwilo? N’cifukwa ciani nthawi zina cimativuta kulandila uphungu?

3 Pokhala anthu, timakhala na kamzimu kaja kokonda kupanduka. Zimenezi zakhala zikuonekela kungocokela pamene mwamuna na mkazi oyamba, Adamu na Hava anacimwa. Olo kuti Mulungu anawalenga angwilo, iwo anapandukila ulamulilo wake. Kucokela pamenepo, anthu onse akhala akubadwa ali opanda ungwilo. Ndiye cifukwa cimodzi cimene nthawi zina cimatilepheletsa kumvela Mulungu kapena anthu anzathu. Cifukwa cina n’cakuti anthu amene Yehova amaseŵenzetsa kuti atipatse malangizo, naonso ni opanda ungwilo.—Genesis 2:15-17; 3:1-7; Salimo 51:5; Aroma 5:12.

4 Cifukwa ca kupanda ungwilo kwathu, timakhala onyada cakuti kumakhala kotivuta kuti tilandile uphungu. Mwacitsanzo, mu Isiraeli wakale, Yehova anasankha Mose kuti atsogolele anthu Ake. Koma mwamuna wina dzina lake Kora, amene anatumikila Yehova kwa zaka zambili, anatayilatu ulemu kwa Mose cifukwa ca kunyada kwake. Mose anali mtsogoleli wa anthu a Mulungu, koma sanali munthu wonyada iyai. Iye anadziŵika kuti anali munthu wodzicepetsa kuposa anthu onse m’nthawi yake. Koma Kora sanauvomeleze utsogoleli wa Mose, cakuti anakopa anthu ambili kuti agwilizane naye popandukila Mose. Nanga cinacitika n’ciani kwa Kora na gulu lake? Onse anaphedwa. (Numeri 12:3; 16:1-3, 31-35) M’Baibo, timapezamo zitsanzo zambili zotiphunzitsa kuti kunyada kumaitana tsoka.—2 Mbiri 26:16-21; onani Mfundo ya Kumapeto 10.

5. Kodi anthu aseŵenzetsa bwanji mphamvu zawo molakwa?

5 Mwina munamvelapo mau akuti, “Mphamvu zimawononga munthu wabwino.” M’mbili yonse, anthu akhala akuseŵenzetsa mphamvu molakwa. (Ŵelengani Mlaliki 8:9.) Mwacitsanzo, pamene Yehova anasankha Sauli kukhala mfumu ya Isiraeli, anali munthu wabwino ndiponso wodzicepetsa. Koma cifukwa analola kunyada na nsanje kukula mu mtima mwake, anayamba kuzunza Davide, munthu wopanda cifukwa. (1 Samueli 9:20, 21; 10:20-22; 18:7-11) M’kupita kwa nthawi, Davide anakhala mfumu, ndipo anali mmodzi wa mafumu abwino kwambili amene analamulilapo mtundu wa Isiraeli. Koma m’kupita kwa zaka, ngakhale Davide anayamba kuseŵenzetsa mphamvu zake molakwa. Anacita cigololo na Batiseba, mkazi wa Uriya, ndipo anayesa kuphimba chimo lake mwa kutumiza Uriya kunkhondo kuti akaphedwe.—2 Samueli 11:1-17.

CIFUKWA CAKE TIMALEMEKEZA ULAMULILO WA YEHOVA

6, 7. (a) Kodi cikondi cathu pa Yehova cimatipangitsa kucita ciani? (b) Kodi citsanzo ca Yesu cingatithandize bwanji kukhala omvela ngakhale pamene kuli kovuta kutelo?

6 Timalemekeza utsogoleli wa Yehova cifukwa timam’konda. Ndipo popeza timam’konda kupambana wina aliyense kapena cina ciliconse, timafuna kucita zinthu zom’kondweletsa. (Ŵelengani Miyambo 27:11; Maliko 12:29, 30.) Kungocokela pa Adamu na Hava m’munda wa Edeni, colinga ca Satana ni kupangitsa anthu kuti azikaikila ulamulilo wa Yehova. Mdyelekezi amafuna tiziganiza kuti Yehova alibe danga yotiuza zocita. Koma timadziŵa kuti imeneyi ni bodza yamkunkhuniza. Ise timavomeleza mau aya akuti: “Ndinu woyenelela, inu Yehova Mulungu wathu wamphamvu, kulandila ulemelelo ndi ulemu, cifukwa munalenga zinthu zonse.”—Chivumbulutso 4:11.

7 Pamene munali mwana, makolo anu anakuphunzitsani kuwamvela. Koma mwina nthawi zina, cinali covuta kwa imwe kuti muwamvele. Ifenso atumiki a Yehova, nthawi zina cingakhale covuta kukhala omvela. Koma cifukwa Yehova timam’konda na kumulemekeza, timayesetsa kumumvela. Yesu anatisiila citsanzo cabwino. Anali womvela kwa Yehova ngakhale pamene zinthu zinali zovuta. Ndiye cifukwa cake anauza Atate wake kuti: “Cifunilo canu cicitike, osati canga.”—Luka 22:42; onani Mfundo ya Kumapeto 11.

8. Kodi Yehova amatitsogolela m’njila monga ziti? (Onani bokosi yakuti “Mvelani Uphungu.”)

8 Masiku ano, Yehova amatitsogolela m’njila zosiyana-siyana. Mwacitsanzo, anatipatsa Baibo, komanso akulu mu mpingo. Conco, tingaonetse kuti timalemekeza ulamulilo wa Yehova ngati tilemekeza anthu amene iye amawaseŵenzetsa potitsogolela. Ngati tikana cithandizo cawo, ndiye kuti takana Yehova. Pamene Aisiraeli anakana Mose, unali mlandu waukulu kwa Yehova. Anaona kuti anali kukana Iye.—Numeri 14:26, 27; onani Mfundo ya Kumapeto 12.

MVELANI UPHUNGU

NTHAWI na nthawi, munthu wina angatipatse uphungu wocokela pa mfundo za m’Baibo. Ngati tilephela kulandila uphungu, zifukwa zake zimakhala zitatu izi.—Miyambo 19:20.

  • Tiona kuti uphunguwo si woyenelela kwa ise. Mwina tiganiza kuti munthu wotipatsa uphunguyo samvetsetsa bwino-bwino zimene zaticitikila. (Aheberi 12:5) Koma tiyenela kudzifunsa kuti, ‘Kodi palibedi cifukwa comveka cimene wanipatsila uphunguwu?’ (Miyambo 19:3) Mukamvetsetsa cifukwa cimene wakupatsilani uphungu, kumakhala kosavuta kuulandila.—Ŵelengani Miyambo 4:13.

  • Sitinakonde kapelekedwe ka uphungu. Munthu wangwilo ndiye angapeleke uphungu wangwilo m’njilanso yangwilo. (Aroma 3:23; Yakobo 3:2) M’malo moyang’ana pa kapelekedwe ka uphungu, yang’anani pa zimene akukamba na mmene zingakuthandizileni.

  • Tiona kuti uphunguwo ni wosatifunikila cifukwa ca msinkhu kapena cidziŵitso cimene tili naco. M’nthawi ya Aisiraeli, ngakhale mfumu inali kulandila uphungu kucokela kwa aneneli, ansembe, komanso anthu ena mu ufumu wake. (2 Samueli 12:1-13; 2 Mbiri 26:16-20) Ngati tilandila uphungu modzicepetsa wocokela m’Baibo, umatithandiza kuyandikila Yehova.—Tito 3:2.

Kumbukilani kuti uphungu wocokela m’Baibo, ni mphatso yocokela kwa Yehova. Iye amatikonda na kutifunila zabwino nthawi zonse. Conco, yesetsani kumalandila uphungu na kuuseŵenzetsa.—Aheberi 12:6-11.

9. Kodi cikondi cimatithandiza bwanji kukonkha malangizo?

9 Ngati tilemekeza ulamulilo, timaonetsanso kuti timakonda abale na alongo athu. Mwacitsanzo, kukacitika ngozi ya zacilengedwe, gulu lopeleka cithandizo limagwila nchito capamodzi kuti apulumutse anthu ambili. Kuti gulu limeneli ligwile bwino nchito, pamafunikila kukhala otsogolela, ndipo aliyense m’gulu limenelo afunika kutsatila malangizo opelekedwa. Koma bwanji ngati wina anyalanyaza malangizowo, n’kumangocita zimene afuna? Ngakhale ngati zolinga zake n’zabwino, kusamvela kwake malangizo kungakwiyitse anzake kwambili. N’cimodzimodzi na ise. Ngati sitimvela malangizo ocokela kwa Yehova, komanso kwa anthu amene iye anawapatsa ulamulilo, anthu ena amavutikilamo. Koma tikakhala omvela kwa Yehova, timaonetsa kuti timakonda abale na alongo athu, ndipo timalemekeza makonzedwe a Yehova.—1 Akorinto 12:14, 25, 26.

10, 11. Kodi tidzakambilana ciani lomba?

10 Ciliconse cimene Yehova angatiuze kucita n’cotipindulitsa. Ngati tilemekeza ulamulilo m’banja mwathu, mu mpingo, komanso kwa oimila boma, anthu onse amapindula.—Deuteronomo 5:16; Aroma 13:4; Aefeso 6:2, 3; Aheberi 13:17.

11 N’cifukwa ciani Yehova amafuna kuti tizilemekeza anthu ena? Tikamvetsetsa cifukwa cake, tidzayamba kulemekeza bwino anthu ena. Lomba, tiyeni tikambilane mwatsatane-tsatane mmene tingaonetsele ulemu m’mbali zitatu.

KULEMEKEZA ULAMULILO M’BANJA

12. Kodi mwamuna angaonetse bwanji kuti amalemekeza ulamulilo?

12 Yehova ndiye anayambitsa banja ndipo munthu aliyense anam’patsa mbali yake. Ngati aliyense m’banja amadziŵa zimene Yehova afuna kwa iye, banja imakhala yogwilizana komanso yamtendele. (1 Akorinto 14:33) Yehova anaika mwamuna kukhala mutu wa banja. Conco, amamuyembekezela kusamalila bwino mkazi wake na ana ake, na kuŵatsogolela mwacikondi. Inde, mwamuna adzayankha mlandu kwa Yehova za mmene amasamalila banja lake. Mwamuna wacikhristu amakhala wokoma mtima ndiponso wacikondi. Ndipo amasamalila banja lake monga mmene Yesu amasamalila mpingo. Ngati mwamuna acita zimenezi, amaonetsa kuti amalemekeza Yehova.—Aefeso 5:23; onani Mfundo ya Kumapeto 13.

Tate aŵelengela ana ake buku yakuti Phunzilani kwa Mphunzitsi Waluso

Tate wacikhristu amatengela citsanzo ca Yesu posamalila banja lake

13. Kodi mkazi angaonetse bwanji kuti amalemekeza ulamulilo?

13 Mkazi wacikhristu nayenso ali na mbali yofunika komanso yolemekezeka. Amathandizila mwamuna wake pamene iye akuyesetsa kusamalila udindo wake monga mutu wa banja. Mothandizana na mwamuna wake, mkazi ali na udindo wophunzitsa ana awo. Njila imodzi imene angaphunzitsile ana ake kukhala aulemu ni mwa kukhala citsanzo kwa iwo. (Miyambo 1:8) Monga mkazi wanzelu, afunika kulemekeza mwamuna wake na kugwilizana pa zigamulo zake. Ngakhale pamene sagwilizana naye pa cinacake, afunika kufotokoza maganizo ake mwa njila yacikondi komanso yaulemu. Ngati mkazi wacikhristu ni wokwatiwa kwa mwamuna amene si Mboni, zimakhala zovuta nthawi zina. Koma ngati apitiliza kukonda mwamuna wake na kum’lemekeza, mwina tsiku lina nayenso angadzafune kudziŵa Yehova na kuyamba kum’lambila.—Ŵelengani 1 Petulo 3:1.

14. Kodi ana m’banja angalemekeze bwanji ulamulilo?

14 Ana ni amtengo wapatali kwa Yehova, ndipo amafunikila citetezo na uyang’anilo wabwino. Ngati ana amvela makolo awo, makolo amakondwela ngako. Ndipo pomvela makolo awo, amaonetsa ulemu waukulu kwa Yehova na kum’kondweletsa. (Miyambo 10:1) Palinso mabanja ena a kholo imodzi, amene amalela okha ana. Zimenezi zingakhale zovuta kwa kholo, komanso kwa ana. Koma ngati anawo amamvela amayi awo kapena atate awo, umoyo wa banjalo umakhalako bwino kwambili. Mulimonse mmene zingakhalile, kulibe banja yangwilo. Koma banja iliyonse ingakhale yacimwemwe ngati aliyense m’banjamo atsatila malangizo a Yehova. Pamenepo, Mlengi wa mabanja onse, Yehova, amalemekezeka.—Aefeso 3:14, 15.

KULEMEKEZA ULAMULILO MU MPINGO

15. Tingaonetse bwanji kuti timalemekeza ulamulilo mu mpingo?

15 Yehova amatitsogolela kupitila mu mpingo wacikhristu, ndipo anapatsa Yesu ulamulilo kuti aziuyang’anila. (Akolose 1:18) Yesu nayenso anapatsa udindo “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu,” kuti asamalile anthu a Mulungu pa dziko lapansi. (Mateyu 24:45-47) Masiku ano, Bungwe Lomamulila ndilo “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu.” Bungwelo limatipatsa zonse zofunikila, komanso panthawi yake, kuti tikhalebe olimba m’cikhulupililo. Akulu, atumiki othandiza, komanso oyang’anila madela, amalimbikitsa mipingo padziko lonse, ndipo amalandila malangizo kucokela ku Bungwe Lolamulila. Abale onsewa ali na udindo wotisamalila. Iwo adzayankha mlandu kwa Yehova za mmene amayendetsela udindo umenewu. Conco, ngati tilemekeza amuna amenewa, timalemekeza Yehova.—Ŵelengani 1 Atesalonika 5:12; Aheberi 13:17; onani Mfundo ya Kumapeto 14.

16. N’cifukwa ciani tingakambe kuti akulu na atumiki othandiza amaikidwa na mzimu woyela?

16 Akulu na atumiki othandiza amathandiza mpingo kukhala wolimba m’cikhulupililo, ndiponso wogwilizana. Koma nawonso ni anthu opanda ungwilo monga ise. Nanga amasankhidwa bwanji? Iwo afunika kukwanilitsa ziyenelezo za m’Baibo. (1 Timoteyo 3:1-7, 12; Tito 1:5-9) Yehova anaseŵenzetsa mzimu woyela kuthandiza olemba Baibo kufotokoza ziyenelezo zimenezo. Akulu amapemphela kwa Yehova kuti awapatse mzimu woyela, pamene akukambilana za amene angaikidwe kukhala mkulu kapena mtumiki wothandiza. N’zoonekelatu kuti Yesu na Yehova ni amene kweni-kweni akusamalila mipingo. (Machitidwe 20:28) Ndiye cifukwa cake, amuna osankhidwa kuti azilimbikitsa mipingo alidi mphatso zocokela kwa Mulungu.—Aefeso 4:8.

17. Kuti aonetse ulemu, kodi nthawi zina mlongo angafunikile kucita ciani?

17 Koma nthawi zina, mpingo ungakhale ulibe akulu kapena atumiki othandiza kuti asamalile mbali zofunikila. Zikakhala conco, abale ena obatizika angathandizile. Ngati palibe ngakhale abale, mlongo angasamalile mbali zimenezo. Koma afunikila kuvala cophimba kumutu, citambala, duku, kapena cisote. (1 Akorinto 11:3-10) Mwa kutelo, mlongoyo amaonetsa kuti amalemekeza makonzedwe a Yehova a umutu, m’banja komanso mu mpingo.—Onani Mfundo ya Kumapeto 15.

KULEMEKEZA OIMILA BOMA

18, 19. (a) Timaphunzilapo mfundo yanji pa Aroma 13:1-7? (b) Kodi timaonetsa bwanji ulemu ku maboma?

18 Pakali pano, Yehova analola kuti maboma a anthu akhale na ulamulilo, ndipo tifunika kuwalemekeza. Maboma amakhazikitsa dongosolo m’dziko, na kuthandiza anthu powakonzela zinthu zofunikila. Akhristu amamvela malangizo opezeka pa Aroma 13:1-7. (Ŵelengani.) Timalemekeza “olamulila akulu-akulu” na kumvela malamulo a m’dziko kapena m’mudzi umene tikhalamo. Malamulo amenewo angakhudze banja lathu, bizinesi yathu, kapena zinthu zathu. Mwacitsanzo, timakhoma misonkhano na kulembetsa zimene boma imafuna. Koma tiyenela kucita ciani ngati boma itilamula kucita zinthu zotsutsana na malamulo a Mulungu? Mtumwi Petulo anakamba kuti: “Tiyenela kumvela Mulungu monga wolamulila, osati anthu.”—Machitidwe. 5:28, 29.

19 Ngati ticita zinthu na oimila boma, monga jaji kapena wapolisi, nthawi zonse tizikamba nawo mwaulemu. Akhristu acicepele afunika kulemekeza matica awo, komanso anthu ena ogwila nchito pa sukulu pawo. Ku nchito, tiyenela kupeleka ulemu kwa abwana, ngakhale ngati anchito anzathu ena saŵalemekeza. Ngati ticita zimenezi, timatengela citsanzo ca mtumwi Paulo. Iye anali kulemekeza oimila boma, ngakhale kuti nthawi zina zinali zovuta. (Machitidwe 26:2, 25) Ngakhale ena aticitile nkhanza, ise timakhalabe aulemu.—Ŵelengani Aroma 12:17, 18; 1 Petulo 3:15.

20, 21. Cingacitike n’ciani ngati tionetsa ulemu kwa anthu ena?

20 Pa dziko lonse lapansi, ulemu pakati pa anthu ukucepela-cepela. Koma anthu a Yehova ni osiyana. Ise timafuna kulemekeza munthu aliyense. Timamvela uphungu wa mtumwi Petulo wakuti: “Lemekezani anthu, kaya akhale amtundu wotani.” (1 Petulo 2:17) Ngati tilemekeza anthu, iwonso amaona. Yesu anati: “Onetsani kuwala kwanu pamaso pa anthu, kuti aone nchito zanu zabwino ndi kuti alemekeze Atate wanu wakumwamba.”—Mateyu 5:16.

21 Ngati tipeleka ulemu m’banja mwathu, mu mpingo, komanso m’mbali zina za umoyo wathu, citsanzo cathu cabwino cingalimbikitse anthu ena kufuna kudziŵa zambili za Yehova. Ndipo poonetsa ulemu kwa anthu ena, timalemekeza Yehova mwiniwake. Pamenepo Yehova amakondwela, cifukwa amaona kuti timam’konda.

MFUNDO ZA M’BAIBO

1 YEHOVA AMASEŴENZETSA ANTHU ENA KUTSOGOLELA

“Lemekezani anthu, kaya akhale amtundu wotani. . . . Opani Mulungu.”—1 Petulo 2:17

N’cifukwa ciani nthawi zina kungakhale kovuta kutsatila malangizo?

  • Numeri 16:1-3; Mlaliki 8:9; Aroma 5:12

    Anthu amene Yehova amaaseŵenzetsa kutitsogolela ni opanda ungwilo monga ise.

  • Luka 22:42

    Yesu anapeleka citsanzo cabwino kwambili. Anali womvela kwa Yehova nthawi zonse.

  • Miyambo 27:11; Maliko 12:29, 30

    Cifukwa cokonda Yehova, timalemekeza makonzedwe ake. M’banja muli tate monga mutu. Ku sukulu kuli matica. Mu mpingo muli akulu.

2 YEHOVA NDIYE ANAKHAZIKITSA BANJA

“Ndikupinda mawondo anga kwa Atate, amene amapangitsa banja lililonse, . . . kukhala ndi dzina.”—Aefeso 3:14, 15

N’cifukwa ciani Yehova amafuna kuti tizilemekeza makonzedwe a banja?

  • Miyambo 10:1

    Yehova anakhazikitsa banja monga malo acitetezo okulilamo ana, komanso kuti onse m’banja azikondana.

  • Miyambo 1:8; 1 Akorinto 11:3; Aefeso 6:1-3; 1 Petulo 3:1

    Banja lonse limapindula ngati aliyense acita mbali yake.

3 YEHOVA ANAPATSA YESU ULAMULILO PA MPINGO

‘Khristu ndiye mutu wa mpingo.’—Aefeso 5:23

N’cifukwa ciani tifunika kukhala omvela mu mpingo?

  • Mateyu 24:45-47

    Yesu amaseŵenzetsa “kapolo wokhulupilila ndi wanzelu” kusamalila anthu a Mulungu pa dziko lapansi.

  • 1 Atesalonika 5:12; Aheberi 13:17

    Akulu na atumiki othandiza amathandiza mpingo kuti uzikhala wolimba. Ngati tikhala omvela kwa abalewa, timalemekeza ulamulilo wa Yehova.

  • Machitidwe 20:28

    Ngati tigwilizana na mpingo, aliyense amapindula. Ndiwo makonzedwe olambilila Yehova.

4 YEHOVA AMALOLA MABOMA KUKHALA NA ULAMULILO WAWO

“Palibe ulamulilo umene ungakhalepo kupatulapo ngati Mulungu waulola. Olamulila amene alipowa ali m’malo awo osiyana-siyana mololedwa ndi Mulungu.”—Aroma 13:1.

Kodi tingaonetse bwanji ulemu ku maboma?

  • Mateyu 5:16; 1 Petulo 3:15

    Timawaonetsa ulemu mwa zokamba zathu na zocita zathu. Powalemekeza m’njila zimenezi, timalemekezanso Yehova.

  • Machitidwe 26:2, 25; Aroma 12:17, 18

    Akhristu amamvela malamulo a dziko limene akhalamo. Amacita izi ngakhale pamene sakuwacitila zabwino.

  • Aroma 13:1-4

    Mfundo za m’Baibo zingakuthandizeni kuti muzimvela anthu a ulamulilo.

  • Mateyu 22:37-39; 26:52; Yohane 18:36; Machitidwe 5:27-29; Aheberi 10:24, 25

    Ngati a boma akuuzani kucita cinthu cosemphana na malamulo a Yehova, mufunika kusankha pakati pa kumvela anthu kapena Mulungu.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani