LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • th phunzilo 13 tsa. 16
  • Kumveketsa Phindu ya Nkhani

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kumveketsa Phindu ya Nkhani
  • Citani Khama pa Kuŵelenga na Kuphunzitsa
  • Nkhani Zofanana
  • Mawu Oyamba Ogwila Mtima
    Citani Khama pa Kuŵelenga na Kuphunzitsa
  • Yesetsani Kuwafika pa Mtima Omvela
    Citani Khama pa Kuŵelenga na Kuphunzitsa
  • Kukamba Mwaumoyo
    Citani Khama pa Kuŵelenga na Kuphunzitsa
  • Nkhani Yophunzitsadi Kanthu Omvela
    Citani Khama pa Kuŵelenga na Kuphunzitsa
Onaninso Zina
Citani Khama pa Kuŵelenga na Kuphunzitsa
th phunzilo 13 tsa. 16

PHUNZILO 13

Kumveketsa Phindu ya Nkhani

Lemba losagwila mawu

Miyambo 3:21

ZOFUNIKILA: Thandizani omvela anu kumvetsa mmene nkhani yanu ikukhudzila umoyo wawo. Komanso afotokozeleni mocitila nazo zimene aphunzila.

MOCITILA:

  • Ganizilani omvela anu. Ganizilani cifukwa cake kuli kofunikila kuti anthuwo amvele nkhani yanu, ndipo onani mfundo zimene zingawathandize kweni-kweni.

  • M’nkhani yanu yonse, onetsani omvela anu zimene afunika kucita. Kungoyamba nkhani yanu, womvela aliyense afunika kukamba mu mtima mwake kuti, ‘Nkhani iyi ni yothandizadi kwa ine.’ Pamene mutambasula mfundo iliyonse, onetsani mmene ingawathandizile kweni-kweni. Pewani kumangokamba mwacisawawa.

    Tumalangizo tothandizila

    Mwacikondi komanso mowaganizila omvela anu, fotokozani mmene mfundo za m’Baibo zimathandizila. M’malo mowapangitsa kudzimva olakwa, alimbikitseni kukonda Yehova na kum’khulupilila, muli na cidalilo cakuti mtima wawo udzawalimbikitsa kulabadila mfundo zimene mwawaunikila.

MU ULALIKI

Pokonzekela ulaliki, ganizilani nkhani zili pa nyuzi, komanso nkhani zimene anthu m’gawo lanu angakonde kukambilana nawo. Pokambilana, onani zimene anthu angacite nazo cidwi. Mwaluso, funsani mafunso amene angamasule munthu kuchula nkhawa zake na zinthu zina zomukhudza. Mvetselani mwachelu, ndipo sinthilani ulaliki wanu kwa iye kuti mum’thandize.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani