PHUNZILO 11
Kukamba Mwaumoyo
Aroma 12:11
ZOFUNIKILA: Muzikamba mwaumoyo kuti omvela anu akhale ogalamuka komanso olimbikitsidwa.
MOCITILA:
Kambani mocokela pa mtima. Pokonzekela nkhani kapena ulaliki wanu, ganizilani za kufunika kwa uthenga wanu. Idziŵeni bwino nkhani yanu cakuti mukaikambe mocokela pa mtima.
Ganizilani omvela anu. Ganizilani za mmene mfundo zimene mudzaŵelenga kapena kuphunzitsa zingapindulitsile ena. Onani njila imene mungazifotokozele mowafika pa mtima omvela anu.
Ikani umoyo m’nkhani yanu. Kambani mwaumoyo, osati mopola. Pangani magesca acibadwa, komanso nkhope izionetsa mmene mukumvelela.