NKHANI YOPHUNZIRA 38
NYIMBO 120 Tengelani Kufatsa kwa Khristu
Lemekezani Ena
“Kulemekezedwa n’kwabwino kuposa siliva ndi golide.”—MIY. 22:1.
ZOFUNIKA KUMVETSETSA
Cifukwa cake tiyenera kulemekeza ena komanso mmene tingacitire zimenezo ngakhale pamene zili zobvuta kutero.
1. N’cifukwa ciani timamva bwino tikapatsidwa ulemu? (Miyambo 22:1)
N’ZOSACITA kufunsa kuti mumamva bwino anthu ena akakupatsani ulemu. Munthu aliyense amafuna kupatsidwa ulemu. Ndipo timasangalala munthu wina akatipatsa ulemu. Ndiye cifukwa cake Baibo imati: “Kulemekezedwa n’kwabwino kuposa siliva”!—Werengani Miyambo 22:1.
2-3. N’cifukwa ciani zimakhala zobvuta nthawi zina kucitira ena ulemu? Nanga ndani amene tiyenera kuwaonetsa ulemu?
2 Koma nthawi zina cimakhala cobvuta kuonetsa ena ulemu. Cifukwa cimodzi n’cakuti timaona zophophonya za ena. Cina, tikukhala m’nthawi imene ulemu ndi wosowa. Koma ife tiyenera kukhala aulemu. Cifukwa ciani? Cifukwa Yehova amafuna kuti tizilemekeza “anthu amitundu yonse.”—1 Pet. 2:17.
3 M’nkhani ino, tikambirana zimene kupatsa ulemu anthu ena kumatanthauza komanso mmene tingaonetsere ulemu kwa (1) a m’banja lathu, (2) alambiri anzathu, ndi (3) anthu amene si Mboni. Tikambirana mmene tingacitire zimenezo maka-maka zikakhala zobvuta kutero.
KODI KULEMEKEZA ENA KUMATANTHAUZANJI?
4. Kodi kulemekeza ena kumatanthauza ciani?
4 Kodi munganene kuti ulemu n’ciani? Mau akuti ulemu amatanthauza mmene timaonera anthu komanso mmene timacitira nao. Tikaona kuti munthu ali ndi makhalidwe abwino, anacita zinthu zinazake zabwino, kapena ali ndi ulamuliro winawake pa ife, timacita naye zinthu m’njira yoonetsa kuti timam’lemekeza. Komabe ulemu umakhaladi weniweni ukacokera mu mtima.—Mat. 15:8.
5. N’ciani cingatithandize kuti tizilemekeza anthu ena?
5 Yehova amafuna kuti tizilemekeza ena. Mwacitsanzo, iye amatiuza kuti tizilemekeza “olamulira akulu-akulu.” (Aroma 13:1, 7) Koma anthu ena amanena kuti, “Ndimapatsa ulemu anthu okhao amene ndi oyenereradi kupatsidwa ulemu.” Koma kodi kaganizidwe kameneka n’komveka? Ai. Pokhala atumiki a Yehova, timazindikira kuti kulemekeza ena sikudalira zocita zao, koma kumadalira cikondi cathu cozama pa Yehova komanso cikhumbo cofuna kum’sangalatsa.—Yos. 4:14; 1 Pet. 3:15.
6. Kodi n’zotheka kulemekeza munthu amene satilemekeza? Fotokozani (Onaninso cithunzi )
6 Ena angadzifunse kuti, ‘Kodi n’zotheka kulemekeza munthu amene sakukulemekeza?’ Inde. Ganizirani zitsanzo izi. Mfumu Sauli ananyazitsa mwana wake Yonatani pamaso pa anthu. (1 Sam. 20:30-34) Komabe, Yonatani anapitirizabe kuwalemekeza atate ake mwa kuwacirikiza kumenya nkhondo mpaka pamene iwo anamwalira. (Eks. 20:12; 2 Sam. 1:23) Pa nthawi ina, mkulu wansembe Eli ananeneza Hana kuti anali ataledzera. (1 Sam. 1:12-14) Komabe, Hana anakambabe naye mwaulemu Eli, ngakhale kuti zinali kudziwika mu Isiraeli yense kuti Eli analephera udindo wake monga kholo, komanso monga mkulu wa ansembe. (1 Sam. 1:15-18; 2:22-24) Ndipo anthu a ku Atene anali kunyoza Paulo pomuchula kuti anali “wobwetuka.” (Mac 17:18) Ngakhale zinali conco, Paulo anakamba nao mwaulemu. (Mac. 17:22) Zitsanzo zimenezi zionetseratu kuti cikondi cozama pa Yehova, komanso mantha oopa kumukhumudwitsa, zingatisonkhezere kuti tizilemekeza ena, osati pa nthawi yokhayo pamene zinthu zili bwino, koma ngakhale pamene zinthu zili zobvuta. Tiyeni tsopano tikambirane amene tiyenera kulemekeza komanso cifukwa cake tiyenera kuwalemekeza.
Ngakhale kuti atate ake anamunyanzitsa Yonatani, iye sanaleke kucirikiza ufumu wao (Onani ndime 6)b
MUZILEMEKEZA A M’BANJA LANU
7. N’ciani cingapangitse kuti zikhale zobvuta kwa ife kulemekezana m’banja?
7 Zimene zingapangitse kuti zikhale zobvuta kuwalemekeza. Timakhala nthawi yaitali ndi a m’banja lathu. Izi zimacititsa kuti tidziwe zimene amacita bwino ndi zophophonya zao. Ena angadwale matenda kapena angakhale ndi nkhawa kwambiri moti zingakhale zobvuta kuwasamalira. Ndipo ena angakambe mau kapena kucita zinthu zimene zingatikhumudwitse. M’malo moyesetsa kukhala osangalala komanso mwamtendele, mabanja ena amacita zinthu mosalemekezana ndipo izi zimapangitsa kuti azikhala okwiya kwa wina ndi mnzake. Zotsatira zake zimakhala zakuti samagwirizana. Monga mmene matenda angalepheretsere ziwalo za thupi kugwira bwino nchito pamodzi, nakonso kusalemekezana kungapangitse anthu a m’banja kusagwirizana. Koma monga mmene zilili kuti matenda ambiri amaciritsika, n’zothekanso a m’banja kuphunzira kukhala ndi ulemu komanso kuuonetsa kwa wina ndi mnzake.
8. N’cifukwa ciani m’pofunika kulemekeza a m’banja lathu? (1 Timoteyo 5:4, 8)
8 Cifukwa cake tiyenera kuwalemekeza. (Werengani 1 Timoteyo 5:4, 8.) M’kalata yake yoyamba kwa Timoteyo, Paulo anafotokoza mmene anthu a m’banja angasamalirane. Iye anafotokoza kuti colinga cacikulu cocitira zimenezi sikungofuna kukwaniritsa udindo ai, koma kuonetsa kuti ndi “odzipereka kwa Mulungu.” Mau akuti “kudzipereka kwa Mulungu,” amatanthauza kulambira Mulungu komanso kumutumikira mokhulupirika. Yehova ndiye anayambitsa banja. (Aef. 3:14, 15) Conco, tikalemekeza a m’banja mwathu, timakhala kuti tikulemekeza Yehova, Muyambitsi wa banja. Ici n’cifukwa camphamvu cotisonkhezera kuti tizilemekeza a m’banja lathu!
9. Kodi mwamuna ndi mkazi angacitirane bwanji ulemu? (Onaninso zithunzi)
9 Mmene tingawaonetsere ulemu. Mwamuna amene amalemekeza mkazi wake, amacita zinthu zoonetsa kuti mkazi wake ndi wamtengo wapatali kwa iye, kaya ali kwaokha kapena ali pa anthu. (Miy. 31:28; 1 Pet. 3:7) Iye amapeweratu kumenya mkazi wake, kumunyazitsa, kapena kumupangitsa kumva kuti ndi wacabe-cabe. Ariel,a amene akhala ku Argentina anati: “Nthawi zina mkazi wanga amakamba mau amene amandikhumudwitsa cifukwa ca matenda ake. Zikakhala conco, ndimakumbukira kuti iye akunena zimenezi cifukwa ca matenda ake osati kuti ndi mmene alili. Zikafika poipa kwambiri, lemba la 1 Akorinto 13:5 imandilimbikitsa kuti ndikambe naye mwaulemu osati momupepula.” (Miy. 19:11) Mkazi amaonetsa kuti amalemekeza mwamuna wake mwa kumukambira zabwino kwa ena. (Aef. 5:33) Iye amapewa mau onyoza, onyodola, komanso kumuchula maina omunyazitsa cifukwa amazindikira kuti zinthu za conco zili ngati nguwe imene ingaononge ukwati wao. (Miy. 14:1) Mlongo wina wa ku Italy amene mwamuna wake amalimbana ndi nkhawa anakamba kuti: “Nthawi zina ndimaona kuti mwamuna wanga amakhala ndi nkhawa ngakhale pa kanthu kang’ono-ng’ono. Kale, mau anga komanso nkhope yanga zinali kuonetsa kuti sindinali kumulemekeza. Koma ndimaona kuti ndikamaceza ndi amene amakamba za ena mwaulemu, inenso ndimalimbikitsidwa kuonetsa ulemu kwa mwamuna wanga.”
Tikamalemekeza anthu a m’banja lathu, timaonetsa kuti timalemekeza Mutu wa banja lathu Wamkulu, Yehova (Onani ndime 9)c
10. Kodi ana angaonetse bwanji kuti amalemekeza makolo ao?
10 Acicepere, muzimvera malamulo amene makolo anu anakuikirani. (Aef. 6:1-3) Muzikamba mwaulemu kwa makolo anu. (Eks. 21:17) Pamene makolo anu akukalamba, m’pamenenso amafunikira kwambiri cisamaliro canu. Muziyesetsa kuwasamalira. Naci citsanzo ca Mariya amene atate ake si a Mboni za Yehova. Atate ake atadwala, zinamubvuta kwambiri Mariya kuti awasamalire cifukwa sanali kucita naye mokoma mtima. Iye anakamba kuti: “Ndinapempha Yehova kuti andithandize kuonetsa atate kuti ndimawalemekeza. Mu mtima ndinati, ‘Popeza Yehova ndiye amafuna kuti ndizilemekeza makolo anga, iye adzandithandiza kucita zimenezo.’ M’kupita kwa nthawi, n’nazindikira kuti atate safunika kucita kusintha khalidwe lao kuti ndiyambe kucita nao mwaulemu.” Tikamalekeza a m’banja lathu mosasamala kanthu za zophophonya zao, timaonetsa kuti timalemekeza Muyambitsi wa banja, Yehova.
MUZILEMEKEZA ALAMBIRI ANZANU
11. Ndi zinthu ziti zingapangitse kuti cikhale cobvuta kucita nao mwaulemu alambiri anzathu?
11 Zimene zingacititse kuti zikhale zobvuta kuwalemekeza. Okhulupirira anzathu amayendera mfundo za m’Baibo pa umoyo wao. Komabe, iwo nthawi zina angacite nafe mopanda cikondi, mopanda cilungamo, kapena angatikhumudwitse. Ngati wokhulupirira mnzathu wacita zinthu zotipangitsa kukhala ndi “cifukwa codandaulira,” zingakhale zobvuta kuti tipitirize kucita naye mwaulemu. (Akol. 3:13) Koma n’ciani cingathandize kuti tisaleke kuwalemekeza?
12. N’cifukwa ciani n’kofunika kulemekeza okhulupirira anzathu? (2 Petulo 2:9-12)
12 Cifukwa cake tiyenera kuwalemekeza. (Werengani 2 Petulo 2:9-12.) M’kalata yake yaciwiri youziridwa, Petulo anakamba kuti ena mu mpingo anali kulankhula zonyoza ‘anthu amene Mulungu anawapatsa ulemerero,’ kutanthauza akulu mu mpingo. Kodi angelo okhulupirika amene anaona zimenezo anatani? “Cifukwa angelowo amalemekeza Yehova,” iwo sanakambe ngakhale liu limodzi lacipongwe ponena za anthuwo. Tangoganizirani, angelo omwe ndi apamwamba kuposa ife sanalankhule mau alionse acipongwe ponena za anthu odzikuza amenewo! M’malomwake, iwo anasiya nkhaniyo m’manja mwa Yehova kuti aweruze anthuwo ndi kuwadzudzula. (Aroma 14:10-12; yerekezerani ndi Yuda 9.) Pali phunziro labwino limene tingatengepo pa nkhaniyi. Ngati anthu otsutsa sitiyenera kukamba nao mopanda ulemu, kuli bwanji okhulupirira anzathu! M’malo mowacotsera ulemu, tiyenera ‘kukhala patsogolo’ powaonetsa ulemu. (Aroma 12:10) Kucita izi kumaonetsa kuti timalemekeza Yehova.
13-14. Kodi tingawaonetse bwanji ulemu abale ndi alongo mu mpingo? Perekani zitsanzo (Onaninso zithunzi.)
13 Mmene tingawaonetsere ulemu. Inu akulu, muziyesetsa kucita zinthu mwacikondi mukamaphunzitsa ena. (Filim. 8, 9) Wina akafunikira uphungu, muzicita naye mokoma mtima osati mwaukali. Inu alongo, mudzathandiza kuti mzimu wocitirana ulemu mu mpingo usathe mwa kupewa misece kapena manong’o-nong’o. (Tito 2:3-5) Tonsefe tingaonetse kuti timalemekeza akulu mwa kutsatira malangizo amene apereka komanso kuwauza kuti timayamikira khama lao pocititsa misonkhano, potsogolera pa nchito yolalikira, komanso pothandiza amene atenga “njira yolakwika.”—Agal. 6:1; 1 Tim. 5:17.
14 Mlongo wina dzina lake Rocío, cinamubvuta kulemekeza mkulu wina amene anamupatsa uphungu. Mlongoyu anati: “N’nakhumudwa cifukwa n’naona kuti mkuluyo sanalankhule nane mwacikondi. N’tafika kunyumba, n’nakamba zoipa zokhudza iye. Pansi pa mtima ndinakaikira ngati mkuluyo anali ndi zolinga zabwino pondipatsa uphunguwo. Conco sindinautsatire uphungu wake koma sindinafune kucita moonetsera.” N’ciani cinamuthandiza kusintha maganizo ake? Mwiniwakeyo anati: “Tsiku lina ndikuwerenga Baibo, ndinawerenga 1 Atesalonika 5:12, 13. N’tazindikira kuti sindikumuonetsa ulemu m’baleyo, cikumbumtima canga cinayamba kundibvutitsa. Ndinapemphera kwa Yehova ndipo ndinafufuza m’zofalitsa zathu kuti ndipeze nkhani imene ingandithandize kuongolera kaganizidwe kanga. Pamapeto pake ndinazindikira kuti bvuto siinali m’baleyo, koma ine ndine ndinali ndi bvuto cifukwa n’nali wodzikuza. Tsopano ndidziwa kuti popanda kudzicepetsa, sindingathe kulemekeza ena. Ndikali kufunikira kupanga masinthidwe. Koma ndikaonetsa ena ulemu, ndimamva bwino podziwa kuti ndakondweretsa Yehova.”
Tonsefe tingaonetse kuti timalemekeza akulu mu mpingo potsatira malangizo amene amatipatsa, komanso powayamikira pa khama limene amacita pogwira nchito zao (Onani ndime 13-14)
MUZILEMEKEZA ANTHU AMENE SI MBONI
15. N’cifukwa ciani nthawi zina zingakhale zobvuta kulemekeza anthu amene si Mboni?
15 Zimene zimapangitsa kuti zikhale zobvuta kuwalemekeza. Nthawi zambiri timakumana ndi anthu mu ulaliki amene alibe cidwi pa coonadi ca m’Baibo. (Aef. 4:18) Ena amasankha mwadala kusamvetsera uthenga wathu cifukwa ca zimene anaphunzitsidwa akali aang’ono. Nthawi zina, anthu amene timagwira nao nchito kapena amene timapita nao kusukulu si aubwenzi. Komanso, abwana athu kapena aphunzitsi athu angakhale kuti ndi obvuta kuwakondweretsa. Zikakhala conco, m’kupita kwa nthawi tingaleke kuwalemekeza ndipo tingaleke kucita nao mokoma mtima.
16. N’cifukwa ciani n’zofunika kucitira ulemu anthu amene akalibe kuyamba kutumikira Yehova? (1 Petulo 2:12; 3:15)
16 Cifukwa cake tiyenera kuwalemekeza. Sitiyenera kuiwala kuti Yehova amaona mmene timacitira ndi anthu amene si Mboni. Mtumwi Petulo anakumbutsa Akhristu kuti khalidwe lao labwino lingasonkhezere ena ‘kutamanda Mulungu.’ Pa cifukwa cimeneci, iye anawalimbikitsa kuti azikhalira kumbuyo cikhulupiriro cao “mofatsa ndiponso mwaulemu kwambiri.” (Werengani 1 Petulo 2:12; 3:15.) Kaya akuteteza cikhulupiriro cao pamaso pa akulu-akulu a boma kapena akukambirana ndi maneba ao, Akhristu anafunika kucita zimenezo ngati kuti ali pamaso pa Mulungu. Zili conco cifukwa Yehova amaona ndi kumvetsera zilizonse zimene tingakambe komanso mmene tingazikambire. Ici n’cifukwa camphamvu cotipangitsa kuti tizicita nao mwaulemu anthu amene si Mboni!
17. Kod tingaonetse bwanji kuti timalemekeza anthu amene si Mboni?
17 Mmene tingawaonetsere ulemu. Tikakhala mu ulaliki, tisapangitse munthu wina kuona kuti ndi wosafunika, cabe cifukwa cakuti sadziwa zambiri za m’Baibo. M’malomwake, tiziwaona kuti ndi amtengo wapatali kwa Mulungu komanso kuti amatiposa. (Hag. 2:7; Afil. 2:3) Conco ngati anthu akukambirani mau onyoza cifukwa ca zimene mumakhulupirira, musakambe nao mwaukali. Tiyenera kupewa kukamba mau amene angaonetse ngati kuti ndife anzeru kwambiri, amene angakhumudwitse anthuwo. (1 Pet. 2:23) Mukazindikira kuti mwakamba zinazake zimene mwadziimba nazo mlandu, muzipepetsa mwamsanga. Kodi tingaonetse motani kuti timawalemekeza anthu amene timagwira nao nchito? Muzigwira nchito mwakhama ndipo muziyesetsa kuona zabwino mwa anchito anzanu komanso mwa abwana anu. (Tito 2:9, 10) Ngati ndinu oona mtima komanso akhama pa nchito, n’kutheka kuti mungasangalatse anthuwo. Koma nthawi zina sizingatheke. Mulimonsemo, mudzakondweretsa Mulungu.—Akol. 3:22, 23.
18. N’cifukwa ciani m’pofunika kucitira ena ulemu?
18 Tili ndi zifukwa zambiri zabwino zotipangitsa kuti tizilemekeza ena. Taphunzira kuti tikamalemekeza a m’banja lathu, timakhala kuti tikulemekeza Mutu wa banja lathu Wamkulu, Yehova. Taphunziranso kuti tikamalemekeza abale ndi alongo athu, timalemekeza Atate wathu wakumwamba. Ndipo tikamalemekeza anthu amene si Mboni, timapangitsa kuti cikhale cotheka kwa io kuti tsiku lina akalemekeze Mulungu wathu wamkulu. Ngakhale kuti anthu ena sangatipatse ulemu, ife tiyenera kupitiriza kuwalemekeza. N’cifukwa ciani? Cifukwa n’cakuti Yehova adzatidalitsa tikatero. Iye analonjeza kuti: “Amene akundilemekeza ndidzawalemekeza.”—1 Sam. 2:30.
NYIMBO 129 Tidzapilila Mosalekeza
a Maina ena asinthidwa.
b MAU OFOTOKOZERA ZITHUNZI Pacikuto: Ngakhale kuti atate ake anamunyanzitsa Yonatani, iye sanaleke kucirikiza ufumu wao.
c MAU OFOTOKOZERA CITHUNZI: Kumanzere, mwamuna akutamanda mkazi wake cifukwa ca nchito yabwino imene akucita. Kulamanja, mkazi akum’kambira zabwino mwamuna wake kwa ena.