PHUNZILO 18
Nkhani Yophunzitsadi Kanthu Omvela
1 Akorinto 9:19-23
ZOFUNIKILA: Kambani mwa njila yopangitsa omvela anu kuganizilapo pa nkhaniyo, na kuona kuti aphunzilapodi kanthu.
MOCITILA:
Ganizilani zimene omvela anu amazidziŵa kale. M’malo mongobweleza zimene iwo anamvelapo kale, athandizeni kuona nkhaniyo mwatsopano.
Fufuzani na kusinkha-sinkha. Ngati n’kotheka, phatikizanipo mfundo zomvekako zacilendo, kapena zocitika za pa nyuzi monga zitsanzo pofuna kumveketsa mfundo zazikulu. Ganizilani mozama mmene zitsanzo zimenezo zikugwilizanila na nkhani yanu.
Onetsani phindu ya nkhani yanu. Unikani mmene mfundo za m’Malemba zingathandizile omvela anu mu umoyo wawo wa tsiku na tsiku. Fotokozani mikhalidwe yakuti-yakuti, kapena maganizo, kapenanso zocitika zoyenelela kwa omvela anu.