NKHANI 4
N’cifukwa Ciani Tiyenela Kulemekeza Ulamulilo?
“Lemekezani anthu, kaya akhale amtundu wotani.”—1 PETULO 2:17.
1, 2. (a) Ndi vuto lotani limene timakhala nalo pankhani yolemekeza ulamulilo? (b) Kodi tidzakambilana mafunso ati?
KODI mumaona mmene mwana wamng’ono amacitila ngati kholo lake lam’pempha kucita cinthu cimene safuna? Nkhope yake imaonekelatu kuti iye akulimbana ndi mitima iŵili. Iye angamve zimene kholo lake lingamuuze, ndipo amadziŵa kuti ayenela kumvela. Koma panthawiyi safuna cabe kumvela kholo lake. Zimenezi zimaonetsa nkhondo imene imacitika mumtima mwa aliyense wa ife.
2 Mwacibadwa, anthufe nthawi zambili timavutika kulemekeza ulamulilo. Kodi nthawi zina zimakuvutani kulemekeza anthu amene amakulamulilani? Ngati ndi conco, dziŵani kuti simuli nokha. Tikukhala m’nthawi imene anthu ocepa cabe ndi amene amafuna kulemekeza ulamulilo. Koma Baibulo limati tiyenela kulemekeza anthu amene amatilamulila. (Miyambo 24:21) Ndipo kucita zimenezo n’kofunika kuti tipitilize kukhala m’cikondi ca Mulungu. Conco, tingafunse kuti: Nanga n’cifukwa ciani nthawi zina zimakhala zovuta kulemekeza ulamulilo? N’cifukwa ciani Yehova amafuna kuti tizilemekeza ulamulilo? Ndipo n’ciani cingatithandize kucita zimenezi? Komanso, tingaonetse bwanji kuti timalemekeza ulamulilo?
CIFUKWA CAKE KULEMEKEZA ULAMULILO KUMAKHALA KOVUTA
3, 4. Kodi ucimo ndi kupanda ungwilo zinayamba bwanji? Nanga kupanda ungwilo kwathu kumatilepheletsa bwanji nthawi zina kulemekeza ulamulilo?
3 Mwacidule tiyeni tikambilane zifukwa ziŵili zimene zimapangitsa kuti tizivutika kulemekeza anthu amene amatilamulila. Coyamba n’cakuti ndife opanda ungwilo. Caciŵili n’cakuti anthu amene amatilamulila naonso ndi opanda ungwilo. Ucimo ndi kupanda ungwilo kwa anthu zinayambila m’munda wa Edeni kale kwambili pamene Adamu ndi Hava anapandukila ulamulilo wa Mulungu. Cotelo, kupanduka ndiko kunabweletsa ucimo. Kucokela pamenepo, tili ndi cibadwa cofuna kupandukila ulamulilo.—Genesis 2:15-17; 3:1-7; Salimo 51:5; Aroma 5:12.
4 Cifukwa copanda ungwilo, n’zosavuta kukhala munthu wonyada ndi wodzikweza. Koma kudzicepetsa ndi khalidwe losoŵa limene timafunika kulimbikila kuti tikhale nalo. Ngakhale tatumikila Mulungu mokhulupilika kwa zaka zambili, n’zotheka kutengela mzimu waliuma ndi wonyada. Mwacitsanzo, ganizilani Kora amene anapilila mavuto pamodzi ndi anthu a Yehova kwa zaka zambili. Koma iye anayamba kulakalaka udindo wapamwamba, cakuti mwamwano anatsogolela anthu kupandukila Mose, munthu wofatsa kuposa anthu onse panthawiyo. (Numeri 12:3; 16:1-3) Ganizilaninso za Mfumu Uziya. Kunyada kunam’cititsa kuloŵa m’kacisi wa Yehova ndi kukacita utumiki wopatulika wofunika kucitidwa ndi ansembe okha basi. (2 Mbiri 26:16-21) Anthu amenewa analangidwa koopsa cifukwa ca kupanduka. Ndipo zitsanzo zao zoipazo ndi cenjezo kwa ife. Tiyenela kugwebana ndi mzimu wonyada umene ungatilepheletse kulemekeza ulamulilo.
5. Kodi anthu opanda ungwilo amagwilitsila nchito bwanji ulamulilo wao molakwika?
5 Kumbali ina, cifukwa copanda ungwilo anthu amene ali paudindo naonso, amacita zinthu zimene zimapangitsa ena kusalemekeza ulamulilo. Ambili ndi ankhanza ndi opondeleza anzao. Ndipo kuyambila kale, anthu akhala akugwilitsila nchito mphamvu zao molakwika. (Ŵelengani Mlaliki 8:9.) Mwacitsanzo, Sauli anali munthu wabwino ndi wodzicepetsa pamene Yehova anam’sankha kukhala mfumu. Komabe, iye anadzakhala wonyada ndi wansanje, cakuti pambuyo pake anazunza munthu wokhulupilika Davide. (1 Samueli 9:20, 21; 10:20-22; 18:7-11) Davide anadzakhala mfumu yabwino kwambili mu Isiraeli. Koma nayenso anagwilitsila nchito mphamvu zake molakwika pamene anatenga mkazi wa Uriya Mhiti ndi kutumiza mwamuna wosalakwayo kutsogolo kwenikweni kwa gulu lankhondo kuti akaphedwe. (2 Samueli 11:1-17) Zoonadi, kupanda ungwilo kumalepheletsa anthu kugwilitsila nchito bwino mphamvu zao. Ndipo anthu amene ali paudindo amakhala oipa kwambili ngati salemekeza Yehova. Pambuyo pofotokoza mmene apapa ena acikatolika anayambila kuzunza anthu kwambili, wandale wina wochuka ku Britain, anati: “Nthawi zambili munthu akakhala ndi ulamulilo, khalidwe lake limaipa, ndipo ulamulilo ukakula, khalidwe lake limaipanso kwambili.” Poganizila zimenezi, tiyeni tipende funso lakuti: N’cifukwa ciani tiyenela kulemekeza ulamulilo?
N’CIFUKWA CIANI TIYENELA KULEMEKEZA ULAMULILO?
6, 7. (a) Kodi kukonda Yehova kumatilimbikitsa kucita ciani? Ndipo n’cifukwa ciani? (b) Kodi kugonjela kumaphatikizapo kucita ciani?
6 Cifukwa cacikulu cimene timalemekezela ulamulilo n’cakuti tili ndi cikondi. Timakonda Yehova, anthu anzathu, ndi moyo wathu. Cifukwa timakonda Yehova kuposa cina ciliconse, timafuna kukondweletsa mtima wake. (Ŵelengani Miyambo 27:11; Maliko 12:29, 30.) Timadziŵa kuti kuyambila pa cipanduko ca mu Edeni, ucifumu wake, kapena kuti ufulu wake wolamulila cilengedwe conse, wakhala ukutsutsidwa padziko lapansi. Timadziŵanso kuti anthu ambili asankha kukhala kumbali ya Satana ndi kukana ulamulilo wa Yehova. Ife timacilikiza ulamulilo wa Yehova mosangalala. Mau a pa Chivumbulutso 4:11, amatikhudza mtima kwambili. Ife sitikaikila ngakhale pang’ono kuti Yehova ndiye Wolamulila woyenela wa cilengedwe conse. Timavomeleza ucifumu wa Yehova, ndi kulemekeza ulamulilo wake pa umoyo wathu wa tsiku ndi tsiku.
7 Ulemu umenewu umatanthauza zambili osati kukhala womvela cabe. Timamvela Yehova mwaufulu cifukwa timam’konda. Komabe, nthawi zina kukhala omvela kumativuta kwambili. Panthawi zimenezi, mofanana ndi mwana uja amene tachula kuciyambi kwa nkhani ino, tifunika kuphunzila kugonjela. Tikumbukile kuti Yesu anagonjela cifunilo ca Atate wake, ngakhale kuti kunaoneka kukhala kovuta kwambili. Iye anauza Atate wake kuti: “Cifunilo canu cicitike, osati canga.”—Luka 22:42.
8. (a) Kodi kugonjela ulamulilo wa Yehova masiku ano kumaphatikizapo kucita ciani? Ndipo Yehova amaiona bwanji nkhani ya kugonjela? (b) N’ciani cingatithandize kulandila uphungu ndi cilango? (Onani kabosi kakuti “Mvela Uphungu Ndipo Utsatile Malangizo.”)
8 Masiku ano, Yehova sakamba ndi aliyense wa ife mwacindunji. Iye amagwilitsila nchito Mau ake ndi anthu amene amamuimila padziko lapansi. Mwakutelo, timaonetsa kuti tikugonjela ulamulilo wa Yehova ngati tilemekeza anthu amene wawaika paudindo, kapena amene wawalola kuti azitilamulila. Ngati tiwapandukila, monga kukana uphungu wao wa m’Malemba, tingakwiitse Mulungu wathu. Pamene Aisiraeli anang’ung’udza ndi kupandukila Mose, Yehova anaona kuti io anapandukila iye.—Numeri 14:26, 27.
9. Kodi kukonda anzathu kungatithandize bwanji kulemekeza ulamulilo? Pelekani zitsanzo.
9 Timalemekezanso ulamulilo cifukwa timakonda anzathu. N’cifukwa ciani tikutelo? Yelekezani kuti ndinu msilikali kunkhondo. Kuti gulu lanu lipulumuke ndi kupambana, zimadalila kuti msilikali aliyense akhale wogwilizanika, womvela ndi waulemu kwa akuluakulu a asilikali. Ngati inu mungapanduke ndi kuleka kumvela atsogoleli anu pankhondo, asilikali anzanu onse angakhale pangozi yaikulu. Masiku ano, asilikali aumunthu amaononga kwambili zinthu ndi miyoyo ya anthu. Koma asilikali a Yehova amacita zabwino zokhazokha. Baibulo limacha Mulungu kuti ndi “Yehova wa makamu” nthawi mahandiledi ambili. (1 Samueli 1:3) Iye ndi Mtsogoleli wa makamu ambili a zolengedwa zauzimu zamphamvu. Nthawi zina, Yehova amayelekezela atumiki ake a padziko lapansi ndi khamu la asilikali. (Salimo 68:11; Ezekieli 37:1-10) Ngati tingapandukile anthu amene Yehova waika kuti atitsogolele, kodi sindiye kuti tikuika asilikali anzathu a kuuzimu pangozi? Ngati Mkristu wapandukila akulu, enanso mumpingo amavutika. (1 Akorinto 12:14, 25, 26) Mwana akapanduka, banja lonse limavutika. Conco, timaonetsa kuti timakonda anzathu ngati tilemekeza ndi kumvela amene amatilamulila.
10, 11. Kodi kufuna kuti zinthu zitiyendele bwino kumatilimbikitsa bwanji kumvela ulamulilo?
10 Timalemekezanso ulamulilo cifukwa cakuti timapindula. Yehova akatiuza kuti tizilemekeza ulamulilo, amachulanso mapindu amene timapeza tikacita zimenezo. Mwacitsanzo, amauza ana kuti akamvela makolo ao adzakhala ndi moyo wautali ndi wabwino. (Deuteronomo 5:16; Aefeso 6:2, 3) Amatiuza kuti tizilemekeza akulu mumpingo, cifukwa kulephela kuwamvela kumaononga ubwenzi wathu ndi Yehova Mulungu. (Aheberi 13:7, 17) Ndipo amatiuzanso kuti tizilemekeza olamulila a dziko kuti tikhale otetezeka.—Aroma 13:4.
11 Kodi simukuvomeleza kuti kudziŵa cifukwa cimene Yehova amafunila kuti tizimvela kumatithandiza kulemekeza ulamulilo? Tsopano tiyeni tikambilane mbali zitatu zofunika kwambili za mmene tingalemekezele ulamulilo.
KUONETSA ULEMU M’BANJA
12. Kodi Yehova anapatsa mwamuna kapena tate udindo wotani m’banja? Ndipo iye ayenela kuukwanilitsa bwanji udindo wakewo?
12 Yehova ndi amene anayambitsa banja. Pokhala Mulungu wa dongosolo, iye anakhazikitsa dongosolo kuti banja liziyenda bwino. (1 Akorinto 14:33) Iye anapatsa ulamulilo kwa mwamuna kapena tate kukhala mutu wa banja. Mwamuna nayenso ayenela kulemekeza Mutu wake, Kristu Yesu, mwa kutengela citsanzo ca mmene iye amacitila umutu wake mumpingo. (Aefeso 5:23) Conco, mwamuna sayenela kunyalanyaza udindo wake, ayenela kuukwanilitsa mwakhama. Ndipo sayenela kukhala wopondeleza kapena wankhanza. M’malo mwake, ayenela kukhala wacikondi, wololela, ndi wokoma mtima. Afunika kukumbukila kuti ulamulilo wake uli ndi malile, ndipo suposa ulamulilo wa Yehova.
Tate wacikristu amatengela citsanzo ca mmene Kristu amacitila umutu wake
13. N’ciani cimene mkazi kapena mai angacite kuti akwanilitse udindo wake m’njila imene ingakondweletse Yehova?
13 Mkazi kapena mai ayenela kukhala mthandizi kapena mnzake woyenelela kwa mwamuna wake. Nayenso mkazi anapatsidwa ulamulilo m’banja, popeza Baibulo limakamba za ‘lamulo la amai ako.’ (Miyambo 1:8) Koma ulamulilo wake suposa ulamulilo wa mwamuna wake. Mkazi wacikristu amalemekeza ulamulilo wa mwamuna wake mwa kum’thandiza kukwanilitsa udindo wake monga mutu wa banja. Iye sayenela kudelela mwamuna wake, kum’lamulila, kapena kum’landa udindo wake. Ayenela kum’cilikiza ndi kugwilizana naye. Ngati sagwilizana ndi zosankha za mwamuna wake, angakambe maganizo ake mwaulemu, koma akhalebe wogonjela. N’zoona kuti ngati mwamuna wake si Mboni zingakhale zovutilapo. Koma khalidwe la mkazi logonjela lingathandize mwamuna wake kuyamba kukonda Yehova.—Ŵelengani 1 Petulo 3:1.
14. Kodi ana angakondweletse bwanji makolo ao ndi Yehova?
14 Ngati ana amvela atate ndi amai ao amakondweletsa mtima wa Yehova. Amabweletsanso ulemu ndi cimwemwe kwa makolo ao. (Miyambo 10:1) M’mabanja a kholo limodzi, ana ayenelanso kukhala omvela, ndi kukumbukila kuti kholo lao limafunikila kwambili kulithandiza ndi kugwilizana nalo. M’mabanja amene aliyense amacita bwino mbali yake imene Mulungu anam’patsa, mumakhala mtendele ndi cimwemwe cacikulu. Zimenezi zimalemekeza Yehova Mulungu, amene anayambitsa mabanja onse.—Aefeso 3:14, 15.
KUONETSA ULEMU MUMPINGO
15. (a) Kodi tingaonetse bwanji kuti timalemekeza ulamulilo wa Yehova mumpingo? (b) Ndi mfundo ziti zingatithandize kumvela amene akutitsogolela? (Onani kabosi kakuti “Muzimvela Amene Akutsogolela Pakati Panu.”)
15 Yehova anasankha mwana wake kukhala Wolamulila mpingo wacikristu. (Akolose 1:13) Nayenso Yesu, wapatsa “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu” udindo wosamalila anthu a Mulungu mwa kuuzimu. (Mateyu 24:45-47) Bungwe Lolamulila la Mboni za Yehova limatumikila monga “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu.” Monga mmene zinalili m’mipingo ya m’nthawi ya atumwi, akulu masiku ano amalandila malangizo ndi uphungu kucokela ku Bungwe Lolamulila mwacindunji, kapena kupitila mwa oimila ake monga oyang’anila oyendela. Ngati tonse timvela akulu mumpingo ndiye kuti tikumvela Yehova.—Ŵelengani 1 Atesalonika 5:12; Aheberi 13:17.
16. Kodi akulu amaikidwa ndi mzimu woyela m’njila yotani?
16 Akulu ndi atumiki othandiza ndi anthu opanda ungwilo. Naonso ali ndi zofooka monga ife. Ngakhale ndi conco, io ndi “mphatso za amuna” ndipo anaikidwa kuti athandize mpingo kukhala wolimba mwa kuuzimu. (Aefeso 4:8) Akulu amaikidwa ndi mzimu woyela. (Machitidwe 20:28) Motani? M’njila yakuti io ayenela kukwanilitsa ziyeneletso za m’Mau a Mulungu ouzilidwa ndi mzimu. (1 Timoteyo 3:1-7, 12; Tito 1:5-9) Ndiponso, akulu amene amapenda ziyeneletso za abalewo, amapemphela mocokela pansi pa mtima kuti mzimu woyela wa Yehova uwatsogolele.
17. Ndi pa zocitika ziti mumpingo pamene alongo ayenela kuvala cophimba kumutu?
17 Nthawi zina mumpingo mungakhale mulibe akulu ndi atumiki othandiza kuti asamalile maudindo monga kutsogoza pa kukumana kwa ulaliki. Zikakhala conco, abale ena obatizidwa angasamalile mbali zimenezo. Ngati palibe abale obatizidwa, alongo oyenelela angacite mbalizo. Koma pamene mlongo asamalila mbali yoyenela mwamuna wobatizidwa, ayenela kuvala cophimba kumutu.a (1 Akorinto 11:3-10) Zimenezi sizipangitsa akazi kukhala otsika. M’malo mwake, zimawapatsa mwai woonetsa kuti amalemekeza makonzedwe a Yehova a umutu, ponse paŵili m’banja ndi mumpingo.
KULEMEKEZA OLAMULILA A DZIKO
18. Kodi mungafotokoze bwanji mfundo ya pa Aroma 13:1-7?
18 Akristu oona amatsatila mokhulupilika mfundo yopezeka pa Aroma 13:1-7. (Ŵelengani.) Mukaŵelenga mavesi amenewa, mudzaona kuti “olamulila akuluakulu” ochulidwa pamenepo ndi maboma a dziko. Malinga ngati Yehova walola maboma a anthu amenewa kukhalapo, amagwila nchito zofunika monga kusungitsa mtendele ndi nchito zina zofunikila. Timalemekeza olamulila amenewa mwa kumvela malamulo. Timaonetsetsa kuti talipila msonkho uliwonse, kulemba mwacilungamo mafomu kapena zikalata zonse zimene boma lingafune, ndi kutsatila malamulo onse okhudza ifeyo, banja lathu, bizinesi yathu, kapena katundu wathu. Koma ngati olamulila a boma afuna kuti tiphwanye malamulo a Mulungu, timakana. M’malo mwake, timayankha mmene anayankhila atumwi kuti: “Tiyenela kumvela Mulungu monga wolamulila, osati anthu.”—Machitidwe 5:28, 29; onani kabokosi kakuti: “Kodi Ndiyenela Kumvela Ulamulilo wa Ndani?”
19. Kodi tingaonetse bwanji kuti timalemekeza olamulila a boma?
19 Timaonetsanso kuti timamvela olamulila a boma mwa khalidwe lathu kwa anthu ena. Nthawi zina tingafunike kucita zinthu ndi akuluakulu a boma mwacindunji. Mtumwi Paulo anacita zinthu mwacindunji ndi olamulila monga Mfumu Herodi Agiripa ndi Bwanamkubwa Fesito. Ngakhale kuti amuna amenewa anali ndi makhalidwe oipa kwambili, Paulo analankhula nao mwaulemu. (Machitidwe 26:2, 25) Ifenso tiyenela kutengela citsanzo ca Paulo, kaya tilankhula ndi wolamulila wamphamvu kapena wapolisi. Kusukulu, Akristu acicepele ayenela kulemekeza aphunzitsi ndi anthu ena ogwila nchito pasukulu imeneyo. Sitiyenela kulemekeza cabe anthu amene amavomeleza zimene timakhulupilila, koma ngakhale aja amene amatitsutsa. Ndithudi, anthu amene si Mboni ayenela kuona kuti ndife anthu aulemu.—Ŵelengani Aroma 12:17, 18; 1 Petulo 3:15.
20, 21. Ndi mapindu ena ati amene amabwela cifukwa colemekeza ulamulilo?
20 Conco, tisacite kaso kupeleka ulemu. Mtumwi Petulo analemba kuti: ‘Lemekezani anthu onse, kaya akhale amtundu wotani.’ (1 Petulo 2:17) Anthu akaona kuti timawalemekeza, angakondwele nafe kwambili. Kumbukilani kuti masiku ano anthu aulemu akucepelacepela. Conco, kupeleka ulemu ndi njila imodzi yosonyeza kuti timamvela lamulo la Yesu lakuti: “Onetsani kuwala kwanu pamaso pa anthu, kuti aone nchito zanu zabwino ndi kuti alemekeze Atate wanu wakumwamba.”—Mateyu 5:16.
21 M’dziko la mdimali, anthu a mitima yabwino amakopeka ndi kuwala kwa kuuzimu. Motelo, ngati tionetsa ulemu m’banja, mumpingo, kapena kwina kulikonse, anthu ena angakopeke ndi kuyamba kuyenda nafe panjila ya kuwala. Zikatelo, zimakhala zosangalatsa kwambili! Koma ngakhale zimenezi zisacitike, timadziŵa kuti kulemekeza ena kumakondweletsa Yehova Mulungu, ndipo kumatithandiza kukhalabe m’cikondi cake. Kodi pangakhale madalitso oposa amenewa?
a Zakumapeto kamutu kakuti “Ndi Liti Pamene Mlongo Ayenela Kuvala Cophimba Kumutu, Ndipo N’cifukwa Ciani?, pali njila zingapo za mmene tingagwilitsile nchito mfundo imeneyi.